Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • be phunziro 52 tsamba 265-tsamba 267 ndime 4
  • Kulimbikitsa Ena Mogwira Mtima Kuti Achitepo Kanthu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulimbikitsa Ena Mogwira Mtima Kuti Achitepo Kanthu
  • Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Nkhani Yofanana
  • Lalikirani Mwachangu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Chikondi cha pa Abale Nchokangaza
    Nsanja ya Olonda—1991
  • ‘Kudandaulira mwa Chikondi’
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Mfundo Zazikulu za M’makalata Opita kwa Tito, Filemoni ndi Aheberi
    Nsanja ya Olonda—2008
Onani Zambiri
Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
be phunziro 52 tsamba 265-tsamba 267 ndime 4

PHUNZIRO 52

Kulimbikitsa Ena Mogwira Mtima Kuti Achitepo Kanthu

Kodi muyenera kuchita motani?

Limbikitsani ena kuti achitepo kanthu powapatsa zifukwa zokhutiritsa kapena uphungu wochokera ku gwero lodalirika. Zimenezi zimafuna kulankhula moona mtima.

N’chifukwa chiyani kuli kofunikira?

Kulimbikitsa ena mogwira mtima kuti alabadire kumawachititsa kuzindikira kuti n’kofunika msanga kuchita zinthu zokondweretsa Yehova.

AKULU achikristu ayenera ‘kulimbikitsa ena kulabadira m’chiphunzitso cholamitsa.’ (Tito 1:9, NW) Nthaŵi zina, izi ziyenera kuchitidwa m’mikhalidwe yovuta kwambiri. Koma n’kofunika kupereka uphungu wogwirizana ndi zimene Malemba amalangiza. N’chifukwa chake akulu ayenera kumvera uphungu wakuti: “Usamalire . . . kuchenjeza.” (1 Tim. 4:13) Ngakhale kuti nkhani ino ikukhudza makamaka akulu kapena aja amene akukalamira udindo umenewo, nthaŵi zina makolonso amafunikira kulimbikitsa ana kuti achitepo kanthu. Ngakhale aja amene amachititsa maphunziro a Baibulo nthaŵi zina amafunikiranso kulimbikitsa ophunzira awo kuti achitepo kanthu. Zikatero, malangizo ofananawo amagwiranso ntchito.

Pamene Chilimbikitso Chimafunikira. Pofuna kudziŵa ngati chilimbikitso chili chofunikira, m’pofunika kufufuza zochitika za m’Baibulo pamene chilimbikitso choterocho chinaperekedwa. Mtumwi Petro analimbikitsa akulu kuti asamalire udindo wawo woŵeta nkhosa za Mulungu. (1 Pet. 5:1, 2) Paulo analimbikitsa Tito kuti azilimbikitsa anyamata kuti “akhale odziletsa.” (Tito 2:6) Paulo analimbikitsanso Akristu anzake kuti ‘azinena chimodzimodzi’ ndi kupeŵa ochititsa magaŵano pakati pa abale. (1 Akor. 1:10; Aroma 16:17; Afil. 4:2) Ngakhale kuti Paulo anayamikira abale a mpingo wa ku Tesalonika pa zinthu zabwino zimene anali kuchita, analimbikitsa kuti apitirizebe kugwiritsa ntchito malangizo onse amene anawalandira. (1 Ates. 4:1, 10) Petro nayenso anadandaulira Akristu anzake kuti ‘akanize zilakolako za thupi.’ (1 Pet. 2:11) Yuda nayenso analimbikitsa abale ake kuti ‘amenye zolimba nkhondo ya chikhulupiriro’ poona makhalidwe otayirira a anthu osapembedza. (Yuda 3, 4) Akristu onse analimbikitsidwa kuti azichenjezana wina ndi mnzake kuti pasapezeke wina amene mphamvu ya uchimo ikanamuumitsa khosi. (Aheb. 3:13) Petro analimbikitsa Ayuda amene anali asanakhulupirire Kristu kuti: “Mudzipulumutse kwa mbadwo uno wokhotakhota.”—Mac. 2:40.

Kodi tiyenera kusonyeza mtima wotani kuti tipereke chilimbikitso champhamvu m’mikhalidwe ngati imeneyo? Kodi wopereka chilimbikitsoyo angachite motani kuti afulumize anthu ndi kuti asamveke wolamula kapena waukali?

“Mwa Chikondi.” Ngati tipereka chilimbikitso mosakhala “mwa chikondi,” chingamveke chowawa. (Fil. 9) Zoona, ngati kukhala kofunikira kuti ena achitepo kanthu msanga, sonyezani zimenezo m’kalankhulidwe kanu. Kulankhula mofeŵa kwambiri kungamveke ngati kupepesa. Komanso, chondererani omverawo ndi mtima woona ndi mwachifundo. Kuchonderera mwachikondi kumakhudza mitima ya omvera ndipo kumawalimbikitsa kulabadira. Polankhula maganizo ake komanso a anzake, Paulo anauza Atesalonika kuti: “Mudziŵa kuti tinachitira yense wa inu payekha, monga atate achitira ana ake a iye yekha, ndi kukudandaulirani.” (1 Ates. 2:11) Oyang’anira achikristu amenewo anadandaulira abalewo mwa chikondi. Inunso muzilankhula ndi nkhaŵa yeniyeni kwa omvera anu.

Khalani wosamala. Musakhumudwitse anthu amene cholinga chanu n’kuwalimbikitsa kuchitapo kanthu. Komanso, musalephere kupereka “uphungu wonse wa Mulungu” kwa omvera anu. (Mac. 20:27) Anthu oyamikira sangakhumudwe kapena kudana nanu chifukwa chakuti mwawalimbikitsa kuchita chinthu chabwino.—Sal. 141:5.

Ndi bwino nthaŵi zambiri kuyamba ndi mawu othokoza pofuna kulimbitsa ena kuti alabadire. Ganizirani zinthu zabwino zimene abale anu amachita—zinthu zimene Yehova amakondwera nazo: chikhulupiriro chimene amasonyeza mwa ntchito zawo, chikondi chimene chimawalimbikitsa kudzipereka, ndi chipiriro chawo pokumana ndi zovuta. (1 Ates. 1:2-8; 2 Ates. 1:3-5) Zimenezi zidzathandiza abale anu kuona kuti mumawalemekeza ndi kuwamvetsa, ndipo adzakhala ndi chidwi cholandira chilangizo chanu.

“Ndi Kuleza Mtima Konse.” Chilimbikitso chiyenera kuperekedwa “ndi kuleza mtima konse.” (2 Tim. 4:2) Kodi zimenezi zimaphatikizapo chiyani? Kuleza mtima kumaphatikizapo kupirira mofatsa pamene wina akulakwirani kapena kukukwiyitsani. Munthu amene amaleza mtima amakhala ndi chiyembekezo chakuti omvera akewo akagwiritsa ntchito zimene akuwauza. Ngati mupereka chilimbikitso ndi mzimu umenewu, omvera anu adzaona kuti simukuwafunira zoipa. Ngati musonyeza chidaliro chakuti abale ndi alongo anu akufunadi kutumikira Yehova ndi mtima wonse mudzawapatsa chidwi chofuna kuchita chabwino.—Aheb. 6:9.

Mwa “Chiphunzitso Cholamitsa.” Kodi mkulu ‘angachenjeze motani m’chiphunzitso cholamitsa?’ Mwa ‘kugwira mawu okhulupirika’ monga mwa luso lake la kuphunzitsa. (Tito 1:9) M’malo mopereka maganizo anuanu, kopani anthu ndi mphamvu ya Mawu a Mulungu. Lolani Baibulo likuthandizeni kudziŵa zoyenera kunena. Tchulani mapindu amene angakhalepo mwa kugwiritsa ntchito zimene Baibulo limanena pankhaniyo. Dziŵani bwino zotsatira zapanopa ndi zam’tsogolo za kusamvera Mawu a Mulungu, ndipo zitchuleni kuti omvera anu aone kufunika kochitapo kanthu moyenerera.

Onetsetsani kuti mwafotokoza bwino lomwe zimene omvera anu ayenera kuchita ndi mmene ayenera kuchitira. Sonyezani bwino lomwe kuti zifukwa zanu zikuchokera m’Malemba. Ngati Malembawo amapereka ufulu winawake wosankha chochita, fotokozani bwino mlingo wake wa ufuluwo. Ndiyeno, m’mawu anu omaliza, apempheni komaliza mwa kuwalimbikitsa kuchitapo kanthu.

Ndi “Ufulu wa Kulankhula.” Kuti munthu alimbikitse ena mogwira mtima, ayenera kukhala ndi “ufulu wa kulankhula m’chikhulupiriro.” (1 Tim. 3:13, NW) Kodi chimachititsa munthu kulankhula momasuka n’chiyani? Ndicho kukhala ndi “chitsanzo cha ntchito zabwino” zogwirizana ndi zimene akulimbikitsa abale ake kuti azichita. (Tito 2:6, 7; 1 Pet. 5:3) Ngati zili choncho, olimbikitsidwawo amazindikira kuti wowalimbikitsayo sakuwayembekezera kuti angachite zimene iye sachita. Amatha kuona kuti akhoza kutsanzira chikhulupiriro chake mmene iyenso akutsanzirira Kristu.—1 Akor. 11:1; Afil. 3:17.

Langizo lolimbikitsa ena kuchitapo kanthu lochokera m’Mawu a Mulungu komanso loperekedwa ndi mzimu wa chikondi limathandiza kwambiri. Amene ali ndi udindo wolimbikitsa ena kuchitapo kanthu ayenera kuyesetsa kuti azilimbikitsa m’njira yothandiza.—Aroma 12:8.

MMENE MUNGALIMBIKITSIRE ENA MOGWIRA MTIMA KUTI ACHITEPO KANTHU

  • Sonyezani chikondi ndi kuleza mtima, ndipo lankhulani moona mtima.

  • Chilimbikitso chanu chizichokera m’Mawu a Mulungu.

  • Zimene mukulimbikitsa zigwirizane ndi chitsanzo chanu.

ZOCHITA: Ŵerengani kalata ya mtumwi Paulo kwa Filemoni. Funani zinthu izi: (1) chiyamikiro cholimbikitsa, (2) chifukwa chimene Paulo akupemphera Onesimo, (3) mfundo zimene anakhutiritsa nazo Filemoni za mmene anayenera kulandirira kapolo wobwererayo, ndipo (4) chidaliro cha Paulo chakuti Filemoni adzachita zoyenera. Onani mmene mungatengere chitsanzo chimenechi polimbikitsa ena kuchitapo kanthu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena