Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 20 tsamba 52-tsamba 53 ndime 3
  • Miliri Inanso 6

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Miliri Inanso 6
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Miliri Itatu Yoyambirira
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Mose ndi Aroni Aona Farao
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Kodi Yehova Ndani?
    Nsanja ya Olonda—1993
  • ‘Yehova Wakhala Chipulumutso Changa’
    Nsanja ya Olonda—2006
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 20 tsamba 52-tsamba 53 ndime 3
Dzombe

MUTU 20

Miliri Inanso 6

Mose ndi Aroni anapita kwa Farao kukamuuza uthenga wochokera kwa Mulungu, wakuti: ‘Ngati sulola kuti anthu anga apite, nditumiza ntchentche zoluma m’dzikoli.’ Ndiyeno ntchentche zolumazo zinadzaza m’nyumba za Aiguputo onse, olemera ndi osauka omwe moti zinali mbwee paliponse. Koma ku Goseni kumene Aisiraeli ankakhala kunalibe ntchentchezi. Kuyambira ndi mliri wa nambala 4 umenewu, miliriyi inkangokhudza Aiguputo okha. Choncho Farao anachonderera Mose kuti: ‘Ukandipemphere kwa Yehova kuti achotse ntchentchezi. Zikatero ndikulolani kuti mupite.’ Koma Yehova atangochotsa ntchentchezo, Farao anasintha maganizo. Iye sanaphunzirepo kanthu.

Yehova anati: ‘Farao akapanda kulola kuti anthu anga apite, ziweto zonse za Aiguputo ziyamba kudwala n’kufa.’ Tsiku lotsatira, ziweto za Aiguputo zinayamba kufa. Koma ziweto za Aisiraeli sizinafe. Ngakhale zinali choncho, Farao sanalolebe kuti Aisiraeli azipita.

Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti apitenso kwa Farao ndipo akaponye phulusa m’mwamba. Phulusalo linasanduka fumbi ndipo linadzaza dziko lonselo moti Aiguputo onse anali fumbi lokhalokha. Fumbilo likagwera munthu kapena ziweto, linkayambitsa zilonda zopweteka kwambiri. Komabe Farao sanalole kuti Aisiraeli apite.

Mliri wa 4 mpaka wa 6 umene unagwa ku Iguputo: tizilombo toyamwa magazi, mliri pa ziweto komanso zilonda

Yehova anatuma Mose kuti apitenso kwa Farao n’kukanena kuti: ‘Kodi sukufunabe kuti anthu anga apite? Mawa ndibweretsa mvula yamphamvu kwambiri yamatalala.’ Tsiku lotsatira, Yehova anabweretsa mvula yamatalala, mabingu ndi moto. Ku Iguputo kunali kusanagwepo chimvula ngati chimenecho chiyambire. Chimvulacho chinawononga mitengo komanso mbewu zonse kupatulapo za ku Goseni. Farao anati: ‘Kandipemphere kwa Yehova kuti aletse chimvulachi ndipo ndikulolani kuti muzipita.’ Koma matalalawo ndi chimvulacho zitangosiya, Farao anasinthanso maganizo.

Kenako Mose anati: ‘Tsopano kugwa dzombe ndipo lidya zomera zonse zimene sizinawonongedwe ndi matalala.’ Choncho kunagwa dzombe lambiri moti linadya mbewu zonse komanso masamba onse a mitengo. Farao anachondereranso kuti: ‘Kandipemphere kwa Yehova kuti achotse dzombeli.’ Koma Yehova atachotsa dzombelo, Farao anakanabe kulola kuti Aisiraeli apite.

Yehova anauza Mose kuti: ‘Tambasula dzanja lako ndipo uloze kumwamba.’ Nthawi yomweyo, kunachita mdima wandiweyani. Kwa masiku atatu, Aiguputo sankatha kuona munthu aliyense kapena chinthu chilichonse. Koma m’nyumba za Aisiraeli munkawala.

Mliri wa 7 mpaka wa 9: matalala, dzombe ndi mdima

Zitatero Farao anauza Mose kuti: ‘Pitani, koma ziweto zanu muzisiye.’ Koma Mose anati: ‘Tizitenga chifukwa tikufuna kukapereka nsembe kwa Mulungu wathu.’ Farao anakwiya kwambiri n’kunena kuti: ‘Choka! Ndisadzakuonenso. Ndipo ukadzangobweranso ndidzakupha.’

“Mudzaonanso kusiyana pakati pa munthu wolungama ndi woipa ndiponso pakati pa munthu amene akutumikira Mulungu ndi amene sakumutumikira.”​—Malaki 3:18

Mafunso: Kodi Yehova anabweretsa miliri inanso iti pa Aiguputo? Kodi miliriyi inali yosiyana bwanji ndi itatu yoyamba ija?

Ekisodo 8:20-32; 9:1-35; 10:1-29

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena