Mutu 130
Kunyanja ya Galileya
TSOPANO atumwiwo akubwerera ku Galileya, monga momwe Yesu anawalangizira kuchita poyambapo. Koma iwo ali osatsimikizira zimene ayenera kukachita kumeneko. Patapita kanthaŵi, Petro akuuza Tomasi, Nataniyeli, Yakobo ndi mbale wake Yohane, ndi atumwi ena aŵiri kuti: “Ndimka kukasodza.”
“Ifenso tipita nawe,” asanu ndi mmodziwo akuyankha motero.
Mkati mwa usiku wonsewo, akulephera kugwira kalikonse. Komabe, pamene kukuyamba kucha, Yesu akuwonekera pagombe, koma atumwiwo sakuzindikira kuti ndiye Yesu. Iye akufuula kuti: “Ananu, muli nako kanthu kakudya kodi?”
“Iyayi!” iwo afuula kwa iye patsidyapo.
“Ponyani khoka kumbali ya dzanja lamanja ya ngalaŵa, ndipo mudzapeza,” iye akutero. Ndipo atatero, iwo ali osakhoza kukoka khokalo chifukwa cha nsomba zonsezo.
“Ndiye Ambuye,” Yohane akufuula motero.
Pakumva zimenezi, Petro akuvala malaya, pakuti anali atavula zovala zake, naloŵa m’nyanja. Pamenepo iye akusambira pafupifupi mamitala makumi asanu ndi anayi kumka kumtunda. Atumwi enawo akutsatira m’ngalaŵa yaing’ono, akumakoka khoka lodzala nsombalo.
Atafika kumtundako, kuli moto wamakala, ndi nsomba pamwamba pake, ndipo kuli mkate. “Tenganiko nsomba zimene mwazigwira tsopano,” Yesu akutero. Petro akwera m’ngalaŵa nakokera khokalo kumtunda. Liri ndinsomba zazikulu 153!
“Idzani mufisule,” Yesu akuwaitana.
Palibe nnena ndi mmodzi yemwe wa iwo akulimba mtima kumfunsa kuti, “Ndinu yani?” chifukwa onsewo akudziŵa kuti ndiye Yesu. Kumeneku ndiko kuwonekera kwachisanu ndi chiŵiri pambuyo pachiukiriro, ndipo kwachitatu kwa atumwiwo monga kagulu. Tsopano iye akupereka chakudya chofisula, akumapatsa aliyense wa iwo mkate ndi nsomba.
Atamaliza kudya, Yesu, mwinamwake akumayang’ana nsomba zambiri zogwidwazo, akufunsa Petro kuti: “Simoni mwana wa Yona, kodi undikonda ine koposa [izi, NW]?” Mosakayikira iye akutanthauza kuti, Kodi ndiwe wodzipereka kwambiri kumalonda a nsomba koposa kuntchito imene ndakukonzekeretsa kuichita?
“Mudziŵa kuti ndikukondani inu,” Petro akuyankha motero.
“Dyetsa ana a nkhosa anga,” akuyankha motero Yesu.
Kachiŵirinso, iye akufunsa kuti: “Simoni mwana wa Yona, ukonda ine kodi?”
“Inde, Ambuye; mudziŵa kuti ndikukondani inu,” Petro akuyankha mwachangu.
“Weta nkhosa zanga,” Yesu akulamulanso kachiŵiri.
Ndiyeno, kachitatunso, iye afunsa kuti: “Simoni mwana wa Yona, kodi undikonda ine?”
Pakali pano Petro akumva chisoni. Iye angakhale akudabwa ngati Yesu akukayikira kukhulupirika kwake. Ndi iko komwe, pamene Yesu posachedwapa anali kuzengedwa mlandu wokhudza moyo wake, Petro kwanthaŵi zitatu anakana kuti samdziŵa. Chotero Petro akuti: “Ambuye, mudziŵa inu zonse; muzindikira kuti ndikukondani inu.”
“Dyetsa nkhosa zanga,” Yesu akulamula kachitatu.
Motero Yesu akugwiritsira ntchito Petro monga chiwiya chokhomerezera mawuwo pa enawo za ntchito imene akufuna kuti iwo achite. Mwamsanga iye adzachoka padziko lapansi, ndipo iye akufuna kuti iwo atsogolere m’kutumikira amene adzaloŵetsedwa m’gulu la nkhosa la Mulungu.
Monga momwedi Yesu anagwidwira ndi kuphedwa chifukwa chakuti anachita ntchito imene Mulungu anamtuma, chotero, iye tsopano akuulula kuti, Petro adzakumana ndi chochitika chofanana. “Pamene unali mnyamata,” Yesu akumuuza motero, “unadzimangira wekha m’chuuno, ndipo unayenda kumene unafuna; koma pamene udzakalamba udzatulutsa manja ako, ndipo adzakumanga wina, nadzakunyamula kumene sufuna.” Mosasamala kanthu za imfa yophedwera chikhulupiriro yoyembekezera Petro, Yesu akumfulumiza kuti: “Nditsate ine.”
Potembenukira kumbuyo, Petro akuwona Yohane nafunsa kuti: “Ambuye, koma nanga uyu?”
“Ngati ndifuna uyu akhale kufikira ndidza ine,” Yesu akuyankha motero, “kuli chiyani ndi iwe? unditsate ine iwe.” Mawu ameneŵa a Yesu anadzazindikiridwa ndi ambiri a ophunzirawo kukhala a kutanthauza kuti mtumwi Yohane sakafa konse. Komabe, monga momwe mtumwi Yohane anafotokozera pambuyo pake, Yesu sananene kuti iye sakafa, koma Yesu anangonena kuti: “Ngati ndifuna iye akhale kufikira ndidza, kuli chiyani ndi iwe?”
Pambuyo pake Yohane nayenso ananena mawu ofunika aŵa: “Koma palinso zina zambiri zimene Yesu anazichita, zoti zikadalembedwa zonse phe, ndilingalira kuti dziko lapansi silikadakhala nawo malo a mabukhu amene akadalembedwa.” Yohane 21:1-25; Mateyu 26:32; 28:7, 10.
▪ Kodi nchiyani chikusonyeza kuti atumwiwo sali otsimikizira za chimene ayenera kuchita ku Galileya?
▪ Kodi atumwiwo akumzindikira motani Yesu ku Nyanja ya Galileya?
▪ Kodi tsopano ndinthaŵi zingati zimene Yesu wawonekera kuyambira pachiukiriro chake?
▪ Kodi Yesu agogomezera motani zimene akufuna kuti atumwi ake achite?
▪ Kodi Yesu akusonyeza motani njira imene Petro adzafera?
▪ Kodi ndindemanga za Yesu zotani zonena za Yohane zimene zinamvedwa molakwa ndi ophunzira ambiriwo?