Kuchita Ulauli—Kukalipobe
”WINA angaganizire, mu tsiku iri lakufala kwa kumvetsetsa ndi maphunziro, kuti sichingakhale choyenera kulemekeza zikhulupiriro zozikidwa pa matsenga ndi kukhulupirira malaulo.” Iyi inali mbali ya sitetimenti yosainidwa ndi asayansi otchuka 186, kuphatikizapo opeza mphoto za otchuka a pachaka 18. Kodi iwo anali kulankhula za chiyani? Kupenda nyenyezi, njira yofala ya ulauli kugwiritsira ntchito nyenyezi kumene malinga ndi iwo, “kumalowerera sosaite ya makono.” Kodi inu mwaumwini mumakhulupirira mu mitundu ina ya kuchita ulauli? Kapena mwina mwake muli okaikira, kapena otsutsa kwa ntu wagalu, monga asayansi otchuka awa? Kawonedwe kanu ka nkhani iyi kali kofunika kwambiri. Tiyeni tiwone nchifukwa ninji.
Kachitidwe kameneka kali kofala kwambiri. Malinga ndi kunena kwa mlankhuli wa msonkhano wa alauli mu Paris, “[anthu] Achifrench 4 miliyoni amapita ku malo a mizimu yakufa miyezi 6 iri yonse.” Mu United States muli chiyerekezo cha openda nyenyezi akanthawi 175, 000 ndi anthaŵi zonse 10, 000. Iwo alinso ambiri mu Great Britain, kumene ali ndi sukulu zawo zawo. Ndipo magazini ya Chifrench Ça m’interesse (Chiri chosangalatsa) ikuchitira ndemanga: “Kulikonse, kuphatikizapo mu masosaite otukuka kwambiri, timakumana ndi ziwerengero zofananazo. Malo a mizimu yakufa akupita patsogolo kumapeto a zana lathu.”
Ndani Amawafunsa Iwo—Ndipo Chifukwa ninji?
Ena angakhulupirire kuti ali kokha awo osaphunzira kwenikweni, anthu apansi amene ali osangalatsidwa mu “sayansi” ya maula, ya imene kupenda nyenyezi mwina mwake kuli kofala kwambiri. Koma Madame Soleil, wopenda nyenyezi wotchuka kwambiri Wachifrench, akuvumbulutsa: “Iwo onse amabwera kwa ine, kaya ndi akumanja kapena kumanzere, andale akawonekedwe konse ka zinthu ndi mafumu akunja a boma. Ndimakhalanso ndi ansembe ndi akomyunisiti.” Mchigwirizano ndi chimenechi, pamene wamatsenga Frédéric Dieudonné anafa, nkhani inawoneka mu Le Figaro, nyuzipepala yosamalitsa ya tsiku ndi tsiku ya Chifrench, imakumbukira kuti iye anakopa “gulu lalikulu la umunthu wa Chiparisiani, aminisitala, nduna za boma, olemba ndi ochita zitsudzo.”
Otchova njuga amafunsira openda nyenyezi kuti adziwe ndimotani mmene angaikire khokhera zawo. Anthu amabizinesi amapita kwa iwo kukapeza ndimotani mmene angasungire ndalama zawo. Openda nyenyezi angakhale ofunitsitsa kukuuzani ndi liti pamene munganyamuke paulendo kapena chimene mungaphike. Ndipo kuchita ulauli kwalowa mminda inanso. Madipatimenti a polisi mu maiko osiyanasiyana amapita kwa alauli kaamba ka kufunafuna aupandu kapena anthu osowa. Ndipo malinga ndi kunena kwa Le Figaro Magazine ya Chifrench ya mlungu ndi mlungu, “ofesi ya nkhondo ya mu U. S. A. imalemba ntchito anthu 34 okhala ndi mphatso yoona za mtsogolo kuwapatsa iwo chidziwitso ponena za zimene zikuchitika mmalo ankhondo a mwamtseri a mu U. S. S. R.” Magazini imodzimodziyo ikusimba za Charles Rose wa mnyumba ya malamulo ya ku U. S. kukhala akunena kuti a Russia nawonso amapita ku mphamvu za mizimu ya anthu akufa.
Kodi nchifukwa ninji kupenda nyenyezi kudakalipobe? Kodi iko kuli sewero lopanda chiwopsezo kapena kungotaya chabe nthawi? Kodi iri njira yabwino koposa yakupezera chimene mtsogolo m’masunga—kapena kodi pali njira yabwinoko? Tiyeni tiwone ngati tingapeze mayankho kumafunso ofunika kwambiri amenewa.