Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • be phunziro 47 tsamba 247-tsamba 250 ndime 1
  • Kugwiritsa Ntchito Mwaluso Zinthu Zooneka Pophunzitsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kugwiritsa Ntchito Mwaluso Zinthu Zooneka Pophunzitsa
  • Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Nkhani Yofanana
  • Mafanizo a Zinthu Zodziŵika Bwino
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Kugwiritsa Ntchito Bwino Zinthu Zooneka
    Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
  • Kulemekeza Ena
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Kuthandiza Awo Amene Ali ndi AIDS
    Galamukani!—1994
Onani Zambiri
Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
be phunziro 47 tsamba 247-tsamba 250 ndime 1

PHUNZIRO 47

Kugwiritsa Ntchito Mwaluso Zinthu Zooneka Pophunzitsa

Kodi muyenera kuchita motani?

Gwiritsani ntchito zithunzi, mapu, machati, kapena zinthu zina kuti mfundo zofunika zioneke bwino kwambiri.

N’chifukwa chiyani kuli kofunikira?

Kuphunzitsa ndi zinthu zooneka, kaŵirikaŵiri kumakhomereza kwambiri mfundo m’maganizo koposa mmene mawu chabe angachitire.

N’CHIFUKWA chiyani kuli kofunika kugwiritsa ntchito zinthu zooneka pophunzitsa? Chifukwa zimathandiza kuti kuphunzitsa kwanu kukhale kogwira mtima kwambiri. Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu anagwiritsa ntchito zinthu zooneka pophunzitsa, ndipo tikhoza kuphunzira kwa iwo. Mukaphatikiza zinthu zooneka pa mawu anu ofotokozera, omvera anu amaphunzira kudzera m’njira ziŵiri. Zimenezi zimathandiza kukopa chidwi cha omverawo ndi kukhomereza kwambiri zimene mukuphunzitsa. Kodi mungaphatikize motani zinthu zooneka polalikira uthenga wabwino? Nanga mungatsimikize bwanji kuti mukuzigwiritsa ntchito mwaluso?

Mmene Aphunzitsi Aakulu Koposa Anaphunzitsira ndi Zinthu Zooneka. Yehova anagwiritsa ntchito zinthu zooneka ndi zosaiŵalika popereka maphunziro ofunika kwambiri. Usiku wina anatulutsa Abrahamu panja namuuza kuti: “Tayang’anatu kumwamba, uŵerenge nyenyezi, ngati ukhoza kuziŵerenga zimenezo: . . . Zoterozo zidzakhala mbewu zako.” (Gen. 15:5) Ngakhale kuti zimene anamulonjezazo zinaoneka kukhala zosatheka malinga ndi kuona kwa munthu, zinam’khudza kwambiri Abrahamu moti anakhulupirira Yehova ndi mtima wonse. Tsiku lina, Yehova anatengera Yeremiya kwa woumba mbiya namuuza kuti aloŵe m’nyumba youmbirayo kuti aone mmene munthuyo akuumbira dongo. Limenelo linali phunziro lamphamvu ndi losaiŵalika pamfundo yakuti Mlengi ali ndi ulamuliro pa anthu! (Yer. 18:1-6) Nanga Yona bwanji? Kodi zikanatheka kuiŵala phunziro losonyeza chifundo limene Yehova anam’patsa kudzera ku msatsi? (Yona 4:6-11) Yehova anauzanso aneneri ake kuti achite zinthu zoyerekeza kukwaniritsidwa kwa maulosi mwa kugwiritsa ntchito zinthu zooneka zoyenerera. (1 Maf. 11:29-32; Yer. 27:1-8; Ezek. 4:1-17) Ngakhale zinthu za m’chihema ndi m’kachisi, zinalinso zinthu zooneka zotithandiza kuzindikira zinthu zakumwamba. (Aheb. 9:9, 23, 24) Mulungu anagwiritsanso ntchito masomphenya ambiri popereka mauthenga ofunika.—Ezek. 1:4-28; 8:2-18; Mac. 10:9-16; 16:9, 10; Chiv. 1:1.

Kodi Yesu anagwiritsa ntchito motani zinthu zooneka pophunzitsa? Pamene Afarisi ndi achipani cha Herode anayesa kum’kola Yesu m’mawu ake, anawapempha kuti am’patse ndalama ya kobiri ndipo anawasonyeza chithunzi cha Kaisara chomwe chinali pandalamapo. Ndiyeno anafotokoza kuti zinthu za Kaisara ziperekedwe kwa Kaisara, koma zinthu za Mulungu ziperekedwe kwa Mulungu. (Mat. 22:19-21) Pofuna kuphunzitsa za kulemekeza Mulungu ndi zonse zimene tili nazo, Yesu anafotokoza za mkazi wamasiye m’kachisi amene chopereka chake—tindalama tiŵiri tochepetsetsa—tinali zonse anali nazo. (Luka 21:1-4) Nthaŵi ina anasonyeza mwana wamng’ono ngati chitsanzo cha kudzichepetsa, popeza mwana sakhumba kutchuka. (Mat. 18:2-6) Iyenso mwiniwakeyo anapereka chitsanzo cha kudzichepetsa mwa kusambitsa mapazi a ophunzira ake.—Yoh. 13:14.

Mmene Tingaphunzitsire ndi Zinthu Zooneka. Mosiyana ndi Yehova, anthufe sitingathe kupereka uthenga kudzera m’masomphenya. Komabe, mabuku a Mboni za Yehova amakhala ndi zithunzi zambiri zokopa maganizo. Zigwiritseni ntchito pothandiza anthu achidwi kuti aone m’maganizo mwawo Paradaiso wa padziko lapansi wolonjezedwa m’Mawu a Mulungu. Paphunziro la Baibulo la panyumba, mungasonyeze wophunzira wanu chithunzi chokhudzana ndi zimene mukuphunzira ndi kum’funsa anene zimene akuonapo. N’zosangalatsa kuona kuti pamene mneneri Amosi anapatsidwa masomphenya ena, Yehova anam’funsa kuti: “Amosi, uona chiyani?” (Amosi 7:7, 8; 8:1, 2) Inunso mungafunse mafunso otero pamene musonyeza anthu zithunzi zimene zaikidwapo ngati zophunzitsira.

Kulemba masamu kuti muŵerengere zaka, kapena kusonyeza tchati yoonetsa zochitika zofunika kwambiri, kumathandiza anthu kumvetsa mosavuta maulosi monga aja onena za “nthaŵi zisanu ndi ziŵiri” za pa Danieli 4:16, ndi “masabata makumi asanu ndi aŵiri” otchulidwa pa Danieli 9:24. Zinthu zooneka zophunzitsira ngati zimenezi zimapezeka m’mabuku athu ambiri ophunzirira.

Pophunzira Baibulo ndi banja lanu, zinthu ngati chihema, kachisi wa ku Yerusalemu, ndi masomphenya a kachisi amene Ezekieli anaona zingakhale zosavuta kumvetsa ngati mugwiritsa ntchito chithunzi kapena tchati. Zimenezi zimapezeka m’mabuku ngati Insight on the Scriptures, kumapeto kwa Baibulo la New World Translation of the Holy Scriptures—With References, ndi m’magazini osiyanasiyana a Nsanja ya Olonda.

Poŵerenga Baibulo pamodzi ndi banja lanu, gwiritsani ntchito kwambiri mapu. Londolani ulendo wa Abrahamu kuchokera ku Uri kupita ku Harana mpaka ku Beteli. Onaninso njira imene mtundu wa Israyeli unayenda pamene anatuluka mu Igupto paulendo wopita ku Dziko Lolonjedwa. Pezani malo amene mtundu uliwonse wa Israyeli unapatsidwa ngati cholandira chawo. Pendani ukulu wa dziko limene Solomo analamulira. Tsatirani njira imene Eliya anadzera kuchokera ku Yezreeli mpaka ku chipululu kupitirira Beereseba, pothaŵa Yezebeli amene anafuna kumupha. (1 Maf. 18:46–19:4) Pezani mizinda ndi midzi imene Yesu analalikirako. Londolani maulendo a Paulo monga awafotokozera m’buku la Machitidwe.

Zinthu zooneka zimathandizanso pofotokozera wophunzira Baibulo zochitika za mpingo wathu. Mungasonyeze wophunzira wanu pulogalamu yosindikiza ya msonkhano waukulu ndi kufotokoza nkhani zimene zikakambidwe kumeneko. Angasangalalenso kuwayendetsa kuti aone Nyumba ya Ufumu kapena kupita nawo kuti akaone ofesi yanthambi ya Mboni za Yehova. Zimenezi zingawathandize kuchotsa maganizo olakwika ponena za ntchito yathu ndi cholinga chake. Powaonetsa malo pa Nyumba ya Ufumu, fotokozani mmene holoyo imasiyanira ndi malo olambirira a zipembedzo zina. Sonyezani mmene alili malo abwino ophunzirira. Sonyezaninso zinthu zokhudzana ndi ulaliki wathu—ngati malo ogaŵirapo mabuku, mapu a gawo, ndi mabokosi a zopereka (kusiyana ndi mbale zosonkhetsera ndalama).

Ngati muli ndi mavidiyo ojambulidwa mwa chilolezo cha Bungwe Lolamulira, agwiritseni ntchito polimbikitsa ophunzira kudalira Baibulo, powathandiza kudziŵa bwino ntchito ya Mboni za Yehova, ndi polimbikitsa oonererawo kutsatira makhalidwe olimbikitsidwa m’Baibulo.

Kuphunzitsa Gulu la Anthu ndi Zinthu Zooneka. Ngati zinthu zooneka muzikonzekera ndi kuzifotokoza bwino, zimakhala zogwira mtima pophunzitsa gulu la anthu. Zinthu zoterozo zoperekedwa ndi gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, zilipo za mitundu yosiyanasiyana.

Nkhani zophunzira za mu Nsanja ya Olonda kaŵirikaŵiri zimakhala ndi zithunzi zimene wochititsa phunzirolo amagwiritsa ntchito pomveketsa bwino mfundo zofunika kwambiri. N’chimodzimodzinso ndi mabuku ophunzira pa Phunziro la Buku la Mpingo.

Maautilaini ena a nkhani za onse angafune kugwiritsa ntchito zinthu zooneka pofuna kumveketsa bwino mfundo zina. Komabe, phindu lalikulu limakhalapo poika maganizo kwambiri pa zimene zili m’Baibulo, ndipo ambiri mwa omvera amakhala ali nalo. Ngati nthaŵi zina muona kuti m’pofunika kusonyeza chithunzi kapena mawu olembedwa pofuna kumveketsa mfundo zazikulu za nkhani yanu, yesezani pasadakhale kuti mutsimikize kuti ngakhale anthu amene adzakhala kumbuyo akatha kuziona bwinobwino (kapena kuziŵerenga) zinthuzo. Koma zinthu zoterozo n’zosafunika kuzigwiritsa ntchito kaŵirikaŵiri.

Cholinga chathu pogwiritsa ntchito zinthu zooneka polankhula ndi pophunzitsa sikusangalatsa ena ayi. Pamene mugwiritsa ntchito chinthu chooneka choyenerera, chiyenera kumveketsa bwino mfundo zofunika kwambiri. Zinthu zoterozo zimakwaniritsa cholinga chake pamene zithandiza kumveketsa mawu olankhulidwa kuti azindikirike bwino, kapena pamene zipereka umboni wamphamvu pa zimene zikunenedwa. Mukazigwiritsa ntchito mwaluso, zinthu zooneka zimakhomereza mfundo kwambiri moti anthu amatha kukumbukira zinthuzo ndi mfundo zakenso kwa zaka zambiri.

Kumva ndi kuona kumathandiza kwambiri pophunzira. Kumbukirani mmene Aphunzitsi aakulu koposa anachitira zimenezi, ndipo yesetsani kutengera iwo pamene mukuphunzitsa ena.

ZINTHU ZOONEKA ZOTHANDIZA KUPHUNZITSA . . .

  • Ziyenera kusonyeza ndi kumveketsa mfundo zofunika kwambiri.

  • Cholinga chake chiyenera kukhala kuphunzitsa.

  • Ziyenera kuoneka bwino lomwe kwa omvera onse ngati zikugwiritsidwa ntchito papulatifomu.

ZOCHITA: Ndandalikani pansipa zinthu zooneka zimene mungagwiritse ntchito . . .

Pothandiza ena kuzindikira bwino gulu la Yehova

․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

Pophunzitsa mfundo za m’Baibulo kwa mwana wamng’ono

․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena