Kodi Pemphero Liri Loyenerera Kuyesetsako?
PA LACHISANU, May 31, 1985, unyinji wa mphepo ya mkuntho unapita kupyola ku chigawo cha kum’mwera cha Ontario, Canada. Mkulu wa chipembedzo wokhala m’mudzi waung’ono wa Grand Valley anayang’ana mopanda thandizo pamene mphepo yaukaliyo inachotsa denga la nyumba yake. Monga mmene kwasimbidwira mu nyuzipepala, iye “anawona zozizwitsa ndi ngozi zikuchitika kumbali ndi kumbali pamene iye anachitira umboni mkwiyo wosalamulirika wa chilengedwe.”
Ndithudi, okondedwa ndi mabwenzi a anthu aŵiri ophedwa ndi mphepo ya mkunthoyo analingalira ichi kukhala ngozi yowopsya. Chinateronso chikwi chosiidwa chopanda nyumba ndi mphepo yopotoza yowonongayo. Kumbali ina, ambiri a awo amene anapulumuka imfa kapena anavulazidwa kwambiri analongosola kupulumuka kwawo monga “chozizwitsa.” Ron ndi wogwira ntchito mnzake anali aŵiri a awa. Iwo anafikira malo a chisungiko a mphamvu kwambiri a mbali ya nyumba ya ofesi yawo ndi chenjezo la timphindi tinayi tokha. Pambuyo pa kulongosola kupulumuka kwawo kozizwitsa kuchokera ku imfa, Ron ananena kuti: “Inde, ndinakhulupirira mwa Mulungu chisanachitike ndipo ndiri wotsimikizira kuti ndiri wokhulupirira mwa Mulungu tsopano.”
Chanenedwa kuti panyengo ya tsoka ladzidzidzi, losayembekezeredwa, ‘pamakhala osakhulupirira Mulungu ochepa, ngati amakhalapo nkomwe.’ Ndipo ngati pali nthaŵi yokwanira pa zochitika zoterozo, mapemphero ofunitsitsa ambiri kaamba ka chitetezo ndi chipulumuko amaperekedwa.
Pa Sande, July 21, 1985, amuna ndi akazi ndi ana oposa zana limodzi anakumana kaamba ka kulambira m’Nyumba yawo ya Ufumu mu Sydney, Australia. Pambuyo pa nyimbo ya chitamando kwa Mulungu, pemphero linaperekedwa m’malo mwa mpingowo. Pamene mtumiki anali m’mphindi ya 15 m’nkhani yake ya Baibulo Sande m’mawa mmenemo, kuphulika kwa bomba mwadzidzidzi kunathetsa mtenderewo, likumamuvulaza iye kowopsya, kupha mwamuna yemwe anali kutsogolo kwa holoyo, ndipo kutulukapo m’kuikidwa m’chipatala kwa anthu oposa 40.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 3]
Kodi Pemphero Limapanga Kusiyana Kulikonse?
Zonse za zochitika zokambidwazo—chimodzi cholongosoledwa monga “mkwiyo wosalamulirika wa chilengedwe” ndi chinacho monga m’chitidwe waupandu—umadzetsa funso ponena za phindu la pemphero. Nchiyani chimene chiri phindu la kupemphera? Kodi pemphero limagwiradi ntchito? Kodi chiridi choyenerera kuyesayesa kupemphera?