Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb tsamba 2-3
  • Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Kubwereza Gawo 2
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Kodi Tingagwiritse Ntchito Bwanji Kabuku Kakuti Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
  • Mawu Oyamba
    Galamukani!—2019
  • Zimene Zili M’magaziniyi
    Galamukani!—2019
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb tsamba 2-3
Banja likugwiritsa ntchito Baibulo pophunzira buku la Zimene Tingaphunzire M’nkhani za M’Baibulo

Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

Okondedwa Abale ndi Alongo Athu:

Popeza timalambira Yehova, timakonda kwambiri Baibulo chifukwa ndi Mawu ake. Timadziwa kuti nkhani zake n’zolondola komanso mfundo zake ndi zothandiza. Tikudziwanso kuti Yehova watipatsa Baibulo chifukwa chakuti amatikonda. (Salimo 119:105; Luka 1:3; 1 Yohane 4:19) Timafunitsitsanso kuthandiza ena kuti adziwe mfundo za choonadi zimene zili m’Mawu a Mulungu. Choncho ndife osangalala kutulutsa bukuli la mutu wakuti, “Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo.” Ndiyeno tikufuna tingofotokoza pang’ono za bukuli.

Bukuli kwenikweni talilemba kuti lithandize ana. Koma ngakhale zili choncho, ndi lothandizanso kwa akuluakulu amene akufuna kulidziwa bwino Baibulo. Popeza Baibulo ndi buku la aliyense, kuphunzira nkhani za m’bukuli kungatithandize kuti tizikhala osangalala.

Pogwiritsa ntchito nkhani za m’Baibulo, bukuli likufotokoza mbiri ya anthu kungoyambira pamene anthuwo analengedwa. Tayesetsa kufotokoza nkhanizi m’njira yosavuta kumva komanso motsatira nthawi imene zinthuzo zinachitika.

Koma sikuti bukuli likungofotokoza nkhani za m’Baibulo. Talemba nkhanizi komanso kukonza zithunzi zake m’njira yoti munthu akamawerenga azikhala ngati akuona zimene zinkachitika komanso kumva mmene anthuwo ankamvera.

Bukuli litithandiza kuona kuti Baibulo limafotokoza za anthu amene anamvera Yehova ndi amene sanamumvere. Ndipo litithandiza kuona zimene tingaphunzire kwa anthuwo. (Aroma 15:4; 1 Akorinto 10:6) Bukuli lili ndi zigawo 14. Kumayambiriro kwa chigawo chilichonse kuli mawu ofotokoza mwachidule zina zimene tingaphunzire m’chigawocho.

Ngati ndinu makolo mungawerenge ndi ana anu mutu uliwonse n’kukambirana zithunzi zake. Kenako mungawerengenso limodzi mavesi a m’Baibulo pamene pachokera nkhaniyo. Thandizani anawo kuona kugwirizana pakati pa zimene mwawerenga m’Baibulo ndi zimene mwaphunzira m’nkhaniyo. Njira imeneyi ingathandizenso ngati mukukambirana ndi munthu wamkulu amene akufuna kulidziwa bwino Baibulo.

Sitikukayikira kuti bukuli lithandiza ana ndi akulu omwe kuti aphunzire mfundo za m’Mawu a Mulungu n’kumazigwiritsa ntchito pa moyo wawo. Izi zingathandize kuti nawonso akhale m’banja la Mulungu n’kumamulambira.

Ndife abale anu,

Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena