Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • be tsamba 71-tsamba 73 ndime 3
  • Kukambirana M’makalata

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kukambirana M’makalata
  • Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kulalikira M’kalata
  • Mawu Pang’ono za Kayalidwe ka Kalata
  • Mawu Omveka Bwino
  • Kalata Yachitsanzo
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
  • Kalembedwe ka Makalata
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki​​—Muzilemba Makalata Abwino
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
  • Bokosi la Mafunso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
be tsamba 71-tsamba 73 ndime 3

Kukambirana M’makalata

MAKALATA akweza miyoyo ndi makhalidwe a mamiliyoni a anthu. Mabuku ochuluka a m’Malemba Achigiriki Achikristu poyambirira anali makalata. Ifenso lero tikhoza kulemba makalata pofuna kulimbikitsa atsopano, kulemberana ndi mabwenzi athu, kulimbikitsa abale ndi alongo omwe ali pamaudindo apadera, kulimbikitsa amene akukumana ndi mavuto, ndi kupereka chidziŵitso chofunikira pa zochitika za mpingo.—1 Ates. 1:1-7; 5:27; 2 Pet. 3:1, 2.

Kulemba makalata ndi njira inanso yothandiza kuchitira umboni. M’madera ena, anthu ambiri amakhala m’nyumba zokhala ndi chitetezo chokhwima kwambiri, kapena m’mahotela ena mmene salola kulalikiramo. Ena sapezeka kaŵirikaŵiri panyumba, choncho timasemphana nawo pamene tilalikira nyumba ndi nyumba. Ena amakhala m’malo otsekeredwa.

Nthaŵi zina, mungalephere kutuluka kunja chifukwa cha kudwala kapena ngati kunja sikunache bwino. Kodi mungalembe kalata kuti mupitirize ulaliki wanu kwa wachibale kapena munthu wina amene munachezapo naye? Kodi wina wa ophunzira Baibulo anu anasamuka? Kum’lembera kalata kungam’thandize kwambiri kukhalabe waumoyo mwauzimu. Kapena mungagaŵane mfundo yabwino ya m’Malemba ndi aja amene angoloŵa kumene m’banja, kapena amene angokhala kumene ndi mwana woyamba, kapenanso amene ataya wokondedwa wawo mu imfa.

Kulalikira M’kalata

Polalikira m’kalata kwa munthu amene simunakumanepo naye, choyamba m’dziŵitseni amene inuyo muli. Mungafotokoze kuti mukuchita ntchito yodzipereka imene ikuchitika padziko lonse lapansi. Ngati n’kofunikira, tchulani kuti ndinu wa Mboni za Yehova. Tchulani chifukwa chimene mwalembera kalata m’malo momuyendera. Lembani monga kuti mukulankhula naye pamaso m’pamaso. Ngakhale ndi choncho, mogwirizana ndi langizo lakuti “khalani ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda,” samalani kwambiri zimene mungaulule kwa munthuyo za inumwini.—Mat. 10:16.

Lembaninso m’kalatamo zimene mukanamuuza mukanati mwamuyendera. Mungatenge mawu oyamba m’buku la Kukambitsirana kapena mungagwiritse ntchito ulaliki wa Malemba wochokera m’kope laposachedwa la Utumiki Wathu wa Ufumu. Mukhoza kufunsa funso ndi kum’limbikitsa kuganizirapo. Ofalitsa ena amangonena kuti tili ndi pulogalamu yaulere yoyankha mafunso a m’Baibulo kenako amalemba mitu ina kuchokera m’limodzi la mabuku athu. Onani kalata ya chitsanzo patsamba  73. Ikuthandizani kuona mmene mungalembere. Koma ndi bwino kumasiyanitsa mawu ake, chifukwa m’kupita kwa nthaŵi, athu angamalandire kalata imodzimodzi mobwerezabwereza.

Anthu ena amagwa mphwayi kuti aŵerenge kalata yaitali yochokera kwa munthu amene samudziŵa. Choncho kungakhale kwanzeru kulemba kalata yaifupi. Izitha munthuyo asanatope kuiŵerenga. N’koyeneranso kutsekeramo kapepala koitanira anthu ku misonkhano ku Nyumba ya Ufumu. Mungaphatikizemonso thirakiti, bulosha, kapena magazini ya Nsanja ya Olonda kapena Galamukani! ndi kufotokoza kuti mukhoza kumam’tumizira nthaŵi zonse ngati angafune. Kapenanso mungam’funse ngati kuli kotheka kumuyendera kuti mudzapitirize kukambirana nkhaniyo.

Mawu Pang’ono za Kayalidwe ka Kalata

Tsopano yang’ananinso kalata yachitsanzo ya ulalikiyo. Onani zotsatirazi: (1) Yalembedwa mwaudongo, osati kungomwaza mawu ayi. (2) Ngakhale emvulopuyo itati yasochera, wolandirayo adzakhalabe ndi dzina ndi adiresi ya wolemba. (3) Cholinga cha kalata chatchulidwa momveka bwino ndi mosapita m’mbali m’ndime yoyamba. (4) Mfundo yaikulu iliyonse yafotokozedwa m’ndime yosiyana. (5) Malinga ndi cholinga chake, kalatayo sinalembedwe momasuka kwambiri komanso osati ngati kalata yantchito.

M’kalata yantchito, monga imene mlembi wa mpingo amalembera ku ofesi ya nthambi, mumakhalanso keyala kapena kuti adiresi ya mpingo, dzina la mlembi, keyala yake, ndi tsiku. Mumakhalanso dzina ndi adiresi ya wolembayo kapena bungwe kumene kalatayo ikupita. Kenako pamatsatira malonje. Pomaliza kalata, pansi pa mawu akuti “Ndine wanu” kapena “Ndine,” timalemba saini kapena kuti siginecha. Siginechayo iyenera kulembedwa pamanja.

M’kalata iliyonse, samalani kulemba mawu molondola, galamala (malamulo a chinenero) yabwino, zizindikiro za m’kalembedwe zoyenerera, komanso kulemba mwaudongo. Kulemba koteroko kumachititsa kalata yanu pamodzi ndi uthenga wake kulemekezeka.

Kunja kwa emvulopu, nthaŵi zonse lembani adiresi yoyankhira—makamaka adiresi yanu ya positi. Ngati mungaone kuti si kwanzeru kupereka adiresi yanu polembera anthu amene simuwadziŵa, funsani akulu ngati angakuloleni kugwiritsa ntchito keyala ya mpingo monga adiresi yoyankhira. Keyala ya Watch Tower Society siyenera konse kugwiritsidwa ntchito pacholinga chimenechi, chifukwa zingaoneke ngati kuti kalata yanu inatumizidwa kuchokera ku ofesi ya Sosaite ndipo zingachititse msokonezo. Ngati simunalembe adiresi yoyankhira koma mwaphatikizamo mabuku, zimenezonso zingaonetse ngati kuti Sosaite ndiyo yatumiza.

Onetsetsani kuti mwamatapo masitampa a ndalama zokwanira, makamaka ngati mwaikamo mabuku. Ngati mwamatapo masitampa a ndalama zosakwanira, wolandirayo angam’lipiritse ndalama zopereŵerazo, ndipo zimenezo zingafooketse uthenga wanu. Kumbukirani kuti m’mayiko ambiri, masitampa otumizira kalata imene mwaphatikizamo bulosha kapena magazini, amakhala a ndalama zambiri kuposa otumizira kalata yokha.

Mawu Omveka Bwino

Pamene mwatha kulemba kalata yanu, iŵerengeni kuti mupende mawu ake. Kodi akumveka motani? Kodi akumveka aubwenzi ndi osamala? Chikondi ndi chifundo ndi ena mwa makhalidwe amene tiyenera kusonyeza pochita zinthu ndi ena. (Agal. 5:22, 23) Ngati muona kuti penapake mawu akumveka otsutsa kapena owopseza, asintheni.

Kalata imatha kukafika kumalo amene inuyo simungafikeko. Mfundo imeneyi imapangitsa kalata kukhala chida chothandiza kwambiri pa ulaliki wathu. Popeza kuti kalata imaimira inuyo ndi khalidwe lanu, ganizirani mofatsa zimene ikunena, mmene ikuonekera, ndi mmene mawu ake akutulukira. Ikhoza kuloŵetsa munthu panjira ya ku moyo, kum’limbikitsa, ndi kum’thandiza kupitirizabe.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena