Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 5/1 tsamba 21-25
  • Yehova Samasiya Atumiki Ake

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yehova Samasiya Atumiki Ake
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Moyo Wanga Woyambirira
  • Kuphunzira Chowonadi cha Baibulo
  • Kutumikira monga Koputala
  • Utumiki Wapakanthaŵi wa pa Beteli
  • Kutumikira Mosasamala Kanthu za Chitsutso
  • Kumangidwa ndi Kuikidwa m’Ndende
  • Kuchokera mu Mdima Kupita ku Kuwunika
  • Kusiya Kulambira Mfumu ndi Kuyamba Kulambira Koona
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Yehova Amakokera Anthu Odzichepetsa ku Choonadi
    Nsanja ya Olonda—2003
  • ‘Kubzala ndi Misozi ndi Kututa ndi Mfuu Yachikondwerero’
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Pamene Wina Aitana, Kodi Mumayankha?
    Nsanja ya Olonda—1992
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 5/1 tsamba 21-25

Yehova Samasiya Atumiki Ake

Monga momwe yasimbidwira ndi Matsue Ishii

KWA chifupifupi chaka chimodzi, ndinasungidwa m’ndende ya chibalo m’ndende yochepa, yauve, yodzala ndi nsabwe, mu Sendai, Japan. Kwanthaŵi yonseyo, sindinaloledwe kutenga madzi kapena kusamba. Thupi langa linakhala ndi zilonda, kulumidwa ndi nsikidzi. Ndinakanthidwa mokulira ndi nyamakazi kotero kuti sindinakhoze ngakhale kukhala kapena kuimirira. Nditakhala mafupa okhaokha ndi kulemera kochepera pa 30 kg, ndinali pafupi kufa.

Koma kodi nchifukwa ninji ndinali kumeneko? Nchifukwa ninji maulamuliro anadzagogonda pa chitseko changa pa nthaŵi ya 5 koloko m’mamawa, June 21, 1939, ndikundimanga ine? Kodi nchiyani chimene ndinachita? Awo anali masiku ovuta chifupifupi zaka 50 zapitazo mu Japan. Ndiloleni ndikuuzeni ponena za izo ndi ponena za mikhalidwe yomwe inandipereka ine m’ndende ndi mmene ndinapulumukira.

Moyo Wanga Woyambirira

Ndinabadwa mu 1909 m’Mzinda wa Kure, Japan, kokha 25 km kuchoka ku Hiroshima. Makolo anga anali ndi sitolo yogulitsa mpunga ndi yogulitsa kimono. Pamene ndinali wa zaka zisanu ndi zinayi, Spanish flu inakantha dera lathu, ndipo mwamsanga mabokosi okhala ndi mitembo anawunjikidwa m’nyumba yosungiramo mitembo. Mkulu wanga ndi ine tinakanthidwa ndi nthendayo, ndipo mlungu umodzi pambuyo pake iye anafa. Pa imfa yake ya mwadzidzidzi, ndinayamba kudabwa: ‘Nchifukwa ninji anthu amafa? Kodi nchiyani chimene chimachitika kwa iwo pa imfa?’

Atate wanga anali m’Buddha wachangu, ndipo kuti ndipeze yankho, ndinachezera makachisi a chiBuddha osiyanasiyana. Ndinakhoza kufunsa akulu a chipembedzo kumeneko: “Kodi nchifukwa ninji anthu amafa?”

“Iwe sufunikira kulingalira pa zinthu zonga zimenezo,” ankayankha tero. “Ngati iwe upitirizabe kudalira pa Buddha ndi kulimbika ndi kudzipereka kwako, udzakhala wotsimikizirika za kufikira ku Nirvana ndi kulowa mu paradaiso.”

Pamene ndinali wa zaka 17, ndinaphunzira ponena za bukhu lotchedwa Baibulo. Ndinapeza limodzi koma sindinakhoze kulimvetsetsa ilo. Pambuyo pake ndinayamba kupezeka ku tchalitchi cha “Chikristu” m’Mzinda wa Kure. Pamene ndinamva kuti imfa ya munthu inali chotulukapo cha uchimo wa Adamu, chinapanga nzeru kwa ine, ndipo ndinakhala chiwalo cha changu cha tchalitchi.

Panthaŵi imeneyo lingaliro lomwe kaŵirikaŵiri linkamveka m’mbali ya ku midzi ndi m’matauni linali: “Yaso Chipembedzo cha Chikristu chidzawononga dziko.” Popeza kuti ndinali “Mkristu” woyambirira wachangu m’dera lathu, anthu a mumzinda anandipatsa mlandu wa kubweretsa manyazi pa mzindawo ndipo anandikakamiza ine chifupifupi kuti ndichoke. Makolo anga anaipidwa nane kwambiri.

Kuphunzira Chowonadi cha Baibulo

M’kuyesayesa kwa kundipangitsa ine kusiya chikhulupiriro changa, Atate anakonzekeretsa kaamba ka ine kuti ndikwatiwe ndi mlendo kotheratu, Jizo Ishii, m’Buddha wachangu. Mbale wake wamkulu anali wansembe wamkulu wa kachisi ya chiBuddha. Ndinauzidwa kuti ngakhale kuti Jizo sanali Mkristu, iye anakhoza kumvetsetsa ponena za chikhulupiriro changa. Chotero ndinasamukira ku Osaka ndipo pa m’sinkhu wa zaka 19 ndinakwatiwa ndi Jizo, yemwe anali wosoka zovala. Koma mosiyana ndi zimene atate wanga ananena, Jizo sanandilole ine kupezeka ku tchalitchi.

Kumbuyo kwa nyumba yathu mu Tojo-cho, Osaka, panali nyumba yokhala ndi chizindikiro chakuti: “Nthambi ya Osaka ya International Bible Students Association.” Ndikumalingalira ilo kukhala gulu la Chikristu, ndinachezera nyumbayo.

“Kodi mumakhulupirira m’kuwoneka kwachiŵiri kwa Ambuye?” Ndinafunsa mwamuna wachichepere yemwe anadza kuchitseko.

“Kuwoneka kwachiŵiri kwa Kristu kunazindikiridwa mu 1914,” iye anayankha tero.

Mumkhalidwe wozizwitsidwa, ndinamuuza iye kuti chimenecho chinali chosatheka. “Ufunikira kuŵerenga bukhu iri,” iye anatero, akundipatsa ine Zeze wa Mulungu.

Kuti ndim’pangitse mwamuna wanga kusaliwona bukhulo, ndinalibisa ilo m’chola chaudzu chokhala ndi makala ndi kuliŵerenga ilo nthaŵi zonse pamene ndinakhoza. Nsonga iriyonse inandikantha ine monga mphezi​—kokha 144,000 adzapita kumwamba; Kristu sali mbali ya Utatu koma ali Mwana wobadwa yekha wa Yehova, Mulungu wamphamvuyonse; tikukhala m’nthaŵi ya mapeto; ndipo Spanish flu yomwe inatenga moyo wa mkulu wanga inali mbali ya kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Baibulo. Ndinakhutiritsidwa kuti ichi chinali chowonadi chomwe ndinkafunafuna.

Potsirizira pake, mwamuna wanga anapeza kuti ndinali kuŵerenga bukhu la Chikristu. Komabe, pamene ndinatenga kaimidwe kolimba kaamba ka chikhulupiriro changa, iye anayamba kudabwa kaya chinachake chofunika koposa chinali chophatikizidwa ndipo chotero anaŵerenga Zeze wa Mulungu iyemwini. Ndinabatizidwa chaka chotsatira, March 23, 1929, ndipo mwamuna wanga anabatizidwa mwamsanga pambuyo pake.

Kutumikira monga Koputala

Tinatseka sitolo yosoka zovala ndi kuchotsa ogwira ntchito. Titadzazidwa ndi chimwemwe, tinayamba m’ntchito yolalikira kunyumba ndi nyumba mu Osaka. Mu September 1929, ndinakhala koputala wachiŵiri wa mu Japan, monga mmene atumiki a nthaŵi zonse ankaitaniridwa, ndipo mwamuna wanga analowa m’ntchito ya ukoputala pambuyo pake. Tonse pamodzi tinatsiriza mbali zitatu mwa zinayi za Japan, kuphatikizapo Osaka, Kyoto, Nagoya, Tokyo, Sendai, Sapporo, Okayama, ndi chisumbu cha Shikoku. Tinakhala mumzinda pa malo alionse kwa chifupifupi miyezi isanu ndi umodzi, tikumalipira chipinda ndi kusumika pa kugawira mabukhu.

Tinagwiritsira ntchito mabukhu omwe analipo mu chiJapanese, onga ngati mabukhu a Zeze wa Mulungu, Deliverance, Creation, Reconciliation, ndi Government, limodzinso ndi The Golden Age, (tsopano Galamukani!) ndi Nsanja ya Olonda. Monga makoputala, tinathera maora 180 pa mwezi tikumapita kunyumba ndi nyumba. Ngakhale kuti tinali otopetsedwa mwa kuthupi, chisangalalo chathu m’kutumikira chinali chokulira.

Akoputala a ku Japan masiku amenewo sankabwezeredwa ndalama kaamba ka zotaika zawo koma analandira theka la ndalama kuchokera ku kugawira mabukhu kaamba ka ndalama zokhalira. Moyo sunali wopepuka. Koputala mnzanga anafa ndi matenda a kamwazi. Pamene ndinkalera wodwalayo, ine nanenso ndinayambukiridwa ndi matendawo ndipo ndinaikidwa m’chipatala. Pamene tinatumikira mu Nagoya, moto unayaka panyumba yapafupi ndi imene tinali kukhala. Tinathamangira pa chigawo cha pansi kuchoka pa chigawo chachiŵiri ndi zovala zokha zomwe tinavala, tikumangothaŵa kokha ndi miyoyo yathu. Ziŵiya zoŵerengeka zomwe tinali nazo ndi mabukhu kaamba ka kugawira zonsezo zinapsya, zikumatisiya ife opanda ndalama.

Pamene tinkatumikira mu Okayama, mwamuna wanga anakhala ndi malungo owopsya kwa masiku angapo ndipo anauzidwa kuti anali ndi TB ya m’mapapo. TB inali nthenda yodzetsa imfa panthaŵiyo. Ngati imfa inali yosapeweka, ife tinafuna kupita ku Sapporo cha kumpoto kwambiri kwa chisumbu, ku Hokkaido, kukachitira umboni kumene ntchito yolalikira inali isanachitidwe ndi kalelonse.

Mu September 1930, tinasamukira ku Hokkaido, kumene ndinayembekezera mwamuna wanga kufa. Kuno mpweya unali wabwino, mkaka ndi mbatata zinali zopanda mtengo kwambiri, ndipo umoyo wamwamuna wanga unawongokera pang’onopang’ono. Yehova sanatisiye ife koma anatidalitsa ife ndi madalitso okulira mu utumiki wathu.

Pamene tinagwira ntchito mu Sendai kwanthaŵi yoyamba, Bambo Inoue, prezidenti wa ku Tohoku Imperial University, anandivomereza kufunsa kwaumwini. Iye analandira mabukhu omwe ndinali nawo ndipo kenaka anandiperekeza ine ku khomo kuti andiwone ine ndikuchoka. Pamene ndinali kuchitira umboni kuchokera kunyumba ndi nyumba, ndinakumananso ndi Bansui Doi, mwamuna wotchuka wa mabukhu, yemwe anatembenuza Iliad ndi Odyssey ya Homer mu chiJapan. Iye analandira bukhu lakuti Creation.

Pakati pa olandira oyamikira a uthenga wathu panali banja la Miura kuchokera ku Ishinomori. Hagino, mkazi wake, anali wa zaka 17 zakubadwa pamene anachezera nyumba yathu mu Sendai. Pamene tinathera usiku wonse kukambitsirana Baibulo, iye anakhutiritsidwa kuti tinali ndi chowonadi. Mwamsanga banja lonse linasamukira ku Tokyo, kumene Hagino ndi mwamuna wake, Katsuo, anatumikira monga akoputala. Katsuo anamwalira monga Mboni yokhulupirika, ndipo Hagino akutumikirabe mokhulupirika. Mwana wawo wamwamuna, Tsutomu, wakhala wotembenuza panthambi ya ku Japan ya Watch Tower Society kwa zaka zambiri.

Utumiki Wapakanthaŵi wa pa Beteli

Mu ma-1930 mwamuna wanga ndi ine tinakhoza kutumikira miyezi yoŵerengeka chaka chirichonse mu Beteli yokhala mu Ogikubo, Tokyo. Panthaŵiyo, kunali chifupifupi ogwira ntchito 20 kumeneko. Makina a phokoso kwambiri aŵiri anasindikiza The Golden Age. Jizo ndi ine tinagwira ntchito m’Dipatimenti ya Zovala. Pa kusintha kwa nyengo, akoputala anakhoza kutumiza zovala zowonongeka ku Beteli. Tinazichapa izo, kuzisoka, ndi kusita ndipo kenaka kuzibwezanso kwa iwo. Tinakhozanso ngakhale kupanga zovala zatsopano kaamba ka akoputala. Pamene ntchito imeneyi inatsirizidwa, tinakhoza kubwerera ku ntchito ya akoputala ife eni.

Chimodzi cha zokumbukira zanga zopambana za ku Beteli chinali chogwirizana ndi msonkhano wopanga mbiri mu Columbus, Ohio, U.S.A., mu 1931. Mbale anasonkhanitsa wailesi yaing’ono yokhoza kulandira kuwulutsiridwa kwa m’maiko ena. Tikumatembenuzatembenuza chotsegulira chake tsiku lonse lathunthu ndi usiku wonse, tinayesera movutikira kuti tipeze programu ya msonkhano. Pakati pa usiku, liwu la prezidenti wa Watch Tower Society, J. F. Rutherford, linadza mwamphamvu. Mwamsanga mbale anayamba kutembenuza. Chotero tinamva chogamulapo cha kutenga dzina latsopano, “Mboni za Yehova,” ndi kuyankha kwamphamvu kwa kuvomereza. Tiri kutali kumeneko ku Beteli ya ku Japan, tinadzutsa kufuula kwa chisangalalo mogwirizana ndi abale athu mu America. Mphindi zoŵerengeka pambuyo pake, kulandira kwa wailesiyo kunazimilirika, ndipo palibe chirichonse chomwe chinamveka. Koma Yehova analola ife kukhala mbali ya nthaŵi ya mu mbiri imeneyi.

Kutumikira Mosasamala Kanthu za Chitsutso

Mkati mwa kupsyinjika kwa dziko lonse pambuyo pa Nkhondo ya Dziko I, m’kuntho wa utundu ndi magulu a nkhondo unasesa Japan. Wolamulira anawonedwa monga mlungu wamoyo kwa amene umphumphu wa nzika zonse unkafunikira kupitako. Koma tinakhoza kuuza anthu: “Pali kokha Mulungu mmodzi.”

“Kodi mukunena kuti wolamulira sali Mulungu?” iwo ankayankha tero.

“Padzafunikira kukhala m’tsogolo mwabwino kwambiri mobweretsedwa ndi Ufumu wa Mulungu,” tinakhoza kulongosola tero.

“Kodi mukufuna ulamuliro woposa uja wa mfumu?” iwo anafunsa tero. Chirichonse chimene tinanena, mawu athu anapotozedwa ndipo tinatchedwa opereka. Ulamuliro unalimbitsa kufufuza kwa mabukhu athu, ndipo kuchurukira kumene ofufuza osavala zovala za ku ntchito anativutitsa kunawonjezeka.

Nthaŵi zambiri kamodzi pa chaka, nkhani ya Baibulo inkachitidwa. Ngakhale kuti tinali kokha ndi Mboni 20 mu Tokyo, chifupifupi 500 anapezeka ku nkhani yakuti “Kugwa kwa Kutsungula kwa Chikristu” mu holo ya unyinji wa m’Mzinda wa Yodobashi. Apolisi anazinga mlankhuli pa pulatiformupo, ndipo atanena chirichonse chimene iwo anachilingalira kukhala choletsedwa, liwu likakhoza kufuula kuti, “Mlankhuliwe, leka!” Pa chimenecho mlankhuli anakhoza mwanzeru kulozera ku lemba ndi kuliŵerenga ilo. Popeza kuti Baibulo silinaletsedwe, iye analoledwa kupitirizabe.

Kumangidwa ndi Kuikidwa m’Ndende

Chifupifupi zaka khumi pambuyo pa kuyamba mu ntchito ya ukoputala, kumangidwa kwa unyinji kwa Mboni za Yehova kunachitika mu Japan. Pa m’mawa moipa mmenemo mwa June 21, 1939, ndinaperekedwa ku ofesi ya polisi mu Ishinomaki ndi kuponyedwa m’chipinda cha ndende cha mdima chomwe chinali ndi mwaye wogwirira kutsindwi kwake. Mwamsanga ndinasinthidwira ku Sendai ndi kuikidwa m’ndende ya chibalo. Mwamuna wanga anagwidwa nayenso, ndipo ndinaleka kugwirizana kulikonse ndi iye kufikira pambuyo pa nkhondo.

Ndinakhala m’ndende yoipayo chifupifupi chaka chimodzi ndipo ndinali pafupi kufa. Pambuyo pake ndinadziŵa kuti mkati mwa nyengo imeneyo maulamuliro ankachita kufufuza kwa Junzo Akashi, woyang’anira wa nthambi ya Japan. Potsirizira, kufunsidwa kwanga kunayambika. “Ponya Baibulo pansi ndi kuliponda,” analamulira tero wofufuza woipa. Kenaka anandiwonetsa ine kufufuza kolembedwa kwa Akashi. Pa nthaŵi yoyamba ndinalingalira kuti chinali chinyengo.

“Kodi umakhulupirira mwa Akashi?” anafunsa tero wondifunsa.

“Akashi ali kokha munthu wopanda ungwiro,” ndinayankha tero. “Malinga ngati Akashi anatsatira malamulo a Baibulo, Akashi anagwiritsiridwa ntchito monga mtumiki wa Mulungu. Koma popeza kuti ndemanga zake zasemphana ndi Baibulo, iye salinso mbale wanga.” Kalanga ine, Akashi anali atasiyadi chowonadi!

Kenaka, mlanduwo unaperekedwa, ndipo ndinatsekeredwa m’ndende ya Azimayi ya ku Sendai. Kachiŵirinso ndinaikidwa m’ndende ya chibalo. Zakudya, ngakhale kuti zinali zosakwanira, zinaperekedwa. Kwa mphindi 30 m’mawa muli monse, ndinaloledwa kuyenda mozungulira mwa kuperekezedwa ndi mkazi wina wosunga ndende. Nthaŵi imodzi wosunga ndendeyu anandiuza kuti: “Ngati nthaŵi zinali zabwino, ukanakhala m’malo a kutiphunzitsa ife. Popeza kuti nthaŵi ziri zoipa, chonde khala wodekha mtima.” Ndinalimbikitsidwa ndi mawu ake.

Panthaŵiyo, Japan inalowa mu nkhondo ndi United States, ndipo ichi chinalamulira mkhalidwe wa dziko. Kulinga ku mapeto kwa 1944, zaka zisanu ndi theka pambuyo pa kumangidwa kwanga, ndinatulutsidwa. Mu August 1945 bomba la atomu linagwetsedwa pa Hiroshima ndi Nagasaki, ndipo Japan inapambanidwa nkhondo.

Kuchokera mu Mdima Kupita ku Kuwunika

Mwamuna wanga ndi ine tinabwerera ku Mzinda wa Kure ndipo m’tsoka la pambuyo pa nkhondo tinayambitsa kakhalidwe mwa kugwiritsira ntchito sitolo yosoka zovala. Mabwenzi akale anamwazikana, ndipo tinasowa chifupifupi kugwirizana kulikonse ndi iwo. Komabe, chifupifupi zaka zinayi pambuyo pa nkhondo, tinamva kuti amishonale ankabwera kuchokera ku United States, ndipo ntchito ya Ufumu ikatsegulidwanso mu Japan.

Tikumatenga mwana wathu wamwamuna wa zaka zisanu ndi chimodzi, yemwe tinamtenga pambuyo pa nkhondo, mwamuna wanga anapezeka pa msonkhano woyamba wa pambuyo pa nkhondo, wochitidwira mu Tarumi, Kobe. Iwo unachitidwa kuchokera kothera kwa December 1949 kufika mu chaka chatsopano cha 1950. Kuyambira 1939 ntchito ya Ufumu mu Japan inakumana ndi ‘mbadwo wa mdima,’ koma potsirizira pake tinkasinthidwira ku kuwunika!

Mu 1951 tinamva kuti Nathan H. Knorr, yemwe anali prezidenti wa Watch Tower Society, anandandalitsidwa kuchezera Japan, koma sitinadziŵe tsiku. Pa April 27, 1951, pamene tinkasoka zovala kufikira pakati pa usiku, tinamva nkhani zotsirizira za tsikulo za pa wailesi. “Mr. N. H. Knorr, prezidenti wa Watch Tower, adzachezera Japan ndi kupereka nkhani pa Holo ya Kyoritsu,” wolengeza anatero. Tsiku lotsatira ndinakwera sitima ndi kuyenda makilomita 900 kupita ku Tokyo pakati pa kusauka kwa pambuyo pa nkhondo. Pa April 29, ndinali khale ndikumvetsera kwa Mbale Knorr.

Ndinali wosangalatsidwa kumvetsera ku chilengezo cha chofalitsidwa cha Nsanja ya Olonda ya mu chiJapanese kwa nthaŵi yoyamba pambuyo pa nkhondo. Ndinapita kunyumba ndi kope lofalitsidwa chatsopano la May 1, 1951. Sindikhoza kukumbukira nthaŵi iriyonse m’moyo wanga wonse pamene ndinadzimva wachimwemwe chotero. “Tsopano ntchito mu Japan yatsegulidwanso mwalamulo,” ndinalingalira tero, “ndipo monga mmene kunaloseredwa, ntchito ya Yehova idzawonjezeka, mmodzi adzakhala chikwi.”

Kuyambira pamenepo takhala tikusangalala ndi kuyanjana kokhazikika ndi gulu la Yehova. Mu August 1951 Mbale Adrian Thompson anatichezera ife kwanthaŵi yoyamba monga woyang’anira wadera. Misonkhano inayambika, ndipo abale aŵiri omwe anali apainiya apadera oyambirira mu Japan anagawiridwa ku Mzinda wa Kure. Mpingo unakula mwapang’onopang’ono, ndipo mwamuna wanga anatumikira monga mtumiki wa mpingo.

Kodi nchiyani chimene chinachitika kwa Mboni zina 130 mu nthaŵi ya nkhondo isadakhale mu Japan? Chitsanzo choipa cha Junzo Akashi, woyang’anira wa nthambi, chinali ndi chotulukapo choipa pa ambiri. Oŵerengeka anakhala omtsatira, ena anamwazikana, ndipo ena mwachiwonekere anafa mu chizunzo. Chifupifupi khumi ndi aŵiri anakhala achangu mu utumiki wa Yehova, ndipo ena akali kudalitsidwabe ndi mlingo wa umoyo ndipo akutumikira mokangalika.

Pamene umoyo wanga unawongokera, ndinatumikira monga mpainiya wokhazikika kwa zaka zoŵerengeka. Pamene mwamuna wanga anali wa zaka 71 zakubadwa, iye anasanza unyinji wokulira wa mwazi ndipo anaperekedwa ku chipatala mofulumira. Adokotala, moyamikira, analemekeza kukana kwake kwa kulandira kuthiridwa mwazi. Ngakhale kuti anachira bwino lomwe, anafa miyezi isanu ndi umodzi pambuyo pake. Mwana wathu woleredwa, Kozo, anali mpainiya wapadera kwa zaka zambiri ndipo tsopano ali mkulu Wachikristu.

Nditayang’ana kumbuyo, chikuwoneka kwa ine kuti ambiri a awo a nkhondo isadakhale omwe anapambana m’mphamvu ndi nzeru anasiya gulu la Mulungu pamene anayang’anizana ndi zipsyinjo zokulira. Mwinamwake iwo anadalira pa mphamvu zawo zokha. Awo omwe anakhala okhulupirika analibe mphamvu zapadera ndipo anali opanda chiwembu. Motsimikizirika tonsefe tifunikira kukhulupirira mwa Yehova nthaŵi zonse mtima wathu wonse.​—Miyambo 3:5.

Potsirizira pake “chisautso chachikulu” chiri chotsimikizirika kubwera. (Mateyu 24:21) Ife kenaka tingayang’anizane ndi ziyeso zomwe zinagonjetsa akalewo. Kupirira izo sikungakhale kopepuka monga mmene tingalingalire. Koma ngati tidalira pa Yehova mowonadi, kumkondadi iye ndi kulira mu mtima mwathu kaamba ka chithandizo chake, monga mmene sanandisiire ine, iye sadzasiya atumiki ake omwe amakalamira kumtumikira iye mokhulupirika.​—Masalmo 37:25.

[Chithunzi patsamba 23]

Ndinakwatiwa ndi Jizo Ishii, mlendo kotheratu kwa ine

[Chithunzi patsamba 25]

Pamene Mbale Knorr anachezera Japan mu 1951, anatumikira amishonale ndi misonkhano mu Tokyo, Nagoya, ndi Kobe (pamwambapa)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena