Chipembedzo ndi Kukhulupirira—Malaulo Mabwezi kapena Adani?
PANALI pa Loŵeruka, June 11, 1983, anthu a m’mudzi pa chisumbu cha ku Indonesia cha Java anawoneka akuthamangira kunyumba zawo, mwachangu kutseka ming’ankha m’madenga, mazenera, ndi zitseko. Nchifukwa ninji anali ndi mantha oterowo? Kuwombana kwa mwezi ndi dzuŵa kunali kutayambika, ndipo anthu a kumudziwo anachita mantha kuti chithunzithunzi cha kuwombanaku chikanalowa m’nyumba zawo ndi kupangitsa tsoka.
Nzika za m’maiko otchedwa otukuka kaŵirikaŵiri zimatsatira zikhulupiriro zoterozo zokhala ndi chisonkhezero cha chipembedzo. Chotero, mu mbali zina za Africa, anthu amapewa kuyenda m’dzuŵa panthaŵi ya masana chifukwa iwo “angachite misala.” Ana amaletsedwa kudya mazira, kuwopera kuti “iwo adzakhala mbala.” Makolo sanganene chiŵerengero chenicheni cha ana awo, kaamba kakuti “mfiti zingakumve ukudzigangira ndi kutenga mmodzi wa iwo.”—African Primal Religions.
Anthu a Kumadzulo amaseka pa machitachita oterowo monga mmene asonyezedwera ndi mantha a kukhulupirira malaulo, chotulukapo cha ‘umbuli wa chikunja.’ Komabe, zikhulupiriro zoterozo siziri kokha kwa awo omwe sali Akristu. Izo “zikupezeka pakati pa anthu padziko lonse lapansi,” akutero Dr. Wayland Hand, profesala wa miyambo ndi zinenero za chiGerman. Iye ndi mnzake Dr. Tally asonkhanitsa kale chifupifupi zitsanzo miliyoni za kukhulupirira malaulo mu United States mokha.
Akufunitsitsa kudziŵa mwaŵi wawo, ambiri otchedwa Akristu amayang’ana ku kupenda nyenyezi—imodzi ya mtundu wakale koposa wa kukhulupirira malaulo. Ndipo mofunitsitsa koposa, zikhulupiriro za kukhulupirira malaulo nthaŵi zina zimalandira chirikizo la poyera ndi chitetezero cha atsogoleri a chipembedzo. Mwachitsanzo, pa tsiku lozizira kwambiri mu New York, January 10, 1982, kholo la ku Eastern Greek Orthodox Vasilios anayang’anira pa Misa ya poyera kukumbukira Phwando la Epiphany. Pambuyo pa chimenecho, ikusimba New York Post, ilo linagwetsera mtanda wa golidi mu East River ndi kuuza openyererawo kuti munthu woyamba kukagwira mtandawo adzakhala ndi mwaŵi wabwino kwa moyo wake wonse.
Koma kodi zikhulupiriro za Chikristu ndi kukhulupirira malaulo ziri zogwirizana? Mlembi mmodzi anawona kuti: “Pa maziko a chikhulupiriro pamamasula duŵa la kukhulupirira malaulo.” Chotero, kodi inu simungayembekezere chipembedzo Chachikristu kutsutsa ndi kuchotsa mantha a kukhulupirira malaulo?
Chipembedzo—Kodi Chimachotsa Mantha a Kukhulupirira Malaulo?
Chipembedzo chowona chiyenera kutero, ndipo mu zana loyamba icho chinatero: Ngakhale kuti Akristu oyambirira anali kukhala pakati pa dziko lokhulupirira malaulo la Chiroma, iwo anakana kukhulupirira malaulo. Koma pambuyo pa imfa ya atumwi a Kristu, ziphunzitso za chipembedzo chonyenga, kuphatikizapo kukhulupirira malaulo, kunayamba kulowerera mu mpingo. (1 Timoteo 4:1, 7; Machitidwe 20:30) Gulu la atsogoleri a chipembedzo linayamba kutsanzira zimenezo, molingana ndi bukhu la A History of the Christian Church, linapita limodzi ndi machitachita akugwiritsira ntchito kupenda nyenyezi ndi kutsatira kukhulupirira malaulo kwina. M’kupita kwa nthaŵi machitachita ofala amenewo anaikidwa chizindikiro cha “Chikristu.”
Ndipo lerolino? Chipembedzo chimalekererabe miyambo ya kukhulupirira malaulo. Lingalirani Suriname, kumene awo otchedwa Akristu a chiyambi cha chiAfrica kaŵirikaŵiri angawonedwe akuvala zithumwa kaamba ka chitetezero choyembekezera motsutsana ndi mizimu yoipa. Woyang’anitsitsa mmodzi akunena kuti: “Tsiku lirilonse anthu amenewo amakhala ndi moyo, amadya, amagwira ntchito ndi kugona m’mantha.” Mamiliyoni kuzungulira padziko lonse ali ndi mantha ofananawo a “mizimu” ya akufa. Mwachindunji, zipembedzo kaŵirikaŵiri zapititsa patsogolo zikhulupiriro za kukhulupirira malaulo zoterozo.
Tengani monga chitsanzo chimene chinachitika pa chisumbu cha mu Africa cha Madagascar. Pamene amishonale a Dziko la Chipembedzo anayamba kufalitsa zikhulupiriro zawo, anthu a ku Madagascar anali ovomereza koma osafunitsitsa kuleka zikhulupiriro zawo za mwambo. Chivomerezo cha matchalitchi? Ikutero Daily Nation, nyuzipepala yochokera ku Kenya: “Amishonale oyambirirawo anali olekerera ndi ofewa ndipo anafika ku kulandira mkhalidwe umenewo.” Chotulukapo chake? Lerolino, theka la anthu a ku Madagascar akundandalitsidwa monga Akristu. Komabe, iwo amawopanso “mizimu” ya makolo akufa! Chotero, iwo mofala amaitana wansembe kapena pasitala kudzadalitsa mafupa a makolo akale asanawaike iwo m’manda a banja. Inde, atsogoleri a chipembedzo apititsa patsogolo bodza lakuti Mulungu, Mdyerekezi, ndi makolo akufa anganyengezedwe ndi mawu otonthoza, kunamizidwa, ndi kupatsidwa chiphuphu mwakusunga zizoloŵezi za kukhulupirira malaulo.
Chofananacho chiri chowona mu South Africa, kumene 77 peresenti ya anthu amadzinenera kukhala Akristu ndipo chiŵerengero cha opezeka pa tchalitchi chimakhala chapamwamba. Komabe, chipembedzo cha mwambo cha chiAfrica, ndi mantha ake a kukhulupirira malaulo a makolo akufa, chimakhala pakati pa mamiliyoni a awo opita ku tchalitchi. Chotero, m’maiko ambiri otchedwa a Chikristu, chipembedzo chiri kokha chikuto. Kandani pamwamba pake, ndipo kukhulupirira malaulo kwakale kungawoneke kuti kunapulumuka ndi kupita patsogolo.
Chipembedzo chowona, ngakhale kuli tero, chimachotsa mantha a kukhulupirira malaulo. Motani? Mfungulo iri chidziŵitso. Chidziŵitso cha chiyani? Ndipo ndimotani mmene mungachipezere icho?