Yesu “m’Dziko la Ayuda”
POLALIKIRA kwa Korneliyo, mtumwi Petro anatchulapo zimene Yesu anachita “m’dziko la Ayuda ndi m’Yerusalemu.” (Mac. 10:39) Kodi mukuganiza kuti ndi madera ati amene Yesu anafikako pochita utumiki wake wosaiŵalika m’mbiri ya anthu?
“Dziko la Ayuda” linaphatikizapo Yudeya, kumene Yesu anagwirako ntchito ina ya Mulungu. (Luka 4:44) Yesu atabatizidwa, anatha masiku 40 ali m’chipululu cha Yuda (kapena, Yudeya), chomwe chinali dera louma kwambiri ndi lopanda anthu kumene ogalukira ndi achifwamba anali kukonda kukhala. (Luka 10:30) Panthaŵi ina, Yesu anali kupita chakumpoto kuchokera ku Yudeya pamene analalikira mkazi wa ku Samariya pafupi ndi Sukari.—Yoh. 4:3-7.
Mukapenda Mauthenga Abwino, mudzapeza kuti Yesu anagwira ntchito kwambiri m’Galileya. Ngakhale kuti ankapita kum’mwera ku Yerusalemu kukakhala nawo pa mapwando apachaka, iye anathera mbali yaikulu ya zaka ziŵiri zoyambirira za utumiki wake kumpoto kwa Dziko Lolonjezedwa. (Yoh. 7:2-10; 10:22, 23) Mwachitsanzo, ali pa Nyanja ya Galileya kapena pafupi ndi kumeneko, iye anafotokoza ziphunzitso zambiri zapadera ndi kuchita zozizwitsa zikuluzikulu. Kumbukirani kuti anatontholetsa chimphepo panyanjapo, ndipo anayenda pamadzi akewo. Yesu analalikira ali m’bwato kwa khamu la anthu amene anakhala pagombe lansangalabwi la nyanjayo. Otsatira ake oyambirira komanso apamtima anachokera kumidzi ya asodzi ndi alimi ya pafupi ndi nyanjayo.—Marko 3:7-12; 4:35-41; Luka 5:1-11; Yoh. 6:16-21; 21:1-19.
Pamene Yesu anali kuchita utumiki wake m’Galileya anali kuchokera ku Kapernao m’mphepete mwa nyanja, “kumudzi kwawo.” (Mat. 9:1) Iye anali paphiri la pafupi ndi kumeneko pamene anapereka Ulaliki wa pa Phiri wotchuka uja. Nthaŵi zina, iye anachoka m’dera la Kapernao paulendo wa pabwato kupita ku Magadani, Betsaida, ndi madera ena apafupi.
Onani kuti “kumudzi kwawo” kwa Yesu sikunali kutali kwambiri ndi Nazarete, kumene iye anakulirako; sikunalinso kutali kwambiri ndi Kana, komwe anasandutsa madzi kukhala vinyo; kapenanso ku Nayini, kumene anaukitsa mwana wamwamuna wa mkazi wamasiye; ndiponso sikunali kutali kwambiri ndi Betsaida, kumene mozizwitsa anadyetsa amuna 5,000 ndi kuchiritsa munthu wina wakhungu.
Paskha wa mu 32 C.E. atatha, Yesu anapita kumpoto ku Turo ndi Sidoni, kumadoko a Foinike. Kenako utumiki wake unam’fikitsa ku ina ya mizinda khumi ya Agiriki yotchedwa Dekapoli. Yesu anali pafupi ndi Kaisareya wa Filipi (F2) Pamene Petro anavomereza kuti Yesu ndi Mesiya, ndipo posakhalitsa Yesu anasandulika, mwinamwake pa Phiri la Herimoni. Zimenezi zitachitika, Yesu anakalalikira m’dera la Pereya, tsidya lina la Yordano.—Marko 7:24-37; 8:27–9:2; 10:1; Luka 13:22, 33.
Mlungu wake womaliza padziko lapansi, Yesu anakhala ndi ophunzira ake m’Yerusalemu, “mzinda wa Mfumu yaikulukulu,” ndi madera ozungulira. (Mat. 5:35) Mungathe kupeza malo omwe anali pafupi omwe munaŵerengapo m’Mauthenga Abwino monga ngati Emau, Betaniya, Betefage, ndi Betelehemu.—Luka 2:4; 19:29; 24:13; Onani mapu aang’ono a “Dera la Yerusalemu,” patsamba 18.
[Mapu patsamba 29]
(Onani m’kabuku kenikeni kuti mumvetse izi)
Promised Land (Jesus’ time)
Mmene Dzikoli Linalili Masiku A Yesu
Mizinda ya Dekapoli
E5 Hippo
E6 Pella
E6 Asikopolisi
F5 Gadara
F7 Gerasa
G5 Dion
G9 Filadelfeya
H1 Damasiko
H4 Raphana
I5 Canatha
Njira Zazikulu (Onani m’kabuku kenikeni kuti mumvetse izi)
Njira ya Pakati pa Galileya ndi Yerusalemu Imene Ambiri Anali Kudutsa (Onani m’kabuku kenikeni kuti mumvetse izi)
Njira Ina ya Pakati pa Galileya ndi Yerusalemu Yodzera ku Pereya
A11 Gaza
B6 Kaisareya
B8 Yopa
B9 Luda
B12 Beereseba
C4 Ptolemayi
C8 SAMARIYA
C8 Antipatri
C8 Arimateya
C9 Emau
C10 YUDEYA
C11 Hebroni
C12 IDUMEYA
D1 Sidoni
D2 Turo
D3 PHOENICIA
D4 GALILEYA
D4 Kana
D5 Sepphoris
D5 Nazarete
D5 Nayini
D7 Samariya
D7 Sukari
D9 Efraimu
D9 Betefage
D9 Yerusalemu
D9 Betaniya
D10 Betelehemu
D10 Herodium
D10 CHIPULULU CHA YUDEYA
D12 Masada
E4 Korazini
E4 Betsaida
E4 Kapernao
E4 Magadani
E5 Tiberiya
E5 Hippo
E6 Betaniya? (tsidya la Yordano)
E6 Asikopolisi
E6 Pella
E6 Salemu
E6 Ainoni
E9 Yeriko
F1 ABILENE
F2 Kaisareya wa Filipi
F4 Gamala
F5 Abila?
F5 Gadara
F7 PEREYA
F7 Gerasa
G3 ITUREYA
G5 Dion
G6 DEKAPOLI
G9 Filadalfeya
H1 Damascus
H3 TRAKONITI
H4 Raphana
H12 ARABIYA
I5 Canatha
[Mapiri]
D7 Phiri la Ebala
D7 Phiri la Gerizimu
F2 Phiri la Herimoni
[Nyanja]
B6 Nyanja ya Mediterranean (Nyanja Yaikulu)
E4 Nyanja ya Galileya
E10 Nyanja ya Mchere (Nyanja Yakufa)
[Mitsinje]
E7 Mtsinje wa Yordano
[Akasupe ndi Zitsime]
D7 Chitsime cha Yakobo
[Chithunzi patsamba 28]
Nyanja ya Galileya. Kapernao ali chakuno kumanzere. Maloŵa amaoneka chonchi mukayang’ana kum’mwera chakumadzulo kudutsa Chidikha cha Genesarete.
[Chithunzi patsamba 28]
Asamariya anali kulambira m’Phiri la Gerizimu. Chakutsogoloko kuli Phiri la Ebala