Mutu 129
Kuwonekera Kowonjezereka
ATUMWIWO adakali achisoni. Iwo sakuzindikira tanthauzo la manda apululuwo, ndiponso sakukhulupirira malipoti a akaziwo. Chotero pambuyo pake pa Lamlungu, Kleopa ndi wophunzira wina akuchoka ku Yerusalemu kumka ku Emau, mtunda wa pafupifupi makilomitala khumi ndi limodzi.
Ali panjira, pamene akukambitsirana zochitika za tsikulo, mlendo wina akutsagana nawo. “Mawu aŵa ndiotani mulandizanawo poyendayenda?” iye akufunsa motero.
Ophunzirawo akuima, nkhope zawo zitagwa, ndipo Kleopa akuyankha nati: “Kodi iwe wekha ndiwe mlendo m’Yerusalemu ndi wosazindikira zidachitikazi masiku omwe ano?” Mlendoyo akufunsa kuti: “Zinthu zanji?”
“Izi za Yesu Mnazarene,” iwo akuyankha motero. “Ansembe aakulu ndi akulu athu anampereka iye kuchiweruzo cha imfa, nampachika iye [pamtengo wozunzirapo, NW]. Ndipo tinayembekeza ife kuti iye ndiye wakudzayo kudzawombola Israyeli.”
Kleopa ndi bwenzi lakelo akufotokoza zochitika zodabwitsa za tsikulo—lipoti lonena za mawonekedwe achilendo a angelo ndi manda apululu—ndiyeno pamenepo iwo akuvomereza kuzizwa kwawo ponena za tanthauzo la zinthuzi. Mlendoyo akuwadzudzula nati: “Opusa inu, ndi ozengereza mtima kusakhulupirira zonse adazilankhula aneneri! Kodi sanayenera Kristu kumva zoŵaŵa izi, ndi kuloŵa ulemerero wake?” Pamenepo iye akuwamasulira mawu ochokera m’malemba opatulika onena za Kristu.
Pomalizira pake iwo akufika pafupi ndi Emau, ndipo mlendoyo akuchita ngati akufuna kupitirira. Pofuna kumva zochuluka, ophunzirawo akumuumiriza kuti: “Khalani ndi ife; pakuti kuli madzulo.” Chotero iye akukhala nawo pa chakudya. Pamene iye apemphera nanyema mkate ndi kuwapatsa, iwo akuzindikira kuti alidi Yesu m’thupi laumunthu lovalidwa. Komano iye akuzimiririka.
Tsopano iwo akuzindikira chifukwa chake mlendoyo anadziŵa zochuluka! “Mtima wathu sunali wotentha mkati mwathu nanga,” iwo akufunsana, “mmene analankhula nafe m’njira, mmene anatitsegulira malembo?” Mosazengeleza, iwo akunyamuka mofulumira kubwerera ku Yerusalemu, kumene akupeza atumwi ndi amene akusonkhana nawo. Kleopa ndi bwenzi lake asananene chirichonse, enawo mokondwera akusimba kuti: “Ambuye anauka ndithu, nawonekera kwa Simoni.” Pamenepo aŵiriwo akusimba mmene Yesu anawonekeranso kwa iwo. Kumeneku nkuwonekera kwachinayi mkati mwa tsikulo kwa ophunzira ake osiyanasiyana.
Mwadzidzidzi Yesu akuchita kuwonekera kwachisanu. Ngakhale kuli kwakuti zitseko ziri chitsekere chifukwa chakuti ophunzirawo akuwopa Ayuda, iye akuloŵa, naimirira pakati pawo penipenipo, nati: “Mtendere ukhale nanu.” Iwo akuchita mantha, akumayerekezera kuti akuwona mzimu. Chotero, akumafotokoza kuti sali mzukwa, Yesu akuti: “Mukhala bwanji ovutika? ndipo matsutsano amauka bwanji m’mtima mwanu? Penyani manja anga ndi mapazi anga, kuti ine ndine mwini: ndikhudzeni, ndipo penyani; pakuti mzimu ulibe mnofu ndi mafupa, monga muwona ndiri nazo ine.” Komabe, iwo akukayikirabe kukhulupirira.
Kuti awathandize kumvetsetsa kuti ndiyedi Yesu, iye akufunsa kuti: “Muli nako kanthu kakudya kuno?” Atalandira nsomba yokazinga ndi kuidya, iye akuti: “Aŵa ndi mawuwo ndinalankhula nanu, paja ndinakhala ndi inu [imfa yanga isanachitike], kuti ziyenera kukwanitsidwa zonse zolembedwa za ine m’chilamulo cha Mose, ndi aneneri, ndi masalmo.”
Popitiriza chimene, m’chenicheni, chikukhala phunziro Labaibulo pamodzi nawo, Yesu aphunzitsa kuti: “Kotero kwalembedwa, kuti Kristu amve zoŵaŵa, nauke kwa akufa tsiku lachitatu; ndi kuti kulalikidwe m’dzina lake kulapa ndi kukhululukidwa kwa machimo kwa mitundu yonse, kuyambira ku Yerusalemu. Inu ndinu mboni za izi.”
Kaamba ka chifukwa china Tomasi palibepo pakusonkhana kwamadzulo kwa pa Lamlungu kofunikaku. Chotero mkati mwa masiku otsatirawo, enawo mokondwa akumuuza kuti: “Tamuwona Ambuye.”
“Ndikapanda kuwona m’manja ake chizindikiro cha misomaliyo,” Tomasi akutsutsa motero, “ndi kuika chala changa m’chizindikiro cha misomaliyo, ndi kuika dzanja langa ku nthiti yake; sindidzakhulupira.”
Eya, masiku asanu ndi atatu pambuyo pake ophunzirawo asonkhananso m’nyumba. Panthaŵiyi Tomasi ali pamodzi nawo. Ngakhale kuti zitseko ziri zokhomedwa, Yesu kachiŵirinso akuima pakati pawo nati: “Mtendere ukhale ndi inu.” Pamenepo, akumatembenukira kwa Tomasi, akumuitana kuti: “Bwera nacho chala chako kuno, nuwone manja anga; ndipo bwera nalo dzanja lako, nuliike kunthiti yanga, ndipo usakhale wosakhulupira.”
“Ambuye wanga, ndi Mulungu wanga,” Tomasi akudzuma motero.
“Chifukwa wandiwona ine, wakhulupira,” Yesu akufunsa. “Odala iwo akukhulupira, angakhale sanawona.” Luka 24:11, 13-48; Yohane 20:19-29.
▪ Kodi ndimafunso otani amene mlendo wina akufunsa ophunzira aŵiri panjira yomka ku Emau?
▪ Kodi nchiyani chimene mlendoyo akunena chimene chikuchititsa mitima ya ophunzirawo kutentha mkati mwawo?
▪ Kodi ophunzirawo akuzindikira motani za amene mlendoyo ali?
▪ Kleopa ndi bwenzi lake atabwerera ku Yerusalemu, kodi ndilipoti losangalatsa lotani limene iwo akumva?
▪ Kodi ndikuwonekera kwachisanu kotani kumene Yesu akupanga kwa ophunzira ake, ndipo nchiyani chikuchitika mkati mwake?
▪ Kodi nchiyani chikuchitika masiku asanu ndi atatu pambuyo pa kuwonekera kwachisanu kwa Yesu, ndipo kodi ndimotani mmene Tomasi potsirizira pake akhutiritsidwira maganizo kuti Yesu ngwamoyo?