Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • yp2 tsamba 12-13
  • Kusirira Mnyamata Kapena Mtsikana

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kusirira Mnyamata Kapena Mtsikana
  • Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Ndingayambe Chibwenzi Nditafika Msinkhu Wotani?
    Galamukani!—2007
  • Kodi Ndafika Poti N’kukhala ndi Chibwenzi?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
  • Kodi Ndimangocheza Naye, Kapena Ndimamufuna? Gawo 2
    Galamukani!—2012
  • Kodi Cholakwa Nchiyani ndi Kulankhuzana?
    Galamukani!—1992
Onani Zambiri
Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
yp2 tsamba 12-13

Chigawo 1

Kusirira Mnyamata Kapena Mtsikana

Kusukulu kwanu, mukuona mnyamata ndi mtsikana atagwirana manja ndipo akuyenda pang’onopang’ono. Kodi mungamve bwanji?

□ Sindingavutike nazo

□ Ndingasirire pang’ono

□ Ndingasirire kwambiri

Mukuonera filimu ndi anzanu ndipo kenako mukuona kuti onse akhala awiriawiri, kupatulapo inuyo basi. Kodi mungamve bwanji?

□ Sindingavutike nazo

□ Ndingachite manyazi pang’ono

□ Ndingasirire kwambiri

Mnzanu wapamtima wayamba kukondana kwambiri ndi mnyamata kapena mtsikana winawake ndipo chibwenzi chayambika. Kodi mungamve bwanji?

□ Ndingasangalale

□ Ndingasirire pang’ono

□ Ndingakhumudwe nazo

Kaya muli ku sukulu, mumsewu ngakhale kumsika mumaona anyamata ndi atsikana ali awiriawiri. Nthawi zonse mukawaona, mumasirira kwambiri moti mumafuna kuti nanunso mukhale ndi chibwenzi. Koma kodi ndinu wokonzekadi kukhala ndi chibwenzi? Ngati zili choncho, mungatani kuti mupeze munthu woyenerera? Mukam’peza, mungatani kuti chibwenzi chanucho chikhale chosadetsedwa? Mungapeze mayankho a mafunso amenewa m’Mitu 1 mpaka 5.

[Chithunzi chachikulu pamasamba 12, 13]

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena