‘Pamene Yehova Anautsa Oweruza’
SIMUNGAVUTIKE kupeza Phiri la Tabori (F4) pa mapuŵa. Phiri limeneli lili kum’mwera chakumadzulo kwa Nyanja ya Galileya, m’Chigwa cha Yezreeli. Tayerekezerani kuti mukuona asilikali 10,000 atasonkhana pamwamba pa phirili. Yehova anagwiritsa ntchito Woweruza Baraki ndi mneneri wamkazi Debora kusonkhanitsa Israyeli kuti alimbane ndi Mfumu Yabini ya Akanani yomwe inakhala ikuwapondereza kwa zaka 20. Motsogoleredwa ndi Sisera, mkulu wa asilikali, magaleta 900 a Yabini, okhala ndi zikwakwa zachitsulo zoopsa kwambiri anachoka nawo ku Haroseti kubwera khwawa la Kisoni, pakati pa Megido ndi Phiri la Tabori.
Woweruza Baraki anatsogolera amuna a Israyeli kupita kuchigwako kukamenya nkhondo ndi asilikali a Sisera. Yehova anawathandiza kupambana nkhondoyo mwa kuchititsa kuti deralo lisefukire madzi zomwe zinatitimitsa magaleta a Sisera, Akananiwo n’kusoŵa pogwira. (Ower. 4:1–5:31) Aka kanali kamodzi chabe mwa maulendo ambirimbiri omwe Israyeli anapambana nkhondo mothandizidwa ndi Mulungu m’nthaŵi za Oweruza.
Kanani atalandidwa, dzikoli linagaŵidwa kwa mafuko a Israyeli. Onani malo amene mafuko osiyanasiyana amene sanali Alevi anakhala. Fuko laling’ono la Simeoni linapatsidwa midzi m’dera la Yuda. Yoswa atamwalira, moyo wauzimu ndiponso makhalidwe a mtunduwu zinasokonezeka kwambiri. Israyeli ‘anasautsika kwambiri’ ndi adani. Powachitira chifundo, “Yehova anautsa oweruza,”—amuna 12 okhulupirika ndi olimba mtima—omwe anapulumutsa Israyeli pazaka 300.—Ower. 2:15, 16, 19.
Woweruza Gideoni anagwiritsa ntchito asilikali 300 okha, opandanso zida zokwanira koma amphamvu, kugonjetsa asilikali 135,000 a Amidyani. Nkhondoyi anamenyera pakati pa mapiri a Giliboa ndi More. Atawagonjetsa adaniwo pakumenyanako, Gideoni anawathamangitsira kum’maŵa, mpaka m’chipululu.—Ower. 6:1–8:32.
Yefita, Mgileadi wa fuko la Manase, anapulumutsa midzi ya Aisrayeli ya kum’maŵa kwa Yordano kwa Aamoni omwe ankaipondereza. Kuti apambane, mwachionekere Yefita anadutsa Msewu Wachifumu womwe unkadutsa ku Ramoti Gileadi mpaka kudera la Aroeri.—Ower. 11:1–12:7.
Kudera lakugombe lozungulira Gaza ndi Asikeloni ndi komwe Samsoni anazunzira Afilisti. Gaza ali m’dera la madzi ambiri lotchuka ndi ulimi. Samsoni anagwiritsa ntchito nkhandwe 300 potentha minda ya Afilisti ya tirigu, ya mphesa, ndiponso ya azitona.—Ower. 15:4, 5.
Malinga ndi nkhani za m’Baibulo kapena mafuko awo, oweruzaŵa anali m’Dziko Lolonjezedwa lonselo. Zilibe kanthu kuti woweruza anagwirira kuti ntchito yake, koma Yehova anali kuwasamalira bwinobwino anthu ake olapa panthaŵi ya mavuto.
[Mapu patsamba 15]
(Onani m’kabuku kenikeni kuti mumvetse izi)
Mafuko ndi Oweruza
Oweruza
1. Otiniyeli (Tribe of Manasseh)
2. Ehudi (Tribe of Judah)
3. Samagara (Tribe of Judah)
4. Baraki (Tribe of Naphtali)
5. Gideoni (Tribe of Issachar)
6. Tola (Tribe of Manasseh)
7. Yairi (Tribe of Manasseh)
8. Yefita (Tribe of Gad)
9. Ibzani (Tribe of Asher)
10. Eloni (Tribe of Zebulun)
11. Abidoni (Tribe of Ephraim)
12. Samsoni (Tribe of Judah)
Malire a Mafuko (Onani m’kabuku kenikeni kuti mumvetse izi)
Midzi ya Manase ya M’dera la Fuko Lina
E4 Doro
E5 Megido
E5 Taanaki
F4 Eni-doro
F5 Betiseani (Betisani)
F5 Ibleamu (Gati-rimoni)
Midzi ya Simeoni ya M’dera la Fuko Lina
C9 Saruheni (Saraimu) (Siliimu)
C10 Beti-lebaotu (Betibiri)
D8 Eteri (Tokeni)
D9 Zikilaga
D9 Aini
D9 Hazar-susah?
D9 Asana
D9 Beer-sheba
D10 Hazari-susa?
E9 Etamu
E9 Beti- malikabotu
E9 Betueli? (Kesili?)
E9 Seba? (Yesuwa)
E10 Baalata-beeri (Baala)
E10 Ezemu
Midzi ya Alevi Yopulumukirako
E8 Hebroni
F3 Kedesi
F6 Sekemu
H4 Golani
H5 Ramoti Gileadi
H8 Bezeri
Njira Zazikulu
B10 Via Maris
G10 Msewu Wachifumu
Mafuko a Israyeli
DANI (D7)
D7 Yopa
E8 Zola
YUDA (D9)
C8 Asikeloni
C9 Gaza
C9 Saruheni (Saraimu) (Siliimu)
C10 Beti-lebaotu (Betibiri)
C12 Azimoni
C12 Kadesi
D7 Yabineli
D8 Eteri (Tokeni)
D9 Zikilaga
D9 Aini
D9 Hazari-susa?
D9 Asana
D9 Beer-sheba
D10 Hazari-susa?
E8 Leki
E8 Betelehemu
E8 Hebroni
E9 Etamu
E9 Beti- malikabotu
E9 Betueli? (Kesili?)
E9 Seba? (Kasili)
E10 BBaalata-beeri (Baala)
E10 Ezemu
F8 Yerusalemu
ASERI (E3)
E2 Turo
E4 Haroseti
E4 Dor
F1 Sidoni
MANASE (E5)
E6 Samiri (Samariya)
E6 Piratoni
F6 Sekemu
G5 Abelemehola
EFRAIMU (E7)
E7 Timinati-sera
F6 Tapuwa
F6 Silo
F7 Beteli (Luzi)
NAFITALI (F3)
F2 Beth-anath
F3 Kedesh
G3 Hazor
ZEBULONI (F4)
E4 Betelehemu
ISAKARA (F5)
E5 Megido
E5 Kedesi (Kisioni)
E5 Taanaki
F4 Eni-doro
F5 Betesita
F5 Betiseani (Betisani)
F5 Ibleamu (Gati-rimoni)
BENJAMINI (F7)
F7 Giligala
DANI (G2)
G2 Dani (Laisi)
MANASE (H3)
H4 Golani
GADI (H6)
G6 Sukoti
G6 Penieli
G6 Mizipa (Mizepe)
G7 Yogebeha
H5 Ramoti-Gileadi
H7 Raba
H7 Abelikerami
RUBENI (H8)
G7 Hesiboni
G9 Aroeri
H7 Miniti
H8 Bezeri
[Malo ena]
I1 Damasiko
[Mapiri]
F4 Phiri la Tabori
F4 More
F6 Phiri la Ebala
F5 Phiri la Giliboa
F6 Phiri la Gerizimu
[Nyanja]
C5 Nyanja ya Mediterranean (Nyanja Yaikulu)
F9 Nyanja ya Mchere
G4 Nyanja ya Galileya
[Mitsinje]
B11 C. cha Igupto
F6 Mtsinje wa Yordano
G6 C. cha Yaboki
G9 C. cha Arinoni
G11 C. cha Zaredi
[Chithunzi patsamba 14]
Phiri la Tabori, m’dera la Isakara, phiri limeneli lili m’chigwa cha Yezreeli
[Chithunzi patsamba 14]
Kisoni atasefukira anatitimitsa magaleta a Sisera