Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 19 tsamba 50-tsamba 51 ndime 2
  • Miliri Itatu Yoyambirira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Miliri Itatu Yoyambirira
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Mose ndi Aroni Aona Farao
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Miliri Inanso 6
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Kodi Yehova Ndani?
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Mose ndi Aroni—Alengezi Olimba Mtima a Mawu a Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1996
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 19 tsamba 50-tsamba 51 ndime 2
Mose ndi Aroni apita kwa Farao

MUTU 19

Miliri Itatu Yoyambirira

Aiguputo ankaumiriza Aisiraeli kuti azigwira ntchito ngati akapolo. Yehova anatumiza Mose ndi Aroni kwa Farao kukanena kuti: ‘Yehova akuti mulole kuti anthu ake apite kuchipululu kuti akamulambire.’ Koma Farao anayankha mwamwano kuti: ‘Zimene Yehova wanenazo ndilibe nazo ntchito. Sindilola kuti Aisiraeli apite.’ Atatero anawonjezera ntchito zimene Aisiraeli ankagwira. Choncho Yehova anafuna kuti Farao adziwe kuti iye ndi wamkulu kuposa milungu yonse. Kodi ukudziwa zimene anachita? Anabweretsa Miliri 10 ku Iguputo. Yehova anauza Mose kuti: ‘Farao sakufuna kundimvera. Mawa m’mawa akhala ali kumtsinje wa Nailo. Upite ukamuuze kuti popeza sakufuna kuti anthu anga apite, madzi onse a mumtsinje wa Nailo asanduka magazi.’ Mose anamvera Yehova ndipo anapitadi kwa Farao. Kumeneko Aroni anamenya ndi ndodo madzi a mumtsinje wa Nailo, Farao akuona ndipo madziwo anasanduka magazi. Madziwo anayamba kununkha, nsomba zonse zinafa ndipo anthu anasowa madzi akumwa. Koma Farao sanalolebe kuti Aisiraeli apite.

Patatha masiku 7, Yehova anatumanso Mose kwa Farao kukamuuza kuti: ‘Ukapanda kulola kuti anthu anga apite, m’dziko la Iguputo mudzakhala achule paliponse.’ Aroni anakweza ndodo yake m’mwamba ndipo achule anayamba kudzaza m’dziko lonse. Achulewo ankapezeka m’nyumba, pabedi, m’mbale, tingoti paliponse. Zitatero Farao anauza Mose kuti akapemphe kwa Yehova kuti mliriwu uthe ndipo analonjeza kuti alola Aisiraeli kuti apite. Choncho Yehova anathetsadi mliriwo ndipo achulewo anayamba kufa. Aiguputo anaunjika achulewo milumilu moti dziko lonse linkanunkha. Koma Farao ataona kuti mliri watha, sanalolebe kuti Aisiraeli apite.

Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: ‘Aroni amenye pansi ndi ndodo ndipo fumbi lisanduka tizilombo toyamwa magazi.’ Aroni anachitadi zimenezi ndipo paliponse panagwa tizilombo toyamwa magazi. Aiguputo ena anauza Farao kuti: ‘Mliriwu wachokera kwa Mulungu.’ Koma Farao sanalolebe kuti Aisiraeli apite.

Miliri itatu pa Miliri 10 yomwe inagwera Aiguputo: magazi, achule ndi ntchentche zoluma

“Ndiwachititsa kuti adziwe mphamvu ndi nyonga zanga, ndipo adziwa kuti dzina langa ndine Yehova.”​—Yeremiya 16:21

Mafunso: Kodi miliri itatu yoyambirira inali iti? N’chifukwa chiyani Yehova anagwetsa miliriyi?

Ekisodo 5:1-18; 7:8-25; 8:1-19; Nehemiya 9:9, 10

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena