Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gf phunziro 4 tsamba 6-7
  • Mmene Mungaphunzirire za Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mmene Mungaphunzirire za Mulungu
  • Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu!
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mulungu Ndani?
    Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?
  • Kalata Yochokera kwa Mulungu
    Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Uyo Amene Anapanga Zinthu Zonse
    Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Kalata Yochokera kwa Mulungu Amene Amatikonda
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
Onani Zambiri
Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu!
gf phunziro 4 tsamba 6-7

PHUNZIRO 4

Mmene Mungaphunzirire za Mulungu

Mungaphunzire za Yehova mwa kuŵerenga Baibulo. Kale kwambiri, Mulungu anasankha anthu ena kuti alembe malingaliro ake. Zimene analembazo zimatchedwa Baibulo. Lerolino timaphunzira za Mulungu mwa kuŵerenga Baibulo. Chifukwa Baibulo lili ndi mawu a Yehova, kapena uthenga wake, limatchedwanso Mawu a Mulungu. Tiyenera kukhulupirira zimene Baibulo limanena chifukwa Yehova sanama konse. “Mulungu sakhoza kunama.” (Ahebri 6:18) Mawu a Mulungu ali ndi choonadi.—Yohane 17:17.

Banja likuwerenga Baibulo

Baibulo ndi imodzi mwa mphatso zamtengo wapatali kwambiri zimene Mulungu watipatsa. Lili ngati kalata yochokera kwa bambo wokonda ana ake. Limatiuza za lonjezo la Mulungu lakuti adzasintha dziko lapansi kuti lidzakhale malo okongola kwambiri—paradaiso. Limatiuza zimene anachitira ana ake okhulupirika m’mbuyomu, zimene akuwachitira tsopano, komanso zimene adzawachitira m’tsogolo. Limatithandizanso kuthetsa mavuto athu ndi kupeza chimwemwe.—2 Timoteo 3:16, 17.

Mboni za Yehova ndi mabwenzi a Mulungu; adzakuthandizani kumvetsa zimene Baibulo limaphunzitsa. Tangowauzani kuti mukufuna kuphunzira Baibulo. Salipiritsa ndalama pochita zimenezi. (Mateyu 10:8) Komanso, mutha kufika pamisonkhano yawo yachikristu. Imeneyi imachitikira m’malo olambirira otchedwa Nyumba za Ufumu. Ngati mukhala nawo pamisonkhano yachikristu, mudzadziŵa zambiri mofulumira ponena za Mulungu.

Mungaphunzire za Mulungu mwa kuona zinthu zimene wapanga. Mwachitsanzo, Baibulo limati: “Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.” (Genesis 1:1) Pamene Mulungu analenga “kumwamba,” anapanganso dzuŵa. Kodi zimenezo zimatiuzanji ponena za Mulungu? Zimatiuza kuti Yehova n’ngwamphamvu kwambiri. Kuti ndi yekhayo angapange chinthu champhamvu motero ngati dzuŵa. Zimatiuzanso kuti Yehova n’ngwanzeru, chifukwa panafunika nzeru kuti dzuŵalo lipangidwe, limene limapereka kutentha ndi kuunika koma ilo osapsa konse.

Zimene Yehova analenga zimasonyeza kuti amatikonda. Tangoganizani za mitundumitundu ya zipatso zonse zimene zili padziko lapansi. Yehova akanafuna akanangotipatsa mtundu umodzi wokha wa zipatso—kapenanso osatipatsa m’komwe chilichonse. Koma m’malo mwake, Yehova anatipatsa mitundu yambiri ya zipatso zosiyanasiyana kwambiri m’mapangidwe ake, ukulu, maonekedwe, ndi kukoma kwake. Izi zimasonyeza kuti Yehova ndi Mulungu wachikondi, wopatsa kwambiri, woganizira ena, ndiponso wokoma mtima.—Salmo 104:24.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena