Ripoti la Olengeza Ufumu
“Khalani Oyera Mtima”
CHITSOGOZO CHA MULUNGU kwa Akristu chiri chakuti “osadzifaniziranso ndi zilakolako zakale, pokhala wosadziwa inu; komatu monga iye wakuitanani inu ali woyera mtima, khalaninso oyera mtima mmakhalidwe anu onse; popeza kwalembedwa: ‘Muzikhala oyera mtima, pakuti ine ndine woyera mtima.’” (1 Petro 1:14-16) Khalidwe loyera mtima llmenelo llri umboni wabwino kwambiri kwa ena. (1 Petro 2:12) Kuzungulira padziko lonse lapansi, monga mmene chokumana nacho chotsatirapochi chikusonyezera, anthu ofunitsitsa apanga kusintha koyenerera kubweretsa mikhalidwe yawo mchigwirizano ndi uphungu umenewo.
◻ Mu Ecuador mwamuna anayimitsa phunziro lake la Baibulo pamene Mboni imene inali kuphunzira ndi iye Inachotsedwa mu mpingo kaamba ka khalidwe lachi“ sembwere. Zosowa zake zauzimu zinamutsogoza iye kufunafuna mu zipembedzo zina. lye anakhazikika mu chipembedzo cha Evangelist ndipo anapita patsogolo ku nsonga yakufikira kukhala pasitala wa tchalitchi chake. Komabe, chikumbumtima chake chinali kumuvutitsa, popeza iye anali asanamkwatire mkazi amene anali kukhala naye. Pamene anafunsa mapasitala amatchalitchi ena, iwo anamutsimikizira lye kuti panalibe vuto. Komabe, iye anadziwa kuti chimenechi sichinali chabwino, popeza kuti Mboni imene inaphunzira naye inachotsedwa mu mpingo kaamba ka khalidwe lachisembwere. lye sanamvetsetse ndi chifukwa ninji iye sanadzudzulidwe ndi tchalitchi chake. Pambuyo pake, mnzake wokhala naye wamkaziyo anapeza Mboni za Yehova ndi kuyamba kuphunzira ndi izo. Mwamunayo anayamba kuphunzira limodzi ndi iye. Onse aŵiri akupezeka pa misonkhano tsopano, kupita patsogolo mnzeru yawo ya maprinsipulo a Baibulo, ndipo akutenga masitepi akukwatirana kotero kuti atumikire Yehova mu njira yoyera ndi yovomerezedwa.
◻ Mu chokumana nacho china chochokera ku Ecuador, Mboni ikusimba kuti: “Mu February 1984, mkazi wa mzaka zapakati anafunsa ife kuphunzira naye.” Kodi nchiyani chimene chinafulumiza chifunsiro chimenechi? Mlongo wake wa mkazi ameneyo anali mmodzi wa Mboni za Yehova, ndipo iye anasangalatsidwa kwambiri ndi khalidwe lake labwino. Mkati mwa phunziro la Baibulo lachiwiri, anakhudza mutu wonena za kusuta ndudu, limene linali limodzi la mavuto a mkaziyo. Komabe, pa phunziro lotsatira mlungu wina pambuyo pake iye monyadira analengeza kuti kuyambira pamene anaphunzira kawonedwe ka Baibulo ka kusuta ndudu iye sanakhudze ndudu iri yonsei lye anali ndi vuto lina—nyumba yake inali yodzadza ndi mafano achipembedzo. Koma pamene anawerenga Deutronomo 7:26, pamene pamanena kuti: “Musamalowa nacho chonyansachi m’nyumba mwanu, . . . popeza ndi chinthu choyenera kuwonongeka konse,” iye anapitirira kuwatenthaiwo.
Kuyambira panthawi Imeneyo kupita patsogolo, iye anayamba kupezeka pa misonkhano ndipo sanaphonyepo umodzi kuyambira panthawiyo. Nthawi pang’ono pambuyo pa chimenecho, iye anali wokhoza kulaka vuto lake lalikulu kwambiri—iye anaphwanya unansi woipa ndi mwamuna wokwatira. Tsopano, kwanthawi yoyamba m’moyo wake, iye anali wokhoza kukumana ndi chimwemwe chenicheni, popeza iye tsopano anali wokhoza kutumikira Yehova ndi chikumbumtima choyera. lye anabatizidwa mu April 1985 ndipo panthawiyo anali kutsogoza maphunziro a Baibulo anayi ndi ena. Chonulirapo chake chotsatira chiri kukhala mpainiya, popeza adzimva kuti iyi iri njira yabwino kwambiri yomwe angasonyezere chiyamikiro chake kwa Yehova, yemwe wamumasula iye kuchokera ku “moyo woipa wopanda phindu.”
◻ Zotulukapo zabwino za khalidwe laumulungu zinawonedwa mu sukulu yogonera konko ya atsikana mu Kenya, kumene khalidwe labwino la Mboni linazindikiridwa mu njira yowonekera kwambiri. Aphunzitsi a amuna asanu ndi anayi anaitanidwa ndi sukuluyo, kuphatikizapo mmodzi wa Mboni za Yehova. Koma mmodzi ndi mmodzi wa iwo anayenera kuchotsedwa chifukwa cha khalidwe loipa lakugonana ndi ophunzirawo. Mkupita kwanthawi, kokha mmodzi pa chiwerengero cha asanu ndi anayiwo anatsala—mphunzitsi amene anali Mboni ya Yehova!
Zowonadi, chiri chothekera kaamba ka anthu omwe anakhala miyoyo yoipa kusintha. Pamene tikhala ‘oyera mtima mu mkhalidwe wathu,’ sitimapereka kokha umboni wabwino kwa ena komanso timapanga mtima wa Yehova kukondwera. Chotero, tlmadziika ife eni mu mzera kaamba ka moyo wosatha.—Miyambo 27:11.
[Bokisi patsamba 21]
“Pakut! ine ndine Yehova Mulungu wanu; poterodzipatuleni, ndipo muzikhala oyera; pakuti Ine ndine woyera.”—Levitiko 11:44.
[Bokisi patasmba 21]
“Tidzikonzere tokha kulekachodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu”—2 Akorinto 7:1.