Israyeli M’masiku a Davide ndi Solomo
MULUNGU analonjeza kuti adzapatsa mbewu ya Abramu dziko lonselo ‘kuyambira pa mtsinje wa Aigupto kufikira . . . mtsinje wa Firate.’ (Gen. 15:18; Eks. 23:31; Deut. 1:7, 8; 11:24) Yoswa ataloŵa m’Kanani, panapita zaka pafupifupi 400 kuti Dziko Lolonjezedwa lifike kumalire amenewo.
Mfumu Davide inagonjetsa ufumu wa Zoba wachiaramiya, umene unafika mpaka ku Firate kumpoto kwa Suriya.a Kum’mwera, dera la Davide linafika kumalire a Igupto chifukwa chogonjetsa Afilisti.—2 Sam. 8:3; 1 Mbiri 18:1-3; 20:4-8; 2 Mbiri 9:26.
Kenako, Solomo analamulira “kuyambira ku Firate kufikira ku dziko la Afilisti ndi kumalire a Aigupto,” ndipo anachitira chithunzi ulamuliro wamtendere wa Mesiya. (1 Maf. 4:21-25; 8:65; 1 Mbiri 13:5; Sal. 72:8; Zek. 9:10) Ngakhale ndi tero, dera limene Israyeli anakhalamo linkanenedwa kuti linayambira “ku Dani kufikira ku Beereseba.”—2 Sam. 3:10; 2 Mbiri 30:5.
Mfumu Solomo sinamvere Mulungu chifukwa chakuti inadzichulukitsira akavalo ndi magaleta. (Deut. 17:16; 2 Mbiri 9:25) Iye ankatha kuyendetsa zimenezi panjira ndi misewu yosiyanasiyana. (Yos. 2:22; 1 Maf. 11:29; Yes. 7:3; Mat. 8:28) Ndi njira zochepa chabe zimene tikudziŵa kwambiri, monga “msewu wokwera kuchokera ku Beteli kumka ku Sekemu, ndi kum’mwera kwa Lebona.”—Ower. 5:6; 21:19.
Buku lakuti The Roads and Highways of Ancient Israel limanena kuti: “Chinthu chodziŵika chimene chimavutitsa zinthu kwambiri pofufuza za misewu ya m’Israyeli wakale n’chakuti sitingathe kudziŵa bwinobwino mmene misewu ya dzikolo ya nyengo ya m’Chipangano Chakale inali kudutsa popeza misewuyo inafafanizika chifukwa chakuti [nthaŵi imeneyo] misewu inalibe tala.” Komabe, mmene deralo lilili komanso zotsala za midzi yakale imeneyi zomwe zafukulidwa zimasonyeza mmene misewu yambiri inadutsa.
Nthaŵi zambiri misewu inathandiza kwambiri asilikali pa kayendedwe kawo. (1 Sam. 13:17, 18; 2 Maf. 3:5-8) Poukira Israyeli, Afilisti anayenda ulendo kuchoka ku Ekroni ndi Gati mpaka kudera lina “pakati pa Soko ndi Azeka.” Asilikali a Saulo anakumana nawo kumeneko ‘kuchigwa cha Ela.’ Davide atapha Goliati, Afilisti anathaŵa kubwerera ku Gati ndi Ekroni, ndipo Davide anakwera ku Yerusalemu.—1 Sam. 17:1-54.
Midzi ya Lakisi (D10), Azeka (D9), ndi Betesemesi (D9) inali m’njira zachilengedwe zodutsa dera la Shefela kuloŵera ku mapiri a Yuda. Choncho midzi imeneyi inkathandiza kwambiri poletsa adani odutsa panjira ya Via Maris kuti asaloŵe m’kati mwa dera la Israyeli.—1 Sam. 6:9, 12; 2 Maf. 18:13-17.
[Mawu a M’munsi]
a Dera la Rubeni linafika mpaka ku Chipululu cha Suriya, ndipo chipululucho kum’maŵa kwake chinathera mu Firate.—1 Mbiri 5:9, 10.
[Bokosi patsamba 16]
MABUKU A M’BAIBULO OLEMBEDWA NTHAŴIYI:
1 ndi 2 Samueli
Masalmo (mbali yake ina)
Miyambo (mbali yake ina)
Nyimbo ya Solomo
Mlaliki
[Mapu patsamba 17]
(Onani m’kabuku kenikeni kuti mumvetse izi)
Deralo ndi Njira zake Nthaŵi Imene Ufumu Unali Umodzi
Malire a M’nthawi ya Solomo
Tifisa
Hamati
Tadimori
Berotai (Kuni?)
Sidoni
Damasiko
Turo
Dani
Yerusalemu
Gaza
Aroeri
Beereseba
Tamara
Ezioni Geberi
Elati (Eloti)
[Mitsinje]
Firate
C. cha Igupto
Misewu ya M’nthawi ya Davide ndi Solomo
B10 Gaza
C8 Yopa
C9 Asidodo
C10 Asikeloni
C11 Zikilaga
C12 CHIPULULU CHA PARANA
D5 Doro
D6 Heferi
D8 Afeki
D8 Rama
D9 Saalibimu
D9 Gezere
D9 Makazi
D9 Ekroni
D9 Betiseani
D9 Gati
D9 Azeka
D10 Soko
D10 Adulamu
D10 Kehila
D10 Lakisi
D11 Yatiri
D12 Beereseba
E2 Turo
E4 Kabulu
E5 Yokineamu (Yokimeamu?)
E5 Megido
E6 Taanaki
E6 Aruboti
E7 Piratoni
E8 Lebona
E8 Zereda
E8 Beteli
E9 Beti-horoni wa Kunsi
E9 Beti-horoni wa Kumtunda
E9 Geba
E9 Gibeoni
E9 Gibeya
E9 Kiriyatu-Yearimu
E9 Nobu
E9 Baalaperazimu
E9 Yerusalemu
E9 Betelehemu
E10 Tekoa
E10 Hebroni
E11 Zifi
E11 Horesi?
E11 Karimeli
E11 Maoni
E11 Esitimoa
F5 Eni-doro
F5 Sunemu
F5 Yezreeli
F6 Betesemesi
F7 Tiriza
F7 Sekemu
F8 Zaretani
F8 Silo
F8 Ofira?
F9 Yeriko
F11 Eni-gedi
G2 Abeli-beti-maaka
G2 Dani
G3 Hazoro
G3 MAAKA
G5 Lodebara (Dibri)
G5 Rogelim
G6 Abelemehola
G7 Sukoti
G7 Mahanaimu
H1 SURIYA
H4 GESURI
H6 Ramoti Gileadi
H8 Raba
H9 Medeba
H11 Aroeri
H12 MOABU
I4 Helamu?
I9 AMONI
[Misewu ikuluikulu]
C10 Via Maris
H6 Msewu Wachifumu
[Mapiri]
F5 Phiri la Giliboa
[Nyanja]
C8 Nyanja ya Mediterranean (Nyanja Yaikulu)
F10 Nyanja ya Mchere (Nyanja Yakufa)
G4 Nyanja ya Galileya
[Kasupe kapena Chitsime]
E9 Eni-rogeli
[Zithunzi patsamba 16]
Kumanja: Chigwa cha Ela, kuyang’ana chakum’maŵa kumapiri a Yuda
M’munsimu: Njira zinathandiza kwambiri pa kayendedwe m’Dziko Lolonjezedwa