Bukhu la Chilengedwe ndi Baibulo
“Chilengedwe chimandizizwitsa! Sindingathe kulingalira kuti ‘koloko’ yochepa yoteroyo ingakhalepo popanda Wopanga koloko.”—Voltaire, wanthanthi wa Chifrench wa mu zana la 18.
KOLOKO yachindunji imadzetsa kusirira kaamba ka luso ndi luntha la mpangi wake. Koma bwanji ponena za chilengedwe chimene chimatizinga? Kodi icho chingavumbule, chifupifupi kumlingo winawake, umunthu wa Mlengi wake?
Chifupifupi zaka 2,000 zapita, mtumwi Paulo, mmodzi wa alembi a Baibulo, anapereka yankho ku funso iri: “Pakuti chilengedwere dziko lapansi zawoneka bwino zosawoneka zake [za Mulungu] ndizo mphamvu yake yosatha ndi umulungu wake; popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa, kuti iwo adzakhale opanda mawu akuwiringula.” (Aroma 1:20) Chotero, nchiyani chimene tingaphunzire kuchokera ku kuyang’anitsitsa bukhu la chilengedwe limeneli?
Chimene Koloko Imatiphunzitsa Ponena za Wopanga Koloko
Mathithi amphamvu, nyanja mkati mwa mkuntho, madzulo opanda mitambo odzazidwa ndi zikwi za nyenyezi—izi ziri zina za zinthu zimene zimatipangitsa ife kulingalira Mlengi wamphamvu. Tsatanetsatane weniweni wa kuzungulira kwa mapulaneti kungatikumbutsenso ife, monga mmene chinakumbutsira Voltaire, kuti Mlengi ayenera kukhala Wolinganiza Wamkulu, Wopanga Koloko Wamkulu.—Masalmo 104:1.
Unyinji wa zomera za dziko lapansi, zipatso ndi ndiwo za masamba zomwe timalandira mochuluka—zimachitiranso umboni, ku kuolowa manja kwa Mulungu. Paulo anatsimikizira ku ichi pamene iye analengeza kuti Mulungu “sanadzisiira iyemwini wopanda umboni, popeza anachita zabwino, nakupatsani inu zochokera kumwamba mvula ndi nyengo za zipatso, ndi kudzaza mitima yanu ndi chakudya ndi chikondwerero.”—Machitidwe 14:17.
Chimene Koloko Simatiuza Ife
Kusanthula kowonjezereka kwa bukhu la chilengedwe kudzatiphunzitsabe ife ponena za mikhalidwe ina ya Mulungu. Koma ngati tidalira kotheratu pa zimene timaphunzira kuchokera ku chilengedwe, chidziŵitso chathu cha Mulungu nthaŵi zonse chidzakhala chopereŵera. Mlembi wa chiFrench Robert Lenoble akulongosola ichi m’bukhu lake lakuti Esquisse d’une histoire de l’idée de Nature, (Mbiri Yolongosola ya Lingaliro ya Chilengedwe): “Munthu nthaŵi zonse adzalunjikitsa chidwi chake ku chilengedwe ndi cholinga chofuna kuloŵerera chinsinsi chake ndi kupeza chinsinsi chake, chinsinsi chimene sichidzavumbulutsidwa kuchokera ku laboritare.” Loposa theka la anthu a chiFrench ofunsidwa ndi nyuzipepala ya tsiku ndi tsiku ya Chikatolika La Croix—kaya iwo anali akhulupiriri kapena osakhulupirira mwa Mulungu—anavomerezana ndi ichi ndi kuvomereza kuti “sayansi sidzakhala yokhoza kupereka kulongosola kokhutiritsa kwa chilengedwe, popeza kuti zinthu zambiri ziri mbali ya nthanthi kapena chipembedzo.”
Chifupifupi zaka 3,500 zapitazo, Yobu wokhulupirika anabwera kumapeto ofananawo. Iye anadzutsa funso lakuti: “Koma nzeru—idzapezeka kuti, ndi luntha, malo ake ali kuti?” Kodi nzeru imeneyi idzayenera kupezeka m’bukhu la chilengedwe? “Pozama pakuti, ‘Mwa ine mulibe!’ Ndi nyanja ikuti, ‘Kwa ine kulibe!’ Popeza pabisikira maso a zamoyo zonse, pabisikiranso mbalame za m’mlengalenga.”—Yobu 28:12, 14, 21.
Ndi kuti, chotero, kumene tiyenera kupita kuti tipeze nzeru imeneyi? Bukhu limodzimodzilo limayankha kuti: “Mulungu ndiye azindikira njira yake, ndiye adziŵa pokhala pake.” (Yobu 28:23) Ndipo Mulungu wagawana nzeru yake ndi mtundu wa anthu m’njira yodabwitsa kupyolera mwa Mawu ake, Baibulo.
Chidziŵitso Chapadera Kuchokera m’Baibulo
Baibulo limatipatsa ife chidziŵitso chapadera m’chiyambi cha mtundu wa anthu. Limatiuza ife kuti Mulungu anakonzekera dziko lapansi ndipo kenaka kuika pamenepo anthu aŵiri oyambirira. Makolo athu oyambirira akanakhala kosatha m’malo angwiro owazinga. Koma iwo anaukira, ndipo mwa chimo lawo iwo anatsegula njira kaamba ka zoipa zonse—kuphatikizapo chimo ndi imfa—zomwe zakantha mtundu wa anthu.—Genesis, mitu 1 mpaka 3; Aroma 5:12-21.
Baibulo limatiuzanso ife mwatsatanetsatane masitepi amene anatengedwa ndi Mulungu a kukonzera mkhalidwewo. Zaka zikwi pambuyo pa Adamu ndi Hava, Mwana weniweni wa Mulungu, Yesu, anabwera ku dziko lapansi kudzapatsa mtundu wa anthu mwaŵi wa kugwirizanitsidwanso ndi Mulungu. Kristu chotero anapereka kwa anthu omwe akasonyeza chikhulupiriro mwa iye ndi amene akazindikira mtengo wa nsembe yake chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi lomwe lidzatembenuzidwa kukhala paradaiso.—Luka 23:43; Yohane 3:16.
Chiyembekezo chimenechi chikuperekedwa kwa aliyense wa ife. Kuti tichizindikire icho tiyenera kupeza chidziŵitso ‘cholongosoka cha Mulungu yekha wowona ndi cha mmodzi yemwe anamtumiza, Yesu Kristu.’ Tiyeneranso kukhala m’chigwirizano ndi chiyembekezo chimenecho. Chidziŵitso cholongosoka chimenechi chimapezeka m’Baibulo.—Yohane 17:3; Yakobo 2:24-26.
Kodi mungakonde kukhala ndi yankho latsatanetsatane ku mafunso onga ngati, Kodi munthu anachokera kuti? Nchiyani chimene chimachitika pambuyo pa imfa? Nchiyani chimene chiri zoyambitsa za mavuto a mtundu wa anthu? Kodi pali chiyembekezo china chirichonse chakuti iwo adzathetsedwa tsiku lina? Ndi liti ndipo ndimotani mmene Mulungu adzabweretsera mikhalidwe yangwiro kwa mtundu wa anthu? Ngati ndi tero, tikukulimbikitsani inu kuyang’ana m’Baibulo, bukhu lokha lomwe lidzakupatsani mayankho ochokera kwa Mulungu wa chilengedwe ndi bukhu lokha lokhala ndi “maziko a chiyembekezo cha moyo wosatha.” Chifuno cha zofalitsidwa za Watchtower Society ndi kukuthandizani kupeza mayankho amenewo m’Baibulo lanu.—Tito 1:1, 2.
[Chithunzi patsamba 5]
Chilengedwe chimavumbulutsa mbali za umunthu wa Mulungu
[Chithunzi patsamba 6]
Kokha Baibulo lingatiuze ife ponena za zifuno za Mulungu kulinga kwa munthu ndi dziko lapansi