40 NEHEMIYA
Anamanganso Mpanda
NEHEMIYA ankakhala ku Perisiya mumzinda wa Susani, koma maganizo ake anali ku Yerusalemu. Iye ankakonda kwambiri mzinda wa Yerusalemu chifukwa n’kumene kunali kachisi wa Yehova. Anthu a Mulungu anali ataloledwa kubwerera kumeneko atakhala ku ukapolo kwa zaka zambiri. Koma kulambira koona kunali kusanayambe kuyenda bwino. Mpanda wa mzindawu unali utagwa. Pa nthawiyo, anthu ankaona kuti mzinda wopanda mpanda ndi wosatetezeka, choncho anthu sankakonda kukhala mumzinda woterewo.
Nehemiya anali ndi udindo waukulu ku Perisiya mu ulamuliro wa Mfumu Aritasasita. Komanso anali mtumiki wokhulupirika wa Yehova. Tsiku lina m’bale wake wa Nehemiya anabwera ndi uthenga wakuti anthu ku Yerusalemu anali “pamavuto aakulu.” Mpanda wa mzindawo unali udakali wakugwa komanso Ayuda ‘ankanyozedwa.’
Nehemiya anakhumudwa kwambiri ndi zimenezi. Iye analemba kuti: “Ndinakhala pansi n’kuyamba kulira ndipo ndinalira kwa masiku angapo.” Anapemphera kwa Yehova ndipo anamuchonderera kuti akumbukire anthu ake komanso awathandize. Kenako pamene ankaperekera vinyo kwa Aritasasita, mfumuyi inamufunsa chifukwa chake nkhope yake inkaoneka yachisoni. Nehemiya anachita mantha, komabe anayankha zimene mfumuyo inafunsa. Anauza mfumuyo mavuto amene anali ku Yerusalemu. Ndiyeno inamufunsa zimene ankafuna. Nehemiya analemba kuti: “Nthawi yomweyo ndinapemphera kwa Mulungu wakumwamba.” Kenako anauza mfumu yamphamvuyo kuti akupempha kuti asiye ntchito yake kwakanthawi kuti apite ku Yerusalemu kukathandiza kumanganso mpanda wa Yerusalemu ndi mageti ake. Mfumuyo inalola kuti Nehemiya achite zonse zimene anapemphazo.
Nehemiya anauyamba ulendo wa ku Yerusalemu womwe unali wautali komanso wotopetsa. Atafika kumeneko, anayenda usiku kuzungulira mpanda kuti aone mmene ulili. Kenako anapeza anthu n’kuwalimbikitsa kuti agwire nawo ntchito yomangayi. Iye anapereka chitsanzo chabwino pomagwira nawo ntchitoyi. Anthuwo anagwiradi ntchitoyi ndipo ena mwa iwo anali achuma, otchuka, osula golide komanso akalonga. Ndipo mmodzi wa akalongawa ankagwira ntchitoyi limodzi ndi ana ake aakazi.
Panali anthu ambiri omwe ankadana ndi Ayuda ndipo sankafuna kuti mzinda wa Yerusalemu ukhale wotetezeka komanso wamphamvu. Poyamba ankawanyoza komanso kuwaseka. Moti munthu wina ananena kuti ngakhale nkhandwe ikanatha kugwetsa mpanda umene Nehemiya ndi anthu ake ankamanga. Koma Nehemiya anangozinyalanyaza ndipo analimbikitsa anthuwo kuti apitirize kugwira ntchitoyo.
Ngakhale kuti adani a Nehemiya ankamunyoza komanso kumuopseza, iye anapitiriza kumanga mpanda wa Yerusalemu
Adani awowo anapitirizabe kuwatsutsa. Atamanga hafu ya mpandawo, adaniwo anakonza zoti abwere kudzawaukira kuchokera kumbali zonse. Nehemiya anachita zonse zimene akanatha kuti ateteze mzindawo. Adaniwo ataona zimene Nehemiya anachitazi, anaganiza zoti asaukirenso Yerusalemu pogwiritsa ntchito zida. Kuyambira nthawi imeneyo, Nehemiya ndi hafu ya ogwira ntchitowo ankalondera atatenga zida ndipo hafu inayo inkagwira ntchito yomangayo. Koma adaniwo sanasiyire pomwepo.
Njira ina imene anagwiritsa ntchito inali yoopseza Nehemiya kuti aphedwa. Iwo anachita zimenezi n’cholinga choti iye achite mantha n’kukabisala m’kachisi wopatulika wa Yehova. Koma Nehemiya anakana chifukwa akanachita zimenezi akaphwanya lamulo la Mulungu. Iye anati: “Kodi mwamuna ngati ine ndingathawe?” Nehemiya anapitiriza kugwira ntchitoyo chifukwa ankadziwa kuti Ayuda akuchita zimene Yehova ankafuna ndipo awathandiza. Yehova anawathandizadi. Moti ntchitoyo inatha patangodutsa masiku 52 okha. Anthu amene ankanyoza komanso kutsutsa aja anachita manyazi.
Nehemiya ankafunikanso kulimba mtima kuti athandize Ayuda anzake. Ankafunika kuwatsogolera kuti azitumikira Yehova. Mwachitsanzo, pamene anthu olemera ankapondereza osauka powapatsa ngongole n’kumafuna chiwongola dzanja chachikulu, Nehemiya analimba mtima n’kuwadzudzula. Kenako atamva kuti Ayuda ena sakumvera lamulo la Yehova loti asamakwatire akazi amitundu ina, anawadzudzulanso mwamphamvu n’kuwauza kuti zimenezo zinali zosemphana ndi lamulo la Yehova.
Pa nthawi ina, pamene anthuwo ankamva chisoni chifukwa cha zimene analakwitsa komanso machimo awo, Nehemiya anawauza mfundo yofunika kwambiri yakuti: “Chimwemwe chimene Yehova amapereka ndi malo anu achitetezo.” Nehemiya ankadziwa kuti kutumikira Mulungu wachimwemwe kumapangitsa munthu kukhala wokhutira kwambiri. Palibe mpanda kapena malo alionse amene angapereke chitetezo kuposa chitetezo chochokera kwa Yehova. Masiku anonso chitetezo chimenechi chimatithandiza kukhala olimba mtima.
Werengani nkhaniyi m’Baibulo:
Funso lokambirana:
Kodi Nehemiya anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?
Zoti Mufufuze
1. Kodi ndi zinthu ziti zimene Nehemiya ankachita pa ntchito yake yoperekera zakumwa kwa mfumu? (w10 7/1 9 ¶5-7) A
National Museum of Iran, Tehran, Iran/Bridgeman Images
Chithunzi A: Chithunzi chapakhoma cha ku Perisiya chosonyeza woperekera zakumwa kwa Dariyo Wamkulu, yemwe anali agogo ake a Aritasasita
2. Kodi ana aakazi a Salumu ankasiyana bwanji ndi Atekowa otchuka? (Neh. 3:5, 12; w19.10 23 ¶11)
3. Kodi zinkatheka bwanji kuti anthu omwe ankanyamula katundu ‘azigwira ntchito ndi dzanja limodzi, dzanja linalo atanyamula chida’? (Neh. 4:17, 18; w06 2/1 9 ¶1) B
Chithunzi B
4. N’chifukwa chiyani Nehemiya anada nkhawa kuti mwina ana ena a Ayuda sangathe kulankhula Chiheberi? (Neh. 13:23-27; w16.10 14 ¶4)
Zomwe Tikuphunzirapo
Kodi akulu angatsanzire bwanji Nehemiya pa nkhani ya . . .
kudalira Yehova? (Neh. 1:4-11; 4:14; 13:1-3)
kufunitsitsa kugwira ntchito ndi abale? (Neh. 4:15, 21-23)
kumvetsera? (Neh. 5:1-7) C
Chithunzi C
Kodi chitsanzo cha Nehemiya chikutiphunzitsa chiyani pa nkhani ya madalitso amene timapeza tikalolera kusiya moyo wofewa n’cholinga choti tizichita zambiri potumikira Yehova?
Kodi mungatsanzire kulimba mtima kwa Nehemiya m’njira zinanso ziti?
Ganizirani Mfundo Yaikulu
Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?
Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?
Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani Nehemiya akadzaukitsidwa?
Phunzirani Zambiri
Kodi nkhani ya Nehemiya ikusonyeza bwanji kuti pemphero limathandiza?
“Mulungu Anayankha Pemphero Lake” (Nkhani zapawebusaiti, “Zoti Muchite Pophunzira Baibulo”)
Muvidiyo yotsatirayi, onani zimene Nehemiya anachita molimba mtima pamene adani ankamutsutsa.