Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wcg mutu 2 tsamba 20-tsamba 23
  • Anatsutsa Dziko

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anatsutsa Dziko
  • Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zoti Mufufuze
  • Zomwe Tikuphunzirapo
  • Ganizirani Mfundo Yaikulu
  • Phunzirani Zambiri
  • “Anayenda Ndi Mulungu Woona”
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
  • “Nowa Anayenda ndi Mulungu Woona”
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Anapulumutsidwa “Pamodzi ndi Anthu Ena 7”
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Nowa Akhoma Chingalawa
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
Onani Zambiri
Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
wcg mutu 2 tsamba 20-tsamba 23

2 NOWA

Anatsutsa Dziko

Losindikizidwa
Losindikizidwa

PATAPITA nthawi Inoki atamwalira, angelo ena anapandukira Mulungu. Angelowo anayamba kusilira akazi padziko lapansi, choncho anadzipangira matupi ngati a anthu n’kudzakwatira akazi alionse omwe anafuna. Ana omwe anabereka ankadziwika kuti Anefili. Iwo anali achiwawa, ankhanza komanso amatupi akuluakulu ndiponso amphamvu kwambiri. Potengera zochita zawozi, anthu anayamba kuchita zinthu zoipa ndipo Mulungu anaona kuti anthu padziko lapansi aipa kwambiri. Koma Nowa yemwe anali mdzukulu wa Inoki, anali wosiyana kwambiri ndi anthu ena onsewo.

Nowa anali munthu wolungama ngati Inoki. Ndipo Baibulo limati: “Yehova ankasangalala ndi Nowa.” Patapita nthawi anakwatira ndipo iye ndi mkazi wake anaphunzitsa ana awo aamuna atatu kuti nawonso azimvera Yehova. Zimenezi zinachititsa kuti banja lawo lizichita zinthu mosiyana kwambiri ndi anthu ena onse.

Tsiku lina, Yehova anauza Nowa kuti waganiza zowononga anthu onse oipa padziko lapansi. Koma anamupatsanso chiyembekezo pomuuza kuti akhome chingalawa chachikulu kuti anthu ena adzapulumukiremo. Nowa anali asanaonepo Chigumula cha dziko lonse ngati mmene Yehova anamuuzira. Komanso iye anali asanapangepo chinthu chachikulu choncho. Nowa anakhulupirira lonjezo la Yehova ndipo anayamba kupanga chingalawacho.

Nowa ndi banja lake anakumana ndi adani oopsa omwe ankadana ndi uthenga komanso ntchito yawo

Nowa ndi banja lake ankafunika kulimba mtima kuti agwire ntchitoyi. N’kutheka kuti anthu ankawatsutsa komanso kuwanyoza. Kuwonjezera pamenepo, angelo oipa aja anali adani oopsa kwambiri ndiponso ana awo ankachitira anthu nkhanza. Koma Nowa, mkazi wake, ana awo aamuna atatu ndi akazi awo, sanafooke ndipo anapitiriza kugwira ntchito. Tsiku ndi tsiku, kwa zaka pafupifupi 50, anthu 8 amenewa anagwira ntchito yokhoma chingalawa.

Nowa ndi ana ake aamuna awiri ndi azikazi awo, akukoka ngolo yodzaza ndi katundu. Pomwe akudutsa, anthu akuwaseka monyoza. Mbali ina ya chingalawa yomwe yakhomedwa ikuonekera chapatali.

Pa nthawiyi, Nowa ankagwiranso ntchito ina. Baibulo limati “ankalalikira za chilungamo cha Mulungu.” Monga mutu wa banja, ankatsogolera banja lake pochenjeza anthu za tsoka lomwe linkabwera. Koma palibe yemwe anamvetsera. Zikuoneka kuti ngakhalenso ambiri mwa achibale ake ananyalanyaza. Anthu sanafune kusiya kuchita zoipa. Nowa anali wosiyana kwambiri ndi anthu amunthawi yake. N’zosadabwitsa kuti Baibulo limanena za Nowa kuti: “Chifukwa cha chikhulupiriro, anatsutsa dziko.”

Pamapeto pake ntchito yokhoma chingalawa ija inatha. Tsopano Nowa ndi banja lake anafunika kusonkhanitsa chakudya ndi madzi zoti iwowo ndi nyama zomwe akanalowa nazo m’chingalawa agwiritse ntchito. Patapita nthawi yochepa, panachitika zinthu zochititsa chidwi. Nyama za mitundu yonse, zazimuna ndi zazikazi zomwe, zinayamba kupita kuchingalawa. Kenako nyama zija “zinalowa ziwiriziwiri mʼchingalawa mmene munali Nowa.”

Mulungu anali atauza kale Nowa kuti alowe ndi banja lake m’chingalawa chija chifukwa kunali kutatsala masiku 7 kuti mvula iyambe kugwa. Tangoganizirani mmene banjali linatanganidwira ndi kulowetsa m’chingalawa zinthu zomalizira zomwe akanafunikira. N’kutheka kuti pa nthawiyi anthu ankawaseka kwambiri. Koma atalowa komanso kulowetsa chilichonse, Yehova anatseka chitseko. Mwina izi zitangochitika, onyoza aja anasowa chonena. Kenako chimvula champhamvu chinayamba kugwa ndipo madzi anayamba kusefukira. Madziwo anapitiriza kusefukira kwa masiku 40 mpaka mapiri anamira. Apa Yehova anawononga anthu onse oipa.

Nowa ndi banja lake anakhala otetezeka m’chingalawa muja momwe anakhalamo kwanthawi yoposa chaka. Pa nthawiyi, madzi a Chigumula anayamba kuphwa pang’onopang’ono. Pomaliza, chingalawa chija chinakaima paphiri, kenako Yehova anauza Nowa kuti atuluke. Pomwe banjali linkatuluka m’chingalawa, linatamanda Yehova pomuthokoza kuti wawapulumutsa. Yehova analonjeza kuti sadzabweretsanso chigumula chamadzi ndipo kumwamba kunaoneka utawaleza ngati chizindikiro chake.

Tonse amene tili ndi moyo masiku ano, tinachokera m’banja la Nowa. Choncho n’zomveka kuti tiziyamikira kuti anthuwa anakhala olimba mtima kuchita zinthu zoyenera ngakhale kuti ankakhala pakati pa anthu oipa.

Werengani nkhaniyi m’Baibulo:

  • Genesis 6:1 mpaka 8:22; 9:​8-19

  • Aheberi 11:7

  • 2 Petulo 2:5

Funso lokambirana:

Kodi Nowa anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?

Zoti Mufufuze

  1. 1. Kodi zinthu zinali bwanji padzikoli Chigumula chisanachitike? (w02 3/1 5 ¶3–6 ¶4)

  2. 2. Kodi ndi liti pomwe Nowa anauzidwa kuti akhome chingalawa? Nanga ndi liti pomwe anadziwa nthawi yeniyeni yomwe Chigumula chidzayambe? (w12 4/15 23 ¶5-8)

  3. 3. Tingakhulupirire bwanji kuti Chigumula chinachitikadi? (ijwbq nkhani 156 ¶2-5, bokosi) A

    Anthu 8 ali m’boti ndipo chinsomba chachikulu chikuwatsogolera kumalo otetezeka.

    Historic Collection/Alamy Stock Photo

    Chithunzi A: Mhindu wina akufotokoza nthano ya munthu wina amene anakhoma boti kuti apulumukiremo chigumula. Pambuyo pake, anapereka nsembe ndipo anakhala kholo la anthu onse.

  4. 4. Kodi n’chiyani chinachitika patatha zaka zopitirira 100 Chigumula chitachitika? Nanga n’kutheka kuti zinakhudza bwanji Nowa yemwe pa nthawiyi anali wokalamba? (it “Nowa” Na. 1 ¶12-wcgr) B

    Pafupi ndi nsanja ya Babeli, azibambo awiri akuyesetsa kulankhulana koma sakumvana.

    Chithunzi B

Zomwe Tikuphunzirapo

  • Kodi masiku ano akufanana bwanji ndi masiku a Nowa? (Mat. 24:​36-39)

  • Kodi chitsanzo cha Nowa chikutiphunzitsa chiyani pa nkhani ya kufunika kokhala . . .

    • wadongosolo? C

      Mlongo akuwerenga lemba la tsiku kwinaku akudya chakudya cham’mawa. Alinso ndi kabuku kolembamo zomwe akufuna kuchita pa tsikulo ndipo kalendala ikuonekera pakhoma.

      Chithunzi C

    • wakhama? D

      Mlongo yemwe uja ali kuntchito ya zomangamanga, akudula thabwa ndi mashini amagetsi.

      Chithunzi D

    • woleza mtima? E

      Mlongo uja ali ndi mnzake, akuchita ulaliki wapashelefu ndipo anthu akudutsa.

      Chithunzi E

  • Kodi mungatsanzire bwanji Nowa pa nkhani yokhala wolimba mtima?

Ganizirani Mfundo Yaikulu

  • Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?

  • Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?

  • Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani Nowa akadzaukitsidwa?

Phunzirani Zambiri

Onani mmene mutu wina wabanja ukuchitira khama potsanzira Nowa.

Muzitsanzira Anthu Achikhulupiro, Osati Opanda Chikhulupiriro—Nowa, Osati Anthu Ena a M’nthawi Yake (2:57)

Thandizani ana anu kuphunzirapo kanthu pa nkhani ya Nowa.

“Nowa Ankakhulupirira Kwambiri Mulungu” (ijwis nkhani 18)

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena