Mutu 77
Nkhani ya Choloŵa
MWACHIWONEKERE anthu akudziŵa kuti Yesu anali kudya chakudya kunyumba ya Mfarisi. Chotero zikwi zambiri za iwo zikusonkhana panja ndipo zikuyembekezera pamene Yesu akutuluka. Mosiyana ndi Afarisi amene amatsutsa Yesu ndi kuyesayesa kumkola kuti alankhule kanthu kena kolakwika, anthuwo akumumvetsera mwachidwi ndi chiyamikiro.
Potembenukira choyamba kwa ophunzira ake, Yesu akuti: “Tachenjerani nokha ndi chotupitsa mikate cha Afarisi, chimene chiri chinyengo.” Monga mmene kunasonyezedwera panthaŵi ya chakudya, dongosolo lonse la chipembedzo la Afarisi nlodzadzidwa ndi chinyengo. Komabe ngakhale kuti kuipa kwa Afarisi kungabisidwe mwa kusonyeza kudzipereka, pambuyo pake kudzavumbulidwa. “Kulibe kanthu kovundikiridwa,” Yesu akutero, “kamene sikadzaululidwa; ndi kobisika kamene sikadzadziŵika.”
Yesu akupitiriza kubwereza chilimbikitso chimene anapereka kwa 12 pamene iye anawatuma ulendo wokalalikira wa ku Galileya. Iye akuti: “Musawope iwo akupha thupi, ndipo akatha ichi alibe kanthu kena angathe kuchita.” Popeza kuti Mulungu samaiŵala ngakhale mpheta imodzi, Yesu akutsimikizira ophunzira ake kuti Mulungu sadzawaiŵala. Iye akunena kuti: “Pamene pali ponse adzamuka nanu kumlandu wa m’sunagoge ndi kwa akulu, ndi aulamuliro, . . . mzimu woyera adzaphunzitsa inu nthaŵi yomweyo zimene muyenera kuzinena.”
Munthu wina wa m’khamulo akufuula. “Mphunzitsi,” iye akupempha kuti, “uzani mbale wanga agaŵane ndi ine chuma chamasiye.” Chilamulo cha Mose chimanena kuti mwana wamwamuna wachisamba akayenera kulandira magawo aŵiri a choloŵa, chotero sipayenera kukhala mkangano uliwonse. Koma mwachiwonekere munthuyo akufuna gawo lake la choloŵa loposa lololedwa ndi lamulo.
Moyenelera Yesu akukana kuphatikizidwa. “Munthu iwe, ndani anandiika ine ndikhale woweruza, kapena wa kugaŵira inu?” iye akufunsa motero. Pamenepo iye akupereka chilangizo ichi chofunika kwambiri kukhamulo: “Yang’anirani, mudzisungire kupeŵa msiliro uliwonse; chifukwa moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo.” Inde, mosasamala kanthu za kuchuluka kwa zinthu zimene munthu angakhale nazo, mwachibadwa iye adzafa ndi kuzisiya. Kuti agogomezere chenicheni chimenechi, ndiponso kusonyeza kupusa kwa kulephera kupanga mbiri yabwino ndi Mulungu, Yesu akugwiritsira ntchito fanizo. Iye akufotokoza kuti:
“Munda wake wa munthu mwini chuma unapatsa bwino. Ndipo anaganizaganiza mwa yekha nanena, Ndidzatani ine, popeza ndiribe mosungiramo zipatso zanga? Ndipo anati, Ndidzatere: ndidzapasula nkhokwe zanga, ndi kumanganso zazikulu, ndipo ndidzasungiramo dzinthu zanga zonse, ndi chuma changa. Ndipo ndidzati kwa moyo wanga, Moyo iwe, uli nacho chuma chambiri chosungika kufikira zaka zambiri; tapumulatu, nudye, numwe, nukondwere. Koma Mulungu anati kwa iye, Wopusa iwe, usiku womwe uno udzafunidwa moyo wako; ndipo zinthu zimene unazikonza zidzakhala za yani?”
Pomaliza, Yesu akuti: “Atero iye wakudziunjikira chuma mwini yekha wosakhala nacho chuma cha kwa Mulungu.” Pamene kuli kwakuti ophunzirawo sangatcheredwe msampha ndi kupusa kwa kuunjika chuma, chifukwa cha zosamalira za tsiku ndi tsiku za moyo iwo mosavuta akakhoza kucheukitsidwa muutumiki wa moyo wonse kwa Yehova. Chotero Yesu akugwiritsira ntchito nyengoyo kubwerezanso uphungu wabwino kwambiri umene iye anali atapereka pafupifupi chaka chimodzi ndi theka zapitazo poyambirira mu Ulaliki wa pa Phiri. Potembenukira kwa ophunzira ake, iye akuti:
“Chifukwa chake ndinena ndinu, Musade nkhaŵa ndi moyo wanu, chimene mudzadya; kapena ndi thupi lanu, chimene mudzavala. . . . Lingilirani makungubwi, kuti samafesayi, kapena kutemayi; alibe nyumba yosungiramo, kapena nkhokwe; ndipo Mulungu awadyetsa. . . . Lingalirani maluŵa, makulidwe awo; sagwira ntchito ndipo sapota; koma ndinena kwa inu, Ngakhale Solomo, mu ulemelero wake wonse sanavala ngati limodzi la awa. . . .
“Ndipo inu musafunefune chimene mudzadya, ndi chimene mudzamwa; ndipo musakayike mtima. Pakuti izi zonse mitundu ya anthu a padziko lapansi amazifunafuna; koma Atate wanu adziŵa kuti musoŵa zimenezi. Komatu tafunafunani Ufumu wake, ndipo izi adzakuwonjezerani.”
Makamaka mkati mwa nthaŵi za mavuto azachuma mawu a Yesu ameneŵa amafunikira kulingaliridwa. Munthu amene amafikira kukhala wodera nkhaŵa mopambanitsa za zosoŵa zake zakuthupi ndi kuyamba kuleka zofunika zauzimu ali, kwenikweni, kusonyeza kusoŵa chikhulupiliro m’kukhoza kwa Mulungu kugaŵira atumiki ake. Luka 12:1-31; Deuteronomo 21:17.
▪ Kodi nchifukwa ninji, mwinamwake, munthuyo akufunsa za choloŵa, ndipo kodi ndichilangizo chotani chimene Yesu akupereka?
▪ Kodi ndifanizo lotani limene Yesu akugwiritsira ntchito, ndipo kodi tanthauzo lake nlotani?
▪ Kodi ndiuphungu wotani umene Yesu akubwereza, ndipo chifukwa ninji uli woyenerera?