Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 4/1 tsamba 14-15
  • Kuwonekera kwa Yesu Kowonjezereka

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuwonekera kwa Yesu Kowonjezereka
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Nkhani Yofanana
  • Kuwonekera Kowonjezereka
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Yesu Ataukitsidwa Anaonekera kwa Anthu Ambiri
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Akulowa m’Chipinda Chotseka
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Yesu Anaukitsidwa
    Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani?
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 4/1 tsamba 14-15

Moyo ndi Uminisitala za Yesu

Kuwonekera kwa Yesu Kowonjezereka

OPHUNZIRA adakali akuda nkhaŵa. Iwo sakumvetsetsa tanthauzo la manda opanda kanthu, ndipo sakukhulupiriranso malipoti a akaziwo. Chotero pambuyo pake pa Sande, Kleopa ndi wophunzira wina achoka ku Yerusalemu kunka ku Emau, mtunda wa makilomita pafupifupi khumi ndi limodzi.

Ali m’njira, pamene akukambitsirana zochitika za tsikulo, mlendo atsangana nawo. ‘Mawu aŵa ndi otani mulandizanawo poyendayenda?’ iye akufunsa.

Ophunzirawo aima, nkhope zawo nzachisoni, ndipo Kleopa ayankha nati: ‘Kodi iwe wekha ndiwe mlendo m’Yerusalemu ndi wosazindikira zidachitikazi masiku omwe ano?’

“Zinthu zanji?” iye akufunsa.

“Izi za Yesu Mnazarene,” iwo ayankha motero. ‘Ansembe akulu ndi akulu athu anampereka iye ku chiweruziro cha imfa, nampachika iye [pamtengo]. Ndipo tinayembekeza ife kuti iye ndiye wakudzayo kudzaombola Israyeli.’

Kleopa ndi mnzake afotokoza zochitika zozizwitsa za tsikulo​—lipoti lonena za mawonekedwe osakhala achibadwa a angelo ndi manda opanda kanthu​—komano aulula kuzizwa kwawo ponena za tanthauzo la zinthu izi. Mlendoyo akuwadzudzula nati: ‘Opusa inu, ndi ozengereza mtima kusakhulupirira zonse adazilankhula aneneri! Kodi sanayenera Kristu kumva zoŵaŵa izi, ndi kuloŵa ulemerero wake?’ Kenaka iye aŵatanthauzira mbali zochokera m’malemba opatulika oloza kwa Kristu.

Potsirizira pake iwo afika pafupi ndi Emau, ndipo mlendoyo achita ngati kuti akupitiriza ulendowo. Pofuna kumva zambiri, ophunzirawo amuumiriza nati: ‘Khalani ndi ife; pakuti kuli madzulo, ndipo dzuŵa lapendekatu.’ Chotero iye akukhala kaamba ka chakudya. Pamene iye ayamika nanyema mkate ndi kuwapatsa, iwo azindikira kuti iye alidi Yesu m’thupi laumunthu losandulika. Komano iye azimiririka.

Tsopano iwo azindikira mmene mlendoyo anadziŵira zambiri motero! “Mtima wathu sunali wotentha m’kati mwathu nanga,” iwo afunsana, “m’mene analankhula nafe m’njira, m’mene anatitsegulira malembo?” Mosataya nthaŵi, iwo anyamuka ndi kufulumira kubwerera ku Yerusalemu, kumene apeza atumwi ndi omwe asonkhana nawo. Kleopa ndi mnzake asanalankhule kalikonse, enawo mokondwera akusimba kuti: ‘Ambuye anauka ndithu, nawonekera kwa Simoni!’ Ndiyeno aŵiriwo afotokoza mmene Yesu anawonekeranso kwa iwo. Iyi ikukhala nthaŵi yachinayi imene wawonekera kwa ophunzira ake osiyanasiyana patsikulo.

Chinkana kuti zitseko nzokhomedwa chifukwa chakuti ophunzirawo akuwopa Ayuda, Yesu mwadzidzidzi akuwonekera kachisanu. Iye aimirira pakati pawo penipenipo nanena kuti: “Mtendere ukhale ndi inu.” Iwo achita mantha, akulingalira kuti akuwona mzimu. Chotero, pofotokoza kuti sali mzukwa, Yesu akuti: ‘Mukhala bwanji ovutika? Ndipo matsutsano amauka bwanji m’mtima mwanu? Penyani manja anga ndi mapazi anga, kuti ine ndine mwini: ndikhudzeni, ndipo penyani: pakuti mzimu ulibe mnofu ndi mafupa, monga muwona ndiri nazo ine.’ Chikhalirechobe, iwo azengereza kukhulupirira chifukwa chakuti kukhala kwake wamoyo kukuwonekera kukhala kwabwino koposa kwakuti nkovuta kuwonedwa kukhala kowona.

Kuti aŵathandize kumvetsetsa kuti iye alidi Yesu, akuwafunsa kuti: “Muli nako kanthu kakudya kuno?” Atalandira chidutswa cha nsomba yokazinga ndi kuchidya, iye ayamba kuwaphunzitsa, nati: ‘Aŵa ndi mawuwo ndinalankhula nanu, paja ndinakhala ndi inu [ndisanafe], kuti ziyenera kukwanitsidwa zonse zolembedwa za ine m’chilamulo cha Mose, ndi aneneri, ndi masalmo.’

Akupitiriza zimene zifikira kukhala phunziro Labaibulo ndi iwo, Yesu akuphunzitsa kuti: ‘Kotero kwalembedwa, kuti Kristu amve zoŵaŵa, nauke kwa akufa tsiku lachitatu; ndi kuti kulalikidwe m’dzina lake kulapa ndi kukhululukidwa kwa machimo kwa mitundu yonse, kuyambira ku Yerusalemu. Inu ndinu mboni za izi.’

Kaamba kazifukwa zina Tomasi sakupezekapo pakukumana kwa pa Sande kofunika kwa madzuloku. Chotero mkati mwamasiku otsatirapo, enawo mokondwa amuuza kuti: ‘Tamuwona Ambuye.’

‘Ndikapanda kuwona m’manja ake chizindikiro cha misomaliyo,’ akutsutsa motero Tomasi, ‘ndi kuika chala changa m’chizindikiro cha misomaliyo, ndi kuika dzanja langa ku nthiti yake; sindidzakhulupira.’

Eya, masiku asanu ndi atatu pambuyo pake ophunzirawo akukumananso m’nyumba. Panthaŵiyi Tomasi ali pamodzi nawo. Chinkana kuti zitseko nzokhomedwa, Yesu akuimiriranso pakati pawo nanena kuti: “Mtendere ukhale ndi inu.” Ndiyeno, akumatembenukira kwa Tomasi, amuitana nati: ‘Bwera nacho chala chako kuno, nuwone manja anga; ndipo bwera nalo dzanja lako, nuliike ku nthiti yanga, ndipo usakhale wosakhulupira, koma wokhulupira.’

Tomasi afuula nati: “Ambuye wanga, ndi Mulungu wanga.”

‘Chifukwa wandiwona ine, wakhulupira?’ Yesu akufunsa motero. ‘Odala iwo akukhulupira, angakhale sanawona.’ Luka 24:11, 13-48; Yohane 20:19-29.

◆ Kodi ndi mafunso otani amene mlendoyo akufunsa ophunzira aŵiriwo panjira yonka ku Emau?

◆ Kodi mlendoyo akunenanji chimene chichititsa mitima ya ophunzirawo kutentha mkati mwawo?

◆ Kodi ophunzirawo akuzindikira motani kuti mlendoyo ndi Yesu?

◆ Pamene Kleopa ndi mnzake abwerera ku Yerusalemu, kodi ndi lipoti lochititsa nthumanzi lotani limene akumva?

◆ Kodi ndi kuwonekera kwachisanu kuti kumene Yesu apanga kwa ophunzira ake, ndipo kodi nchiyani chikuchitika pamenepo?

◆ Kodi nchiyani chikuchitika masiku asanu ndi atatu pambuyo pakuwonekera kwa Yesu kwachisanu, ndipo kodi ndimotani mmene Tomasi potsirizira pake akukhutiritsidwira kuti Yesu ngwamoyo?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena