Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 21 tsamba 54-tsamba 55 ndime 2
  • Mliri wa 10

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mliri wa 10
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Mose ndi Aroni Aona Farao
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Miliri Itatu Yoyambirira
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Kodi Yehova Ndani?
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Mulungu Anapulumutsa Ana a Isiraeli
    Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani?
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 21 tsamba 54-tsamba 55 ndime 2
Mwisiraeli akupaka magazi pachitseko cha nyumba yake

MUTU 21

Mliri wa 10

Mose anauza Farao kuti sadzapitanso kukaonana naye. Koma asananyamuke, anamuuza kuti: ‘Lero pakati pa usiku ana onse aamuna oyamba kubadwa a Aiguputo afa, kuyambira mwana wa Farao mpaka ana a akapolo.’

Yehova anauza Aisiraeli kuti adye chakudya chapadera. Anawauza kuti: ‘Mupeze mwana wankhosa kapena wambuzi. Akhale wamphongo komanso wachaka chimodzi. Mumuphe ndipo magazi ake mupake pamafelemu a zitseko zanu. Nyama yakeyo muiwotche ndipo muidye limodzi ndi mikate yopanda zofufumitsa. Mudye mutavala zovala zanu komanso nsapato pokonzekera ulendo. Usiku wa lero mutuluka mu Iguputo.’ Kodi ukuganiza kuti Aisiraeli anamva bwanji atauzidwa zimenezi?

Pakati pa usiku, mngelo wa Yehova anapita kunyumba zonse za mu Iguputo. Nyumba iliyonse imene inalibe magazi pafelemu, mwana woyamba anafa. Koma mngeloyo sankapha ana a m’nyumba zimene anapaka magazi pamafelemu. M’banja lililonse la Aiguputo, kaya lolemera kapena losauka, munafa mwana woyamba. Koma palibe mwana ngakhale mmodzi wa Aisiraeli amene anafa.

Mwana woyamba wa Farao weniweniyo anafanso. Apa m’pamene makani a Farao anathera. Nthawi yomweyo anauza Mose ndi Aroni kuti: ‘Nyamukani. Chokani kuno. Pitani mukalambire Mulungu wanu. Mutengenso ziweto zanu n’kumapita.’

Usiku womwewo, Aisiraeli ananyamuka ndipo kunja kunali kukuwala kwambiri chifukwa mwezi unali wathunthu. Mabanja komanso mafuko ankayendera limodzi. Panali amuna 600,000 komanso akazi ndi ana ambiri. Panalinso anthu a mitundu ina amene anapita nawo kuti akalambirenso Yehova. Apa m’pamene panathera ukapolo wa Aisiraeli.

Pofuna kukumbukira zimene Yehova anachita powapulumutsa, Aisiraeliwa ankadya chakudya chapadera chija chaka chilichonse. Mwambowu ankautchula kuti Pasika.

Aisiraeli akuchoka ku Iguputo

“Ndakusiya ndi moyo kuti ndikusonyeze mphamvu zanga komanso kuti dzina langa lilengezedwe padziko lonse lapansi.”​—Aroma 9:17

Mafunso: Kodi mliri wa 10 unali wotani? Kodi Aisiraeli ankafunika kuchita chiyani kuti atetezeke ku mliriwu?

Ekisodo 11:1-10; 12:1-42; 13:3-10

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena