NYIMBO 5
Ntchito Zodabwitsa za Mulungu
Losindikizidwa
1. M’lungu mumandidziwa bwino
Ndikagona kaya ndikadzuka.
Mumafufuza maganizo anga.
Mumadziwanso zimene
Ndimachita.
Munandiona ndili m’mimba,
Munaonanso mafupa anga.
Munapanga ziwalo zanga zonse.
M’lungu wamphamvu
Ndizikutamandani.
Nzeru zanu Mulungu n’zodabwitsa,
Ndikudziwa ndithu zimenezi.
Ngakhale nditabisidwa ndi mdima
Mzimu wanu udzandipezabe.
Kodi ndingabisale kuti
Komwe inu simungandione,
Kumanda kodi kapena kumwamba?
Palibe malo
Omwe ndingabisale.
(Onaninso Sal. 66:3; 94:19; Yer. 17:10.)