Mawu Oyamba Gawo 9
Chigawochi chikufotokoza za achinyamata, aneneri komanso mafumu amene anasonyeza kuti ankakhulupirira kwambiri Yehova. Ku Siriya kunali kamtsikana kena ka ku Isiraeli komwe kankakhulupirira kuti mneneri wa Yehova angathe kuchiritsa Namani. Mneneri Elisa ankakhulupirira kuti Yehova angamupulumutse kwa adani ake. Mkulu wa Ansembe dzina lake Yehoyada anaika moyo wake pangozi kuti apulumutse Yehoasi amene agogo ake a Ataliya ankafuna kumupha. Mfumu Hezekiya inkakhulupirira kuti Yehova apulumutsa Yerusalemu ndipo sanagonjere zimene Asuri ankafuna. Mfumu Yosiya inachotsa mafano, kumanganso kachisi n’kuthandiza anthu kuti ayambirenso kulambira koona.