Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lmd phunziro 6
  • Kulimba Mtima

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulimba Mtima
  • Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zomwe Yesu Anachita
  • Zomwe Tikuphunzira kwa Yesu
  • Zomwe Mungachite Potsanzira Yesu
  • Tsanzirani Yesu mwa Kulalikira Molimba Mtima
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Kodi Mumalalikira Molimba Mtima?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
  • ‘Lankhulani Mawu a Mulungu Molimba Mtima’
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Pitirizani Kulankhula Mawu a Mulungu Molimbika Mtima
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
Onani Zambiri
Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa
lmd phunziro 6

ULENDO WOYAMBA

Yesu akuuza Zakeyu kuti atsike mumtengo ndipo anthu ena akuyang’ana modabwa.

Luka 19:1-7

PHUNZIRO 6

Kulimba Mtima

Mfundo yaikulu: “Tinalimba mtima mothandizidwa ndi Mulungu wathu kuti tikuuzeni uthenga wabwino wa Mulungu.”​—1 Ates. 2:2.

Zomwe Yesu Anachita

Yesu akuuza Zakeyu kuti atsike mumtengo ndipo anthu ena akuyang’ana modabwa.

VIDIYO: Yesu Analalikira Zakeyu

1. Onerani VIDIYO, kapena werengani Luka 19:1-7. Kenako kambiranani mafunso otsatirawa:

  1. Kodi mwina n’chiyani chinkachititsa anthu ena kuti azipewa Zakeyu?

  2. Ngakhale zinali choncho, n’chiyani chinachititsa Yesu kuti amuuze uthenga wabwino?

Zomwe Tikuphunzira kwa Yesu

2. Tiyenera kukhala olimba mtima kuti tilalikire uthenga wa Ufumu kwa aliyense.

Zomwe Mungachite Potsanzira Yesu

3. Muzidalira Yehova. Mzimu wa Mulungu unamupatsa Yesu mphamvu kuti alalikire. Ifenso ungatipatse mphamvu. (Mat. 10:19, 20; Luka 4:18) Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kukhala olimba mtima kuti mukwanitse kulalikira anthu omwe mukuchita nawo mantha.​—Mac. 4:29.

4. Musamaweruze anthu. Tingamazengereze kulalikira anthu ena chifukwa cha maonekedwe awo, chuma chawo, mmene amakhalira kapena chifukwa cha zomwe amakhulupirira. Komabe muzikumbukira kuti:

  1. Yehova komanso Yesu yekha, ndi omwe amaona za mumtima mwa munthu.

  2. Musamaganize kuti Yehova sangamuchitire chifundo.

5. Muzilimba mtima komanso kuchita zinthu mosamala. (Mat. 10:16) Musamakangane ndi anthu. Ngati munthuyo sakufuna kumvetsera uthenga wabwino kapenanso ngati mukuona kuti moyo wanu uli pangozi, chokanipo mwaulemu.​—Miy 17:14.

ONANINSO MALEMBA AWA

Mac. 4:31; Aef. 6:​19, 20; 2 Tim. 1:7

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena