Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g92 7/8 tsamba 9-11
  • Akazi—Kodi Amapatsidwa Ulemu Pantchito?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Akazi—Kodi Amapatsidwa Ulemu Pantchito?
  • Galamukani!—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mwamuna Wosautsa
  • Akazi ndi Lamulo
  • Kuvuta Akazi—Vuto Lapadziko Lonse
    Galamukani!—1996
  • Akazi—Kodi Amapatsidwa Ulemu Panyumba?
    Galamukani!—1992
  • Kodi Ndingachitenji Ndikamavutitsidwa ndi Amuna Kapena Akazi?
    Galamukani!—2000
  • Akazi—Kodi Amapatsidwa Ulemu Lerolino?
    Galamukani!—1992
Onani Zambiri
Galamukani!—1992
g92 7/8 tsamba 9-11

Akazi—Kodi Amapatsidwa Ulemu Pantchito?

“Kaya akhale mbeta kapena okwatira, amuna ochuluka anawona akazi kukhala monga nyama zosakidwa.”—Jenny, amene kale anali mlembi wamaloya.

“Kuvutitsa akazi m’zakugonana ndi kuwachitira nkhanza m’zipatala kuli koipitsitsa.”—Sarah, nesi wa m’chipatala.

“Ndinali kunyengedwa mosalekeza kuntchito kuti agonane nane.”—Jean, nesi wa m’chipatala.

KODI nkhani zimenezi zimasonyeza mkhalidwe wachilendo, kapena kodi nzofalikira? Mtola nkhani wa Galamukani! anafunsa akazi angapo ogwira ntchito kwazaka zambiri. Kodi iwo anapatsidwa ulemu ndi kulemekezedwa ndi amuna ogwira nawo ntchito? Nazi zina za ndemanga zawo:

Sarah, nesi wa ku New Jersey, U.S.A., wogwira ntchito kwa zaka zisanu ndi zinayi m’zipatala za asirikali mu United States: “Ndikukumbukira pamene ndinkagwira ntchito mu San Antonio, Texas, ndipo panali malo antchito ofunikira munthu mu Dipatimenti Yochiritsira Impso. Ndinafunsa kagulu ka madokotala chimene ndifunikira kuchita kuti ndipeze ntchito imeneyo. Mmodzi wa iwo anandiyankha motyasira nati, ‘Kagone ndi dokotala wamkulu.’ Ndinangoti, ‘Ngati zofunikira zinali zimenezo sindiifuna ntchitoyo.’ Komatu kaŵirikaŵiri ndimo mmene kukwezedwa pantchito ndi kuipeza kumatsimikizidwira. Mkazi ayenera kulolera kwa mkulu wapantchito wachilakolako chakeyo.

“Pachochitika china, ndinkagwira ntchito m’chipinda chodwazikira matenda akayakaya ndikumaika chipangizo choloŵa m’mitsempha kwa wodwala wina pamene dokotala anabwera ndi kundigwiragwira matako. Ndinakwiya ndipo ndinatuluka mwaukali kuloŵa m’chipinda china chapafupi. Anandilondola m’menemo akumanena mawu onyanya. Ndinam’bwanyula nakagwera m’chithini cha zinyalala! Pamenepo ndinabwereranso kwa wodwala wanga. Kuyambira pomwepo sanayesenso kundivutitsa!”

Miriam, mkazi wokwatira wa ku Igupto amene kale anachita ntchito yaulembi m’Cairo, anafotokoza mkhalidwe wa akazi ogwira ntchito mu Igupto pakati pa Asilamu. “Akazi amavala modekha kwambiri kuposa m’maiko Akumadzulo. Sindinawone kuvutitsa akazi kowagwiragwira kulikonse kapena kofuna kugonana nawo pantchito panga. Koma kuvutitsa akazi kumachitika m’tireni yapansi panthaka m’Cairo kumlingo wakuti tsopano toroko yoyamba imapatsidwa kwa akazi okha.”

Jean, mkazi wachete koma wotsimikiza amene wagwira ntchito yaunesi kwa zaka 20, anati: “Ndinatsatira mchitidwe wankhokera wakusayenda ndi aliyense pantchito. Koma kuvutitsidwa kunalipo kaya ndinali ndi madokotala kapena anesi achimuna. Iwo onse anaganiza kuti anali oposerapo chifukwa chakukhala kwawo amuna. Ngati anesife ‘sitinagwirizane nawo’ pazofuna zawo zakugonana, pamenepo manesi amunawo sakatithandiza pamene tinafunikira chithandizo chakunyamula odwala kuwagoneka pakama ndi zinthu zina zotero.”

Jenny anagwira ntchito monga mlembi wa maloya kwa zaka zisanu ndi ziŵiri. Anafotokoza zimene anawona pogwira ntchito ndi maloya. “Kaya anali mbeta kapena okwatira, amuna ochuluka anawona akazi monga nyama zosakidwa. Kaimidwe kawo kamaganizo kanali kakuti, ‘Monga maloya zonse nzathu, ndipo akazi ali pakati pa mwaŵi wathu.’” Ndipo umboni ukuwonekera kusonyeza kuti ogwira ntchito zapamwamba ena alinso ndi lingaliro lofananalo. Koma kodi mkazi angachitenji kuchepetsa kuvutitsidwa?

Darlene, Mmereka wachikuda amene anagwira ntchito monga mlembi ndi woperekera chakudya wachikazi m’kantini anati: “Zinthu zikhoza kulakwika ngati ulephera kuika malire a kudzisungira. Ngati mwamuna ayamba kukuseleula nawenso nkumabwezera, pamenepo zinthu zikhoza kufika mosavuta posalamulirika. Ndinayenera kufotokoza momvekera bwino kaimidwe kanga panthaŵi zosiyanasiyana. Ndagwiritsira ntchito mawu monga akuti, ‘Ndikanayamikira ngati simukananena ndi ine mawu amenewo.’ Panthaŵi ina ndinati: ‘Monga mkazi wokwatiwa, mawu amene mwanena ngoputa, ndipo sindiganiza kuti mwamuna wanga angakonde kuwamva.’

“Mfundoyo njakuti, ngati mumafuna ulemu, muyenera kuupeza mwakudzisungira. Ndipo sindikuwona mmene mkazi angapezere ulemu ngati ayesa kupikisana ndi amuna m’nthabwala zosayenera ndi kulankhula ndi zofuna zachisembwere. Ngati mulemba malire osawonekera bwino pakati pa kuvomera ndi kukana, pamenepo mwamuna wachisembwereyo adzawawoloka.”

Mwamuna Wosautsa

Connie, amene wagwira ntchito yaunesi kwa zaka 14, anafotokoza mtundu wina wa kuvutitsa kumene kungabuke m’mikhalidwe yambiri. “Ndinali kugwira ntchito ndi dokotala yosintha mabandeji pazilonda monga mwanthaŵi zonse. Ndinatsatira njira zonse zimene ndinaphunzira. Ndimadziŵa zonse ponena za njira yakusamalira mabandeji ndi zilonda kukhala zosadetsedwa, ndi zina zotero. Koma palibe chimene chinali chabwino kwa dokotalayo. Ankandizazira ndi kusuliza chimene ndinachita. Mchitidwe umenewu, wakululuza akazi, ngwofalikira. Amuna ena ali ndi vuto lakudzikweza, ndipo kukuwonekera ngati kuti afunikira kukakamiza ulamuliro wawo pa akazi ogwira nawo ntchito.”

Sarah, wogwidwa mawu papitapo, anapitiriza kusimba chokumana nacho chake motere. “Ndinali kugwira ntchito kukonzekera opareshoni pamene ndinkapenda zizindikiro zofunika za wodwala kuwona ngati zinali bwino. Cholembapo chake cha EKG [electrocardiogram] chinasonyeza kusinthasintha chotero ndinadziŵa kuti sanali mumkhalidwe wabwino wakuti achitidwe opareshoni. Ndinapalamula mwakusonyeza zimenezi kwa dokotalayo. Anakwiya, ndipo yankho lake linali lakuti: ‘Manesi ayenera kusamalira aguthuthu, osati ma EKG.’ Chotero ndinangouza mkulu wa madokotala ogoneka tulo, ndipo anati m’mikhalidwe yoteroyo timu lake silingagwirizane ndi dokotalayo. Ndiyeno dokotalayo anatembenuka ndi kuuza mkazi wa mwamuna wodwalayo kuti ndine ndinachititsa kuti mwamuna wake asachitidwebe opareshoni! M’zochitika zotero mkazi sangapambane. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti mosadziŵa umathupsa thamo la mwamuna.”

Mwachiwonekere, akazi kaŵirikaŵiri amavutitsidwa ndi machitidwe akusapatsidwa ulemu pantchito. Koma kodi kaimidwe kawo nkotani ku lamulo?

Akazi ndi Lamulo

M’maiko ena kwatengera akazi zaka mazana ambiri kuti apeze ngakhale lamulo lolembedwa lakuti ali olingana ndi amuna mwalamulo. Ndipo ngakhale kumene lamulo limati akazi ali olingana ndi amuna, kaŵirikaŵiri pamakhala phompho lalikulu pakati pa mawu olembedwa ndi kuchita.

Bukhu la UN lakuti The World’s Women—1970-1990 limati: “Kusiyana kwakukulu kumeneku [kwa mchitidwe wa boma] kuli m’malamulo amene amatsutsa kuti akazi akhale olingana ndi amuna m’zoyenera zawo zakukhala eni kadziko, kukongola ndalama ndi kuloŵa m’mapangano.” Monga momwe mkazi wina wa ku Uganda ananenera: “Tikupitirizabe kukhala nzika zotsika—inde, zotsika koposa, popeza kuti ana athu aamuna amatiposa. Ngakhale abulu ndi matalakita nthaŵi zina zimasamaliridwa bwino.”

Bukhu la Time-Life lakuti Men and Women limati: “Mu 1920, Kusintha kwa 19 kwa Mpambo wa malamulo wa United States kunatsimikizira akazi ufulu wakuchita voti—nthaŵi yaitali atapeza kale ufulu umenewo kumaiko ambiri a ku Ulaya. Koma kuyenera kuchita voti sikunaperekedwe m’Briteni kufikira 1928 (ndipo m’Japani pambuyo pa Nkhondo Yadziko II).” Kusonyeza kutsutsa chisalungamo cha ndale zadziko pa akazi, mkazi wa ku Briteni womenyera ufulu wakuchita voti kwa akazi, Emily Wilding Davison, anadziponya patsogolo pa kavalo wa Mfumu pampikisano wa akavalo mu 1913 ndipo anaphedwa. Anakhala wofera ufulu wa kulingana pakati pa akazi ndi amuna.

Chenicheni chakuti mpaka posachedwapa mu 1990, Nyumba ya Malamulo ya United States inapereka “Lamulo Loletsa Kuchitira Akazi Chiwawa” chimasonyeza kuti mabungwe amalamulo amene ochuluka ake ali amuna akhala osafulumira kulabadira zosoŵa za akazi.

Malongosoledwe achidule a mmene akazi amachitiridwa padziko lonse lapansi amachititsa kufunsa kuti, Kodi mikhalidweyo idzakhala yosiyana nkomwe? Kodi pafunikiranji kuti mkhalidwewo usinthe? Nkhani ziŵiri zotsatira zidzapenda mafunsoŵa.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 11]

Kodi Ndani Ali Mumkhalidwe Woipirapo?

“Akazi amachita magawo aŵiri mwa atatu antchito zonse zadzikoli. Amatulutsa 60 mpaka 80 peresenti ya chakudya cha Afirika ndi Asiya, 40 peresenti ya chakudya cha ku Latin America. Chikhalirechobe, iwo amalandira gawo limodzi lokha mwa magawo khumi amalipiro apadziko lonse ndipo ali ndi katundu wosakwanira peresenti imodzi ya katundu wapadziko lonse. Iwo ali pakati pa anthu osauka koposa padziko lapansi.”—May You Be the Mother of a Hundred Sons, lolembedwa ndi Elisabeth Bumiller.

“Chenicheni nchakuti asungwana aang’ono samapita kusukulu [m’mbali zina zadziko] chifukwa chakuti kulibe madzi akumwa abwino. . . . Ndawona asungwana osinkhukirapo akukatunga madzi pamtunda wamakilomita makumi aŵiri kapena makumi atatu, kumene amathera tsiku lathunthu akuyenda. Podzafika pamsinkhu wazaka khumi ndi zinayi kapena khumi ndi zisanu, asungwanaŵa . . . sanaloŵe konse sukulu, saphunzire konse chirichonse.”—Jacques-Yves Cousteau, The Unesco Courier, November 1991.

[Chithunzi patsamba 10]

Kuvutitsa akazi sikuyenera kulekereredwa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena