Buku Lonamizidwa
“Chiphunzitso chakuti mayendedwe a dziko lapansi ali paŵiri, kuyenda likumazungulira ngati nguli kwinaku nkumazungulira dzuŵa nchabodza, ndipo chimawombana kotheratu ndi Malemba Opatulika.” Linatero bungwe la Congregation of the Index la Tchalitchi cha Roma Katolika m’lamulo la mu 1616.1 Kodi Baibulo limatsutsanadi ndi zenizeni za sayansi? Kapena kodi angolinamiza chabe?
M’CHISANU cha mu 1609/10, Galileo Galilei analozetsa telesikopo yake yatsopano kumwamba naona miyezi inayi ikuzungulira pulaneti la Jupiter. Zimene anapezazo zinatsutsa kotheratu chikhulupiriro chomwe ambiri anali nacho chakuti zam’mwamba zonse zimazungulira dziko lapansi. Kumbuyoko mu 1543, wopenda zakuthambo wa ku Poland, Nicolaus Copernicus, anali atanena kuti mapulaneti amazungulira dzuŵa. Galileo anatsimikiza kuti zimenezo ndi choonadi cha sayansi.
Komabe, akatswiri azaumulungu achikatolika anaziyesa chipanduko zimenezo. Tchalitchi nthaŵi yaitali chinkakhulupirira kuti dziko lapansi ndilo pakati pa chilengedwe chonse.2 Ankakhulupirira zimenezo chifukwa chomasulira malemba m’lingaliro lenileni osonyeza kuti dziko lapansi linakhazikika “pa maziko ake, silidzagwedezeka ku nthaŵi yonse.” (Salmo 104:5) Galileo atapita ku Roma kumene anamuitana, anakaonekera pamaso pa Bwalo la Inquisition. Atamusautsa nawo mafunso, iyeyo anakakamizika kukana zimene anapeza, ndipo anamuika m’ndende ya panyumba yake moyo wake wonse.
Mu 1992, zaka ngati 350 kuchokera pa imfa ya Galileo, Tchalitchi cha Katolika pomalizira pake chinavomereza kuti iye ankanenadi zoona.3 Koma ngati Galileo ananenadi zoona, kodi ndiye kuti Baibulo linanama?
Kumvetsa Tanthauzo la Mavesi a m’Baibulo
Galileo anali kukhulupirira kuti Baibulo nloona. Pamene maumboni asayansi omwe anali kupeza anatsutsana ndi mmene ambiri anali kumasulira mavesi ena a m’Baibulo, iye anangoti akatswiri azaumulunguwo sanali kumvetsa tanthauzo la mavesiwo. Ndi iko komwe, “zoonadi ziŵiri sizingatsutsane,” analemba motero.4 Iye anatero kuti mawu olondola asayansi samatsutsa mawu ozoloŵereka a m’Baibulo. Koma akatswiri azaumulungu sanamlole iye kuwakopa. Iwo anaumirira kuti mawu a m’Baibulo onena za dziko lapansi ayenera kutengedwa mmene alili. Chifukwa cha zimenezo iwo sanangokana zimene Galileo anapeza komanso sanamvetse tanthauzo lenileni la mawu ngati amenewo a m’Malemba.
Kunena zoona, nzeru iyenera kutisonyeza kuti pamene Baibulo limanena za “ngondya zinayi za dziko,” silimatanthauza kuti olemba Baibulo anaganiza kuti dziko lapansi linalidi lamakona ngati bokosi. (Chivumbulutso 7:1) Baibulo linalembedwa m’chinenero cha anthu wamba, ndipo nthaŵi zambiri limagwiritsira ntchito mawu okuluŵika ochititsa chidwi. Chotero pamene Baibulo linena kuti dziko lapansi lili ndi “ngondya zinayi,” “maziko” achikhalire, ndi ‘mwala wa pangondya,’ silimakhala likufotokoza dziko malinga nkufotokoza kwa sayansi; mwachionekere limalankhula mophiphiritsa, zimene timachita masiku onse polankhula.a—Yesaya 51:13; Yobu 38:6.
M’buku lake lakuti Galileo Galilei, wolemba mbiri ya munthu, L. Geymonat, anati: “Akatswiri azaumulungu ochepa nzeruwo amene anafuna kupondereza sayansi ndi malingaliro awo a m’Baibulo akanakayikitsa Baibulo.”5 Nzimene anachita kumene. Ndipotu, kumasulira Baibulo kwa akatswiri azaumulungu—osati Baibulo ayi—nkumene kunapondereza sayansi kwambiri.
Momwemonso, anthu opembedza oumirira mwambo lerolino amapotoza Baibulo pamene amaumirira kuti dziko lapansi linalengedwa m’masiku asanu ndi limodzi amaola 24. (Genesis 1:3-31) Malingaliro ameneŵo sagwirizana ndi sayansi kapena Baibulo. M’Baibulo, monga polankhula masiku onse, liwulo “tsiku” limasinthasintha tanthauzo lake, likumanena za nthaŵi yosiyanasiyana utali wake. Pa Genesis 2:4, masiku onse akulenga asanu ndi limodzi akutchedwa “tsiku” limodzi, kuphatikiza onse pamodzi. Liwu lachihebri lotembenuzidwa kuti “tsiku” m’Baibulo lingangotanthauza “nthaŵi yaitali.”6 Chotero, palibe chifukwa cha m’Baibulo choumirira kuti masiku akulenga anali amaola 24 lililonse. Mwa kuphunzitsa zinazina, oumirira mwambo amalinamiza Baibulo.—Onaninso 2 Petro 3:8.
M’mbiri yonse, akatswiri azaumulungu apotoza Baibulo nthaŵi zambiri. Talingalirani njira zina zimene zipembedzo za Dziko Lachikristu zalinamizira Baibulo pa zimene limanena.
Lanamizidwa ndi Chipembedzo
Ntchito za aja omwe amati amatsatira Baibulo nthaŵi zambiri zimawononga mbiri ya bukulo limene amati akulilemekeza. Omwe amati ndi Akristu akhetsa mwazi wa wina ndi mnzake m’dzina la Mulungu. Komabe, Baibulo limalamula otsatira Kristu ‘kukondana wina ndi mnzake.’—Yohane 13:34, 35; Mateyu 26:52.
Atsogoleri ena achipembedzo amakambulula nkhosa zawo, kuzilanda ndalama zawo zovuta kupezazo mwa kuzinyengerera—kusiyana kutali ndi malangizo a Malemba akuti: “Munalandira kwaulere, patsani kwaulere.”—Mateyu 10:8; 1 Petro 5:2, 3.
Kunena zoona, Baibulo sitingaliweruze malinga ndi zokamba kapena zochita za aja omwe amangogwira mawu ake kapena omwe amati amalitsatira. Chotero munthu wofuna kudziŵa zinthu amafufuza yekha kuti adziŵe za Baibulo ndiponso chifukwa chake lili buku lapadera.
[Mawu a M’munsi]
a Mwachitsanzo, ngakhale openda zakuthambo amakono okonda kutenga zinthu mmene zilili amalankhula za “kutuluka” ndi “kuloŵa” kwa dzuŵa, nyenyezi, ndi magulu a nyenyezi—ngakhale kuti zimenezi, kwenikweni, zimaoneka ngati zikuyenda chifukwa cha kuzungulira kwa dziko lapansi.
[Chithunzi patsamba 4]
Matelesikopo aŵiri a Galileo
[Chithunzi patsamba 5]
Galileo pamaso pa omfunsa