Mutu 131
Kuwonekera Komaliza, ndi Pentekoste wa 33 C.E.
PANTHAŴI ina Yesu akupanga makonzedwe akuti atumwi ake onse 11 akumane naye paphiri ku Galileya. Mwachiwonekere ophunzira ena auzidwa za msonkhanowo, ndipo okwanira anthu oposa 500 asonkhana. Umenewu ukutsimikizira kukhala msonkhano wosangalatsa chotani nanga pamene Yesu akuwonekera nayamba kuwaphunzitsa!
Pakati pa zinthu zina, Yesu akufotokozera gulu lalikululo kuti Mulungu wampatsa ulamuliro kumwamba ndi padziko lapansi. “Chifukwa chake mukani,” iye akuwafulumiza motero, “phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.”
Tangoganizani! Amuna, akazi, ndi ana onsewo akulandira malangizo ofananawo a kukhala ndi phande m’ntchito yakupanga ophunzira. Otsutsa adzayesa kuimitsa kulalikira kwawo ndi kuphunzitsa, koma Yesu akuwatonthoza kuti: “Ndipo wonani, ine ndiri pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimariziro cha nthaŵi ya pansi pano.” Yesu akukhala ndi otsatira ake mwa njira ya mzimu woyera, kuwathandiza kukwaniritsa uminisitala wawo.
Onse pamodzi, Yesu wadziwonetsa wamoyo kwa ophunzira ake kwanyengo yamasiku 40 pambuyo pa chiukiriro chake. Mkati mwa kuwonekera kumeneku iye akuwaphunzitsa za Ufumu wa Mulungu, ndipo akugogomezera chimene mathayo awo ali monga ophunzira ake. Pachochitika china iye akuwonekera ngakhale kwa mbale wake wa bambo wina Yakobo nakhutiritsa maganizo a amene panthaŵi ina anali wosakhulupirira kuti Iye ndithudi ndiye Kristuyo.
Atumwiwo akali ku Galileya, Yesu mwachiwonekere akuwauza kubwerera ku Yerusalemu. Pokumana nawo kumeneko, iye akuwauza kuti: ‘Musachoke ku Yerusalemu, komatu mulindire lonjezano la Atate, limene munalimva kwa ine; pakuti Yohane anabatiza ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi mzimu woyera, asanapite masiku ambiri.’
Pambuyo pake Yesu akukumananso ndi atumwi ake nawatsogolera kunja kwa mzinda kumka ku Betaniya, amene ali m’chigwa chakummaŵa kwa Phiri la Azitona. Modabwitsa, mosasamala kanthu za zonse zimene wanena za kuchoka kwake mwamsanga kupita kumwamba, iwo akukhulupirirabe kuti Ufumu wake udzakhazikitsidwa padziko lapansi. Chotero iwo akufunsa kuti: “Ambuye, kodi nthaŵi ino mubwezera ufumu kwa Israyeli?”
Mmalo mwa kuyesanso kuwongolera malingaliro awo olakwa, Yesu akungoyankha kuti: “Sikuli kwa inu kudziŵa nthaŵi kapena nyengo, zimene Atate anaziika muulamuliro wake wa iye yekha.” Pamenepo, kachiŵirinso akumagogomezera ntchito imene iwo ayenera kuchita, iye akuti: “Komatu mudzalandira mphamvu, mzimu woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga m’Yerusalemu, ndi m’Yudeya lonse, ndi m’Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.”
Iwo ali chipenyere, Yesu akuyamba kunyamuka kukwera kumka kumwamba, ndiyeno mtambo ukumphimba kuti iwo asamuwone. Atavula thupi lake lanyama, iye akukwera kumwamba monga munthu wauzimu. Pamene 11 amenewo akupitiriza kuyang’anitsitsa dwii kuthambo, amuna aŵiri ovala zoyera akuwonekera pambali pawo. Angelo ovala matupi ameneŵa akufunsa kuti: “Amuna a ku Galileya, muimiranji ndi kuyang’ana kumwamba? Yesu amene walandiridwa kumka kumwamba kuchokera kwa inu, adzadza momwemo monga munamuwona alinkupita kumwamba.”
Njira imene Yesu wachokera nayo padziko lapansi iri yopanda dzoma lapoyera la kutsazikana ndipo yokhala ndi otsatira ake okha okhulupirika openyerera. Chotero iye adzabwera m’njira yofananayo—popanda dzoma lapoyera la kumchingamira ndipo otsatira ake okha okhulupirika akumazindikira kuti iye wabweranso ndipo wayamba kukhalapo kwake m’mphamvu ya Ufumu.
Atumwiwo tsopano akutsika pa Phiri la Azitona, nadutsa Chigwa cha Kidroni, ndi kuloŵanso m’Yerusalemu. Iwo akukhala mmenemo momvera lamulo la Yesu. Masiku khumi pambuyo pake, pa Phwando la Ayuda la Pentekoste wa 33 C.E., pamene pafupifupi 120 a ophunzira asonkhana m’chipinda chosanja m’Yerusalemu, mwadzidzi phokoso lofanana ndi la mphepo yolimba yomawomba likudzadza nyumba yonseyo. Malirime onga amoto akuwonekera, ndipo lirilonse likukhala pa munthu aliyense wa opezekapowo, ndipo ophunzira onsewo akuyamba kulankhula m’zinenero zosiyanasiyana. Kumeneku ndikutsanuliridwa kwa mzimu woyera umene Yesu adalonjeza! Mateyu 28:16-20; Luka 24:49-52; 1 Akorinto 15:5-7; Machitidwe 1:3-15; 2:1-4.
▪ Kodi nkwayani kumene Yesu akuperekako malangizo otsazikira paphiri ku Galileya, ndipo kodi malangizo ameneŵa ngotani?
▪ Kodi Yesu akupereka chitonthozo chotani kwa ophunzira ake, ndipo kodi ndimotani mmene iye adzakhalira nawo?
▪ Kodi Yesu akuwonekera kwautali wotani kwa ophunzira ake pambuyo pa chiukiriro chake, ndipo kodi akuwaphunzitsanji?
▪ Kodi nkwamunthu uti amene mwachiwonekere sanali wophunzira imfa ya Yesu isanachitike kwa amene Yesu akuwonekera?
▪ Kodi ndikusonkhana komalizira kuŵiri kuti kumene Yesu akuchita ndi ophunzira ake, ndipo kodi chikuchitika nchiyani pamisonkhano imeneyi?
▪ Kodi ndimotani mmene Yesu adzabwerera m’njira imodzimodziyo monga momwe akupitira?
▪ Kodi nchiyani chikuchitika pa Pentekoste wa 33 C.E.?