Lalikirani Mwachangu
1. Kodi Paulo anapereka malangizo otani amene ndi ofunika kwambiri masiku ano?
1 “Lalika mawu, chita nawo mwachangu.” (2 Tim. 4:2) Kodi n’chifukwa chiyani malangizo a Paulo amenewa ndi ofunika kwambiri masiku ano? Kodi malangizo amenewa angakhudze bwanji moyo wathu ndiponso wa anthu ena?
2. N’chifukwa chiyani timachita khama pofufuza anthu amene sanamvepo uthenga wabwino?
2 Moyo wa Anthu Uli Pangozi: Anthu ambiri sanamvepo uthenga wabwino umene ungawathandize kuti adzapulumuke. (Aroma 10:13-15; 1 Tim. 4:16) Anthu ambiri amaganizo oyenera amakhala m’madera amene timalalikira kawirikawiri. Kusintha tsiku kapena nthawi imene timalalikira m’madera amenewa, kungathandize kuti tizipeza anthu ena atsopano. Khama lotereli ndi lofunika kuti tikhale ndi chikumbumtima choyera komanso kuti tipewe mlandu wa magazi.—Mac. 20:26.
3. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji nthawi mwanzeru tikakhala mu utumiki?
3 Akhristu oyambirira ‘anadzaza Yerusalemu yense ndi chiphunzitso chawo’ ngakhale kuti ankatsutsidwa ndiponso kuzunzidwa kwambiri. (Mac. 5:28) Kodi ifenso tatsimikiza “kupereka umboni wokwanira”? (Mac. 10:42) Kodi timagwiritsa ntchito nthawi mwanzeru tikakhala mu utumiki? Tikamayembekezera anzathu amene aima panyumba ina, kodi timalalikira kwa anthu odutsa m’njira?
4. Kodi kulalikira mwachangu kumatithandiza bwanji kukhala maso?
4 Kukhala Maso: Popeza mapeto a dongosolo lino la zinthu ayandikira kwambiri, tiyenera kukhala maso, kapena kuti kukhala tcheru. (1 Ates. 5:1-6) Tikamalankhula kawirikawiri za zimene tikuyembekezera mu Ufumu wa Mulungu, timapewa kulemetsedwa ndi dongosolo lino la zinthu. (Luka 21:34-36) Ndipo ‘tikamakumbukira nthawi zonse’ tsiku la Yehova, tidzalimbikira kugwira ntchito imeneyi yomwe ndi yopulumutsa anthu.—2 Pet. 3:11, 12.
5. Kodi kulemekeza moyo kumatilimbikitsa bwanji mu utumiki?
5 Tikamalalikira mwachangu timasonyeza kuti timaona moyo ngati mmene Yehova amauonera. Iye “safuna kuti wina akawonongeke, koma amafuna kuti anthu onse alape.” (2 Pet. 3:9; Ezek. 33:11) Choncho tiyeni tiziyesetsa kulalikira kwa anthu ambiri n’cholinga choti Yehova atamandidwe.—Sal. 109:30.