Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • be phunziro 31 tsamba 190-tsamba 193 ndime 2
  • Kulemekeza Ena

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulemekeza Ena
  • Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Nkhani Yofanana
  • Mafanizo a Zinthu Zodziŵika Bwino
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Kugwiritsa Ntchito Mwaluso Zinthu Zooneka Pophunzitsa
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Kodi Ndingawapangitse Motani Ena Kundipatsa Ulemu?
    Galamukani!—1992
  • Muzilemekeza Anthu Ena
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
Onani Zambiri
Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
be phunziro 31 tsamba 190-tsamba 193 ndime 2

PHUNZIRO 31

Kulemekeza Ena

Kodi muyenera kuchita motani?

Sonyezani kuti mumaganizira ena, apatseni ulemu.

N’chifukwa chiyani kuli kofunikira?

Kusonyeza ulemu ndi udindo wa Mkristu umene umathandiza ena kukhala ndi mtima wolandira zimene akuwaphunzitsa kuchokera m’Baibulo.

MALEMBA amatilangiza ‘kuchitira ulemu anthu onse’ ndi ‘kusachitira mwano munthu aliyense.’ (1 Pet. 2:17; Tito 3:2) Ndithudi, munthu aliyense amene tingakumane naye ‘anakhalapo monga mwa mafanizidwe a Mulungu.’ (Yak. 3:9) Aliyense ndi munthu amene Kristu anam’fera. (Yoh. 3:16) Ndipo onse ndi ofunikira kumva uthenga wabwino kotero kuti alabadire, akapulumuke. (2 Pet. 3:9) Alipo anthu ena ofunikira ulemu wapadera malinga ndi moyo wawo kapena udindo wawo.

Nanga n’chifukwa chiyani anthu ena amakana kupereka ulemu umene Baibulo limalimbikitsa? Ena ndi chifukwa cha mwambo wa kwawo umene umasonyeza munthu woyenera kum’patsa ulemu malinga ndi fuko lake, maonekedwe a khungu, kukhala mwamuna kapena mkazi, umoyo wabwino, msinkhu, chuma, kapena udindo. Kufala kwa katangale pakati pa antchito a boma kwapangitsa anthu kusalemekezanso ulamuliro wa boma. M’mayiko ena anthu ndi okhumudwa kwambiri ndi moyo wawo, mwina amagwira ntchito maola ochuluka kungoti apezeko zofunika pamoyo, mwinanso amakhala ndi anthu a khalidwe losasonyezana ulemu. Achinyamata amaumirizidwa ndi anzawo kuti azipandukira aphunzitsi amene sawakonda ndi anthu ena audindo. Ambiri amawonongeka poonerera nkhani za pawailesi yakanema zoonetsa ana ochita zinthu zopusitsa makolo awo ndi kuwalamulira. Pamafunika kuyesetsa zolimba kuti tiletse maganizo a dziko amenewo kuwononga ulemu wathu kwa ena. Koma pamene tilemekeza anthu ena, pamakhala mkhalidwe wabwino umene umalimbikitsa kupatsana nzeru mosavuta.

Kufikira Anthu Mwaulemu. Munthu amene amachita ntchito ya Mulungu amayembekezeka kusonyeza ulemu m’kavalidwe ndi m’kachitidwe ka zinthu. Koma makhalidwe amene anthu amati ndi oyenerera amasiyana malinga ndi malo. Kumadera ena ndi kupanda ulemu kufikira munthu wina mutavala chisoti kapena mutapisira dzanja m’thumba. Koma kumadera ena, zimenezo si vuto. Ganizirani maganizo a anthu akumaloko kuti musawakhumudwitse. Kuchita zimenezo kungakuthandizeni kupeŵa zopinga zimene zingakulepheretseni kufalitsa uthenga wabwino mogwira mtima.

N’chimodzimodzinso polankhula ndi anthu ena, makamaka achikulire. Kumadera ambiri, ndi kupanda ulemu ngati achichepere atchula achikulire ndi dzina loyamba, kupatula ngati achicheperewo achita kuuzidwa kutero. Kumadera ena, ngakhale achikulire sayenera kutchula munthu wosam’dziŵa bwino ndi dzina loyamba. Ndiponso, m’zinenero zambiri amatchula mawu olemekeza ngati “inu,” “a ujeni,” kapena mawu ena osonyeza ulemu kwa munthu wamkulu kapena waudindo.

Ulemu Pokumana ndi Munthu. Kumadera amene anthu si ochuluka kwambiri, ndi ulemu kupereka zikomo kapena moni kwa munthu amene mwakumana naye, kaya poyenda panjira kapena poloŵa m’nyumba. Ulemu umenewo amausonyeza kaya mwa kumwetulira, kugwedeza mutu, ngakhale kungokweza zikope. Kunyalanyaza munthu wina amakuona kuti ndi kupanda ulemu.

Koma alipo anthu amene angaonebe ngati mwawanyalanyaza ngakhale mutapereka ulemuwo. Chifukwa chiyani? Chifukwa amatha kuonabe kuti simukuwaŵerengera ngati munthu payekha. Anthu ena amatchulidwa ndi mawu owaika m’magulu chifukwa cha chofooka cha thupi. Kaŵirikaŵiri anthu olemala ndi ena odwala amasalidwa kapena kupewedwa. Komabe, Mawu a Mulungu amatilangiza mmene tiyenera kusonyezera chikondi ndi ulemu kwa anthu oterowo. (Mat. 8:2, 3) Aliyense wa ife ali ndi zofooka zinazake zochokera ku uchimo wa Adamu. Kodi mungaone kuti anthu amakulemekezani ngati nthaŵi zonse amakutchulani ndi chofooka chanu? Kodi simungakonde kuti azikudziŵani ndi makhalidwe abwino ambiri amene muli nawo?

Kusonyeza ulemu kumaphatikizaponso kuzindikira mutu wa panyumba. M’malo ena, m’pofunika kulankhula ndi mutu choyamba musanalalikire kwa ena a m’banjalo. Ngakhale kuti ntchito yathu yolalikira ndi kuphunzitsa ndi yochokera kwa Yehova, timadziŵa kuti makolo ndi amene Mulungu anawapatsa udindo wophunzitsa ana, kuwalangiza ndi kuwatsogolera. (Aef. 6:1-4) Choncho, mukafika pakhomo, ndi bwino nthaŵi zonse kuyamba mwakambirana ndi makolo musanalankhule ndi ana.

M’pofunikanso kudziŵa kuti achikulire amadziŵa zambiri pamoyo ndipo tiyenera kuwalemekeza. (Yobu 32:6, 7) Kuzindikira mfundo imeneyi kunathandiza mpainiya wina wachitsikana ku Sri Lanka amene anafikira bambo wina wachikulire. Wachikulireyo poyamba anakana kuti amvere uthengawo, amvekere: “Mwana ngati iwe ungaphunzitse ine Baibulo?” Poyankha mtsikanayo anati: “Ayi, sikuti ndabwera kuti ndikuphunzitseni. Koma kuti ndikuuzenkoni zimene ndaphunzira. Zandisangalatsa kwambiri moti ndingofuna n’tauzako anthu ena.” Kuyankha kwaulemu kwa mpainiyayo kunagwira mtima wachikulireyo. Kenako bamboyo anati: “Chabwino tandiuza, waphunzira chiyani?” Mtsikanayo anati: “Ndaphunzira mmene ndingapezere moyo wamuyaya.” Bamboyo anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Si achikulire onse amene angasonyeze kuti akukhumba atapatsidwa ulemu woterowo, koma ochuluka angayamikire kwambiri.

Komabe, nthaŵi zina munthu akhoza kupereka ulemu wopitirira malire. Ku zilumba za Pacific ndi kumadera ena, mawu aulemu ofika nawo pamudzi kapena kwa mafumu angathandize Mboni kuti anthuwo amvetsere ndi kuti iye apeze mwayi wolankhula kwa mafumu ndi anthu awo. Komabe, ulemu wachiphamaso umakhala chipongwe. (Miy. 29:5) Mofananamo, chinenero chingakhale ndi mawu olemekeza, komatu ulemu wachikristu sufuna kuchita kunyanyira nawo.

Kulankhula Mwaulemu. Baibulo limatilimbikitsa kufotokoza chifukwa cha chiyembekezo chathu mwa “chifatso ndi mantha.” (1 Pet. 3:15) Choncho, ngakhale kuti tingathe kusonyeza mosavuta zolakwa za maganizo a munthu winayo, kodi kungakhale kwanzeru kuchita zimenezo m’njira yom’chotsera ulemu wake? Kodi sikungakhale bwino kwambiri kumvetsera moleza mtima, mwinanso kufunsa chifukwa chake akuganiza choncho, ndi kuyesa kumumvetsa pamene tikumufotokozera zifukwa za m’Malemba?

Ulemu ngati wa pakati pa anthu aŵiri umenewo uyeneranso kukhalapo pamene mukulankhula ku gulu muli pa pulatifomu. Wokamba nkhani amene amalemekeza omvera ake sangawatsutse mwaukali kapena kuonetsa mzimu wotanthauza kuti: “Ngati simukatsatira zimenezi n’nzanu izo.” Kulankhula mwa njira imeneyo kumangogwetsa mphwayi ena. Zimakhala bwino kwambiri kuona omverawo ngati gulu la anthu okonda Yehova ndi ofunitsitsa kum’tumikira! Potengera chitsanzo cha Yesu, tiyenera kukhala omvetsa pochita ndi anthu ofooka mwauzimu, atsopano, kapena ochedwa kuyamba kugwiritsa ntchito uphungu wa m’Baibulo.

Omverawo amatha kuona kuti wokamba nkhaniyo akuwalemekeza ngati iyenso amadziphatikiza kuti afunikira kugwiritsa ntchito Mawu a Mulungu mokwanira. Choncho, potanthauzira malemba, n’kwanzeru kuchepetsako mawu oloza anzanu ngati akuti “inu.” Mwachitsanzo, taonani kusiyana pakati pa funso lakuti: “Kodi inu mumayesetsa kuchita zimenezo?” ndi lakuti “Aliyense wa ife adzifunse kuti: ‘Kodi ine ndimayesetsa kuchita zimenezo?’” Mfundo ya mafunso aŵiriŵa ndi yofanana, koma loyamba likusonyeza kuti wolankhulayo sakudziika pamalo ofanana ndi omvera ake. Lachiŵiri likulimbikitsa munthu aliyense, kuphatikizapo wolankhulayo, kuti apende mkhalidwe wake ndi zolinga zake.

Peŵani njerengo kapena nthabwala zongofuna kuseketsa anthu. Zimenezo zimachotsera ulemu uthenga wa m’Baibulo. N’zoona kuti tiyenera kukhala osangalala potumikira Mulungu. Ndipo mwina nkhani yathu ingakhale ndi mbali zina zoseketsa. Komabe, kusandutsa nkhani yaikulu kukhala nthabwala ndiko kupanda ulemu kulinga kwa omvera ndi Mulungu.

Tionetsetse kuti mmene tikuwafikira anthu, khalidwe lathu, ndi kalankhulidwe kathu, nthaŵi zonse tizionetsa kuti timaona anthu ena mmene Yehova watiphunzitsira.

MMENE MUNGACHITIRE ZIMENEZO

  • Kumbukirani mmene Yehova amawaonera anthu.

  • Zindikirani mutu wa banja, msinkhu, ndi anthu audindo.

  • Lolani anthu ufulu wokhala ndi maganizo awo.

  • Muwamvetsetse omvera anu.

ZOCHITA: Ganizirani za munthu wina wamkulu kapena wamng’ono pa inu. Lingalirani za mmene mungam’fikire, mmene mungayambire kukambirana naye, ndi zimene mungachite pofuna kuonetsa ulemu woyenerera kwa munthuyo ndi zimene wanena. Kachiteni zimene mwakonzekerazo.

Njira zimene ndingasonyezere ulemu wokulirapo

․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena