Lachisanu
“Nthawi zonse kondwerani mwa Ambuye. Ndibwerezanso, Kondwerani”—Afilipi 4:4
M’MAWA
9:20 Kuonera Vidiyo ya Nyimbo
9:30 Nyimbo Na. 111 ndi Pemphero
9:40 NKHANI YA TCHEYAMANI: N’chifukwa Chiyani Yehova ndi “Mulungu Wachimwemwe”? (1 Timoteyo 1:11)
10:15 NKHANI YOSIYIRANA: Zimene Zimatithandiza Kukhala Osangalala
• Moyo Wosalira Zambiri (Mlaliki 5:12)
• Chikumbumtima Chabwino (Salimo 19:8)
• Kuona Ntchito Moyenera (Mlaliki 4:6; 1 Akorinto 15:58)
• Anzathu Abwino (Miyambo 18:24; 19:4, 6, 7)
11:05 Nyimbo Na. 89 ndi Zilengezo
11:15 KUWERENGA BAIBULO MWASEWERO: “Yehova Anawachititsa Kusangalala” (Ezara 1:1– 6:22; Hagai 1:2-11; 2:3-9; Zekariya 1:12-16; 2:7-9; 3:1, 2; 4:6, 7)
11:45 Tizisangalala ndi Zimene Yehova Amachita Populumutsa Anthu Ake (Salimo 9:14; 34:19; 67:1, 2; Yesaya 12:2)
12:15 Nyimbo Na. 148 ndi Kupuma
MASANA
1:30 Kuonera Vidiyo ya Nyimbo
1:40 Nyimbo Na. 131
1:45 NKHANI YOSIYIRANA: Muzisangalala M’banja Mwanu
• Amuna, Muzisangalala ndi Mkazi Wanu (Miyambo 5:18, 19; 1 Petulo 3:7)
• Akazi, Muzisangalala ndi Mwamuna Wanu (Miyambo 14:1)
• Makolo, Muzisangalala ndi Ana Anu (Miyambo 23:24, 25)
• Ananu, Muzisangalala ndi Makolo Anu (Miyambo 23:22)
2:50 Nyimbo Na. 135 ndi Zilengezo
3:00 NKHANI YOSIYIRANA: Chilengedwe Chimasonyeza Kuti Yehova Amafuna Tizisangalala
• Maluwa Okongola (Salimo 111:2; Mateyu 6:28-30)
• Chakudya Chokoma (Mlaliki 3:12, 13; Mateyu 4:4)
• Mitundu Yokongola ya Zinthu (Salimo 94:9)
• Thupi Lathu Logometsa (Machitidwe 17:28; Aefeso 4:16)
• Kaphokoso Kosangalatsa (Miyambo 20:12; Yesaya 30:21)
• Nyama Zochititsa Chidwi (Genesis 1:26)
4:00 Anthu “Olimbikitsa Mtendere Amasangalala” (Miyambo 12:20; Yakobo 3:13-18; 1 Petulo 3:10, 11)
4:20 Kukhala pa Ubwenzi Wolimba ndi Yehova Kumachititsa Kuti Munthu Azisangalala Kwambiri (Salimo 25:14; Habakuku 3:17, 18)
4:55 Nyimbo Na. 28 ndi Pemphero Lomaliza