PHUNZIRO 46
Mafanizo a Zinthu Zodziŵika Bwino
NDIPONSO, n’kofunika kwambiri kuti mafanizo amene mukupereka azigwirizana ndi nkhani imene mukukamba. Komabe, kuti azikhala ogwira mtima kwambiri, m’pofunikanso kuti aziyenerana ndi omvera anu.
Kodi mtundu wa omvera anu ungathandize motani kusankha mafanizo oyenerera polankhula pamaso pa gulu? Kodi Yesu Kristu anachita motani? Polankhula ndi makamu a anthu kapena ndi ophunzira ake, Yesu sanagwiritse ntchito zitsanzo zokhudza zinthu zachilendo za moyo wa mayiko a kunja kwa Israyeli. Zitsanzo zoterozo zikanakhala zosatsatirika bwino kwa omvera ake. Mwachitsanzo, Yesu sanatchule zochitika za m’mabanja achifumu a Igupto kapena zokhudza zipembedzo za ku Indiya. Chikhalirechobe, mafanizo ake anali okhudza zochitika zodziŵika kwa anthu a m’mayiko onse. Iye analankhula za kusoka zovala, kuchita malonda, kutayikidwa zinthu za mtengo wapatali, ndi kufika ku madyerero a chikwati. Anali kudziŵa mmene anthu amachitira m’mikhalidwe yosiyanasiyana, ndipo anasamala zimenezo. (Marko 2:21; Luka 14:7-11; 15:8, 9; 19:15-23) Popeza kuti ulaliki umenewu makamaka anali kuupereka kwa Aisrayeli, mafanizo a Yesu kaŵirikaŵiri anali okhudza zinthu ndi zochitika za moyo wa tsiku ndi tsiku. N’chifukwa chake iye anali kutchula zinthu ngati ulimi, mmene nkhosa zimachitira kwa mbusa wawo, ndi kusunga vinyo m’matumba achikopa. (Marko 2:22; 4:2-9; Yoh. 10:1-5) Iye anatchulanso zitsanzo zodziŵika zakale—kulengedwa kwa anthu aŵiri oyamba, Chigumula cha m’masiku a Nowa, chiwonongeko cha Sodomu ndi Gomora, imfa ya mkazi wa Loti, ndi zina zambiri. (Mat. 10:15; 19:4-6; 24:37-39; Luka 17:32) Kodi inunso mumaganizira bwino lomwe zochitika zofala kwa omvera anu ndi chikhalidwe chawo pamene mukusankha mafanizo?
Bwanji ngati mukulankhula kwa munthu mmodzi kapena anthu oŵerengeka, m’malo mwa gulu lalikulu? Yesetsani kusankha fanizo loyenerera womvera mmodzi kapena angapo. Pamene Yesu analalikira kwa mkazi wachisamariya pachitsime pafupi ndi mudzi wa Sukari, analankhula za “madzi amoyo,” ‘kusamvanso ludzu,’ ndi “kasupe wa madzi otumphukira ku moyo wosatha”—onseŵa anali mafanizo okhudzana ndi ntchito ya mkaziyo. (Yoh. 4:7-15) Ndipo polankhula ndi amuna amene anali kutsuka maukonde awo, iye anapereka mafanizo okhudzana ndi ntchito ya usodzi. (Luka 5:2-11) Yesu akanafuna akanatchula za ulimi kwa mkaziyo ndi asodziwo, chifukwa anthuwo anali kukhala m’madera aulimi. Koma kutchula zinthu zimene iwo anali kuchita kunali kogwira mtima kwambiri chifukwa amaziona bwino lomwe m’maganizo mwawo! Kodi inunso mumayesetsa kuchita zimenezo?
Pamene Yesu anasamala kwambiri za “nkhosa zotayika za banja la Israyeli,” mtumwi Paulo sanatumidwe kwa Aisrayeli okha komanso kwa amitundu Akunja. (Mat. 15:24; Mac. 9:15) Kodi izi zikutanthauza kuti Paulo analankhula m’njira yosiyanako? Inde. Polembera Akristu a ku Korinto, iye anatchula mpikisano wothamanga, kudyera chakudya mu akachisi a mafano, ndi ndawala za kuguba akapambana nkhondo. Izi ndi zinthu zimene Akunjawo anali kuzidziŵa bwino lomwe.—1 Akor. 8:1-10; 9:24, 25; 2 Akor. 2:14-16.
Kodi inunso mumakhala wosamala muja anachitira Yesu ndi Paulo posankha mafanizo ndi zitsanzo zogwiritsa ntchito pophunzitsa? Kodi mumaganizira za moyo wa omvera anu ndiponso zochitika zawo za tsiku ndi tsiku? N’zoona kuti dziko lasintha kwambiri poyerekeza ndi m’zaka 100 zoyambirira. Anthu ambiri amatha kumva nkhani za padziko lonse pa wailesi yakanema. Kaŵirikaŵiri amatha kudziŵa zochitika za kumayiko ena. Ngati ndi mmene zilili kwanuko, sikulakwa kupereka mafanizo okhudza nkhani ngati zimenezo. Komabe, zimene zimakhudza anthu kwambiri ndi zinthu zochitika pamoyo wawo—zinthu ngati nyumba zawo, mabanja awo, ntchito zawo, chakudya chimene amadya, ndi nyengo ya kudera lakwawo.
Ngati muona kuti mukufotokoza zambiri pofuna kumveketsa fanizo lanu, n’kutheka kuti mwina mukukamba za chinthu chosadziŵika kwenikweni kwa omvera anu. Fanizo loterolo limaphimba mfundo imene mukuyesa kuphunzitsa. Chotsatira chimakhala chakuti omverawo amangokumbukira fanizo lokhalo osati mfundo ya m’Malemba imene mukufuna kuphunzitsa.
M’malo moyerekeza zinthu zovuta kumva, Yesu anatchula zochitika za masiku onse. Anatchula zinthu zazing’ono pomveketsa zinthu zazikulu ndi zinthu zosavuta pomveketsa zinthu zozama. Mwa kugwirizanitsa zochitika za tsiku ndi tsiku ndi mfundo zauzimu, Yesu anathandiza anthu kumvetsa mosavuta zinthu zauzimu zimene anawaphunzitsa ndipo ankazikumbukira. Kodi si chitsanzo chabwino choyenera kutengera?