Akazi M’malo Antchito—Ziyeso ndi Zitokoso
“AKAZI alowa m’mphamvu ya ntchito ya chibadidwe mu chiwerengero chosaŵerengeka mkati mwa zaka makumi atatu apita.” Likutero ripoti la mafufuzidwe a gulu la Worldwatch Institute. “Ponse pawiri m’maiko olemera ndi osauka,” ripotilo likupitiriza, “kuperewera kwa ndalama kumalimbikitsa akazi kugwira ntchito kaamba ka malipiro.” Kapena monga mmene mkazi m’modzi wa ku Nigeria akuikira icho: “Chitsenderezo cha chuma chiri chotero kotero kuti ndiyenera kungopita kunja ndi kugwira ntchito.”
Monga “mkazi wangwiro” wanthawi ya Baibulo, akazi ambiri ali achimwemwe kupereka chogawira choyenerera mwa chuma ku ubwino wa mabanja awo. (Miyambo 31:10, 16, 24) Ndipo ena amapeza kukhala ndi ntchito kukhala chitokoso ndi chikwaniritso. Koma pamene ntchito ya kuthupi iri ndi mapindu ake, ingakhalenso ndi zobweza m’mbuyo zake.
Mwachitsanzo, mkazi m’modzi yemwe ndi manijala wa sitolo akunena kuti: “Ndimakonda ntchito yanga. Mkulu wanga wa pantchito ali wabwino, ofesi yanga iri yokongola. Koma ndimadana nayo pamene ntchitoyo itenga yambiri ya nthawi yanga yoposa imene ndingaipatse iwo, chifukwa pambuyo pake ndiri ndi ntchito ina imene iri kundidikira kunyumba—monga mkazi ndi mayi.” Komabe, akazi ambiri amasamalira kaamba ka ntchito, nyumba, ndi banja bwino lomwe, ndipo kaamba ka icho iwo ayenera kuyamikiridwa.a
Ntchito zolembedwa, angakhale kuli tero, zimaika akazi pamavuto apadera ku malo antchito. Kwa ambiri, chitokoso chiri kukhala ndi kawonedwe kolinganizika pamene akakamizidwa kugwira ntchito m’mkhalidwe wodzazidwa ndi mpikisano wochititsa mantha kapena kusagwirizana kokakala. Chikhumbo cha kupita patsogolo, kutsogola, chatsogolera akazi ena kupanga ntchito zawo kukhala chonulirapo chenicheni m’miyoyo yawo.
Nthawi zina malo antchito angakhalenso magwero a zitsenderezo za makhalidwe. Kuvumbulutsidwa ku muyeso wa tsiku ndi tsiku wa nkhani zosayenera iri dandaulo lofala la akazi ogwira ntchito. Choipa koposerapo, ena amadzipeza iwo eni kukhala minkhole ya kuipsidwa mwa kugonedwa kosagwira mtima. “Pamene ndiyamba kugwira ntchito,” amakumbukira choncho mkazi Wachikristu, “ndinali mtsikana yekha mu ofesimo. Amunawo anapanga ndemanga zolingalira, ndipo chinalidi chovuta kaamba ka ine.”
Mavuto oterowo alidi chodetsa nkhawa chenicheni kwa akazi omwe ayenera kukumanizana nawo tsiku ndi tsiku, makamaka awo amene amakhumba kusunga kaimidwe ka Chikristu. Mwachimwemwe, pali magwero athandizo lenileni kaamba ka iwo.
[Mawu a M’munsi]
a Onani nkhani yokambitsiridwa “Awiri Ogwira Ntchito—Kuyang’anizana ndi Zitokoso,” m’kope la February 8, 1985, kope ya magazini ya Galamukani! (m’Chingelezi).