PHUNZIRO 35
Kubwereza Komveketsa Mfundo
KUPHUNZITSA kogwira mtima kumaphatikizapo kutchula zinthu mobwereza. Mfundo yofunika akaitchula mobwereza, omvera amakaikumbukira kwambiri. Makamaka mfundoyo akaitchulanso m’njira yosiyanako, m’pamene angaimvetse bwino kwambiri.
Ngati omvera anu sangathe kukumbukira zimene mumanena, mawu anu sadzasintha zimene iwo amakhulupirira kapena kusintha moyo wawo. Akhoza kungoganizira chabe mfundo zina zimene munagogomeza kwambiri, basi n’kuthera pomwepo.
Mlangizi wathu Wamkulu Yehova, amatipatsa chitsanzo chabwino pa kubwereza mawu. Iye anapereka Malamulo Khumi ku mtundu wa Israyeli. Kudzera mwa mngelo wom’lankhulira, Yehova analankhula kwa mtunduwo kuwauza malamulo khumiwo pa Phiri la Sinai. Pambuyo pake anadzawapatsa kwa Mose atalembedwa. (Eks. 20:1-17; 31:18; Deut. 5:22) Mouzidwa ndi Yehova, Mose anabwerezanso malamulowo kwa mtunduwo asanaloŵe m’Dziko Lolonjezedwa, ndipo mwa mzimu woyera, Mose analemba zimenezo pa Deuteronomo 5:6-21. Mwa malamulo operekedwa kwa Aisrayeli panali lakuti akonde Yehova ndi kum’tumikira ndi mtima wonse, moyo wonse, ndi nyonga yonse. Lamulo limenelinso analibwerezabwereza. (Deut. 6:5; 10:12; 11:13; 30:6) Chifukwa chiyani? Monga Yesu ananenera, linali “lamulo lalikulu ndi loyamba.” (Mat. 22:34-38) Kudzera mwa mneneri Yeremiya, Yehova anakumbutsa anthu a Yuda, koposa ka 20, za kufunika komvera iye m’zinthu zonse zimene anawalamula. (Yer. 7:23; 11:4; 12:17; 19:15) Ndiponso kudzera mwa Ezekieli, Mulungu ananena koposa ka 60 kuti amitundu “adzadziŵa kuti Ine ndine Yehova.”—Ezek. 6:10; 38:23.
M’nkhani zosimba utumiki wa Yesu, timaonanso kubwereza mawu kogwira mtima. Mwachitsanzo, pali nkhani zinayi za Uthenga Wabwino—iliyonse imafotokoza zochitika zofunika kwambiri zimene zimapezekanso m’nkhani zina za Uthenga Wabwino koma zofotokozedwa m’njira zina. Pamene Yesu mwiniwakeyo anali kuphunzitsa, anafotokoza mfundo yaikulu imodzimodzi pa zochitika zosiyanasiyana komanso m’njira zosiyanasiyana. (Marko 9:34-37; 10:35-45; Yoh. 13:2-17) Ndipo Yesu ali pa Phiri la Azitona, kutatsala masiku ochepa kuti aphedwe, anabwereza mawu pofuna kutsindika langizo lofunika ili: “Dikirani, pakuti simudziŵa tsiku lake lakufika Ambuye wanu.”—Mat. 24:42; 25:13.
Mu Utumiki wa Kumunda. Pamene mulalikira anthu, mumafuna kuti akakumbukire zimene mukunena. Kubwereza mfundo mwaluso kungakuthandizeni kukwaniritsa cholinga chimenecho.
Kaŵirikaŵiri, kubwereza mfundo pamene ikufotokozedwa kumathandiza kuti ikhomerezeke m’maganizo mwa munthu. Choncho, mutaŵerenga lemba, mungaligogomeze mwa kutchulapo mawu ofunika kwambiri ndi kufunsa kuti, “Kodi mwaona mmene mawuŵa anawalembera?”
Mawu omaliza nawo kukambirana kwanu angakhalenso ogwira mtima. Mwachitsanzo, munganene kuti: “Ndikhulupirira mfundo yaikulu imene muziikumbukira ndi yakuti . . .” Kenako itchuleni mosavuta. Munganene kuti: “Cholinga cha Mulungu n’chakuti dziko lapansi lidzakhale paradaiso. Ndipo cholinga chimenecho chidzakwaniritsidwa ndithu.” Kapena munganene kuti: “Baibulo limasonyeza bwino lomwe kuti tikukhala m’masiku otsiriza. Ndipo kuti tikapulumuke, tifunikira kuphunzira zimene Mulungu amafuna kwa ife.” Ngakhale kunena kuti: “Monga taonera, Baibulo limapereka uphungu wothandiza mmene tingathanire ndi mavuto a m’banja.” Nthaŵi zina mungangobwereza mawu a m’Baibulo monga mfundo yofunika kuikumbukira. Koma kuti zimenezi zitheke, m’pofunika kukonzekera.
Pamaulendo obwereza, komanso pamaphunziro a Baibulo, mungabwerezenso mfundo zazikulu mwa kuŵerenga mafunso obwereza.
Ngati munthu alephera kumvetsa kapena kugwiritsa ntchito uphungu wina wa m’Baibulo, mungafunikire kutchulanso nkhaniyo koposa kamodzi. Yesani kuifotokoza m’njira zosiyanasiyana. Sikuti kukambiranako kuzichita kutenga nthaŵi yaitali ayi, koma kuzikhala kolimbikitsa wophunzirayo kumaganizira nkhaniyo. Kumbukirani, Yesu anagwiritsa ntchito njira yobwereza nkhani imeneyi pothandiza ophunzira ake kugonjetsa mzimu wofuna kukhala patsogolo pa ena.—Mat. 18:1-6; 20:20-28; Luka 22:24-27.
Pokamba Nkhani. Pamene mukamba nkhani pa pulatifomu, cholinga chanu sikungopereka mfundo ayi. Mumafuna kuti omvera anu amvetse mfundozo, akazikumbukire, ndipo akazigwiritse ntchito. Kuti zimenezi zitheke, dziŵani kubwereza mfundo mogwira mtima.
Komabe, ngati mubwereza mfundo zazikulu pafupipafupi kwambiri, omvera anu angataye chidwi. Mosamala, sankhani mfundo zofunikiradi kuzimveketsa bwino. Zimenezi zikhale mfundo zazikulu zimene zili maziko a nkhani yanu, koma zingaphatikizeponso mfundo zina zimene zingakhale zofunikira kwa omverawo.
Kuti mubwereze bwino mfundo zazikulu, choyamba zitchuleni m’mawu anu oyamba. Chitani zimenezo mwa masentensi aafupi opereka chithunzi cha nkhani imene mukambe, limodzi ndi mafunso, kapena zitsanzo zachidule zosonyeza mavuto ofunika kuwathetsa. Mungatchule chiŵerengero cha mfundo zazikulu zimene zilipo ndi kuziŵerenga mwa kuzitchula manambala. Ndiyeno fotokozani imodzi ndi imodzi m’nkhani yanu. Mungatsindike mfundozo m’nkhaniyo mwa kubwerezanso mfundo yaikulu iliyonse musanapite pa ina. Kapena mungatero mwa kugwiritsa ntchito chitsanzo chosonyeza mmene mfundo yaikuluyo imathandizira. Mungatsindikenso mfundo zazikulu ndi mawu omaliza obwereza mfundozo, oziunika mwa kusonyeza kuipa kosazitsata, oyankha mafunso amene mwafunsa poyamba, kapena osonyeza njira zothanira ndi mavuto amene mwatchula.
Kuwonjezera pa zomwe tafotokozazi, wokamba nkhani waluso amaganizira mosamala za anthu osiyanasiyana mwa omvera ake. Ngati ena akulephera kumvetsa mfundo ina, iye amatha kuzindikira zimenezo. Ngati mfundoyo ndi yofunika kwambiri, amaibwerezanso. Komabe, kubwereza ndendende mawu omwewo sikungakwaniritse cholingacho nthaŵi zina. Palinso njira zina zophunzitsira. Ayenera kukhala wokhoza kusinthasintha. Angafunikire kuloŵetsapo mfundo zina zimene sanakonzekere. Kudziŵa kukwaniritsa zosoŵa za omvera mwa njira imeneyi kumathandiza kwambiri kuti mukhale mphunzitsi wogwira mtima.