Bokosi la Mafunso
◼ Kodi tiyenera kukumbukira chiyani polemba makalata kwa eni nyumba amene sitinathe kuwapeza panyumba?
Kaamba ka zifukwa zosiyanasiyana, tikupeza kuonana ndi anthu kukhala kovuta kwambiri pamene tifika panyumba pawo. Ofalitsa ena aona kulemba makalata kukhala njira yothandiza yowafikira. Pamene kuli kwakuti zimenezi zingatulutse zipatso zabwino, tifunikira kulingalira zikumbutso zina zimene zingatithandize kupeŵa zovuta zina:
Musagwiritsire ntchito keyala ya Sosaite yoyankhira makalata. Kuchita zimenezi kungasonyeze mosayenera kuti maofesi athu ndiwo amatumiza makalatawo, zikumachititsa mavuto osayenera ndipo nthaŵi zina ndalama zolipirira zowonjezereka.
Tsimikizirani kuti mwalemba keyala yolondola ndi kuikapo masitampa okwanira.
Musalembere kalata kwa “Mwini nyumba”; gwiritsirani ntchito dzina lenileni.
Musasiye makalata pakhomo pamene palibe munthu aliyense panyumbapo.
Makalata aafupi ngabwino koposa. Ikanimo trakiti kapena magazini m’malo mwa kuyesa kulemba uthenga wautali.
Makalata otayipidwa amakhala osavuta kwambiri kuŵerenga ndipo amasonkhezera kwambiri chidwi.
Makalata samaŵerengeredwa kukhala maulendo obwereza pokhapokhapo ngati munapereka umboni mwachindunji kwa munthuyo papitapo.
Ngati mukulembera munthu amene poyamba anasonyeza chidwi, muyenera kupereka keyala kapena nambala ya telefoni kotero kuti alankhulane nanu. Longosolani za programu yathu ya phunziro la Baibulo.
Muitanireni kumisonkhano ya mpingo wa kumaloko. Mpatseni keyala ndi nthaŵi zosonkhana.
Musapitirize kutumiza makalata kwa osapezeka panyumba mutabwezera ndime; wofalitsa amene ali mwini ndime tsopano ndiye ali ndi thayo la kugwiramo ntchito.