NYIMBO 76
Kodi Mumamva Bwanji?
1. Kodi m’mamva bwanji
Mukasonyeza khama
Polalikira anthu
Ndi kuwaphunzitsa?
Mukamayesetsa
M’lungu adzadalitsa.
Mudzathandiza anthu
Kudziwa Mulungu.
(KOLASI)
Timasangalala ndithu
Kupereka mtima wathu,
Choncho timutumikire
Tsiku lililonse.
2. Kodi m’mamva bwanji
Mukadziwatu kuti
Mwawafika pamtima
Akamva uthenga?
Ena amakana,
Ena amatitsutsa.
Koma timanyadira
Tikalalikira.
(KOLASI)
Timasangalala ndithu
Kupereka mtima wathu,
Choncho timutumikire
Tsiku lililonse.
3. Kodi m’mamva bwanji
Pokumbukira kuti
Mwa chikondi Yehova
Amatsogolera?
Timalalikira,
Timaphunzitsa anthu
Akhale ndi tsogolo,
Adzapeze moyo.
(KOLASI)
Timasangalala ndithu
Kupereka mtima wathu,
Choncho timutumikire
Tsiku lililonse.
(Onaninso Mac. 13:48; 1 Ates. 2:4; 1 Tim. 1:11.)