Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 12/1 tsamba 27-31
  • Kusiya Kulambira Mfumu ndi Kuyamba Kulambira Koona

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kusiya Kulambira Mfumu ndi Kuyamba Kulambira Koona
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zimene Zinandisonkhezera Kutsata Chipembedzo Paubwana Wanga
  • Zaka za Nkhondo
  • Ndikhala ndi Chiyembekezo Chatsopano
  • Chimwemwe cha Utumiki wa Upainiya
  • Kulaŵiratu Dziko Latsopano
  • Kuyamikira Ntchito Zanga
  • Zifukwa Zambiri Zokhalira ndi Chimwemwe
  • Yehova Amakokera Anthu Odzichepetsa ku Choonadi
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Yehova Samasiya Atumiki Ake
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Ndinathandizidwa Kuthetsa Manyazi
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Pamene Wina Aitana, Kodi Mumayankha?
    Nsanja ya Olonda—1992
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 12/1 tsamba 27-31

Kusiya Kulambira Mfumu ndi Kuyamba Kulambira Koona

YOSIMBIDWA NDI ISAMU SUGIURA

Ngakhale kuti kunali kwachidziŵikire kuti mu 1945 Japan anali kulephera Nkhondo Yadziko II, tinali ndi chidaliro kuti kamikaze (“mphepo ya mulungu”) idzaomba ndi kugonjetsa adani. Kamikaze ndi namondwe amene anawononga kwambiri sitima zankhondo za a Mongol mu 1274 ndi mu 1281 pafupi ndi doko la Japan, ndi kuwapitikitsa.

CHONCHO, pa August 15, 1945, pamene Mfumu Hirohito inalengeza kwa anthu kuti Japan wagonja ku Magulu Ankhondo Ogwirizana, mamiliyoni zana odzipereka kwa iye anataya chiyembekezo. Panthaŵiyo ndinali mnyamata wa pasukulu, ndipo inenso ndinataya chiyembekezo. ‘Ngati mfumu si Mulungu wamoyo, kodi iyeyo ndani?’ ndinadzifunsa. ‘Ndikhulupirire ndani?’

Komabe, kulephera kwa Japan mu Nkhondo Yadziko II, kunatitsegulira njira ineyo ndi Ajapani ena zikwizikwi kuti tiphunzire za Mulungu woona, Yehova. Ndisanakuuzeni za kusintha kumene ndinafunikira kupanga, choyamba ndikuuzeni za chipembedzo chimene ndakuliramo.

Zimene Zinandisonkhezera Kutsata Chipembedzo Paubwana Wanga

Ndinabadwa pa 16 June, 1932, mu mzinda wa Nagoya, ndipo ndinali wamng’ono mwa anyamata anayi. Atate ankagwira ntchito yopima malo. Amayi anga anali wokhulupirira weniweni wa Chitenrikyo, kagulu ka mpatuko ka Chishinto, ndipo mchimwene wathu wamkulu anaphunzira uphunzitsi wa Tenrikyo. Ine ndi amayi tinkagwirizana kwambiri, ndipo ankanditenga popita kokapembedza kumalo osonkhanira.

Ndinaphunzitsidwa kuweramitsa mutu popemphera. Chipembedzo cha Chitenrikyo chinaphunzitsa kukhulupirira mlengi wotchedwa Tenri O no Mikoto, kuphatikizapo milungu ina yaing’ono khumi. Mamembala ake anali kuchiritsa mwa chikhulupiriro, ndiponso anagogomezera kutumikira ena ndi kufalitsa zikhulupiriro zawo.

Monga mnyamata, ndinali wofunsafunsa. Ndinachita chidwi ndi mwezi komanso kuchuluka kwa nyenyezi kuthambo usiku, ndipo ndinkadzifunsa za kukula kwa thambo kuti limafika pati. Ndinkasangalala kuona kukula kwa mabiringanya ndi minkhaka zimene ndinali kubzala padimba laling’ono kuseri kwa nyumba yathu. Kuona chilengedwe kunalimbitsa chikhulupiriro changa mwa Mulungu.

Zaka za Nkhondo

Zaka zanga za pasukulu ya mkaka kuyambira 1939 mpaka 1945 zinalinso nyengo ya Nkhondo Yadziko II. Mbali yofunika pa Chishinto, kulambira mfumu, inagogomezeredwa m’maphunziro athu kusukulu. Tinaphunzitsidwa shushin imene inaphatikizapo kuphunzira makhalidwe a utundu ndi zankhondo. Miyambo yokweza mbendera, kuimba nyimbo ya fuko, kuphunzira malamulo a chifumu, komanso kupereka ulemu ku chithunzi cha mfumu zinali chizoloŵezi pasukulu yathu.

Tinkapitanso ku kachisi wachishinto wa kwathuko kukapempha Mulungu kuti gulu la nkhondo la mfumu lipambane. Akulu anga aŵiri anali asilikali. Chifukwa cha kuphunzitsidwa mwambo wa chipembedzo ndi utundu, ndinkasangalala ndikamva nkhani za kupambana kwa gulu la nkhondo la Japan.

Nagoya anali pachimake pa indasitale ya ndege ku Japan, choncho kunali kumene ndege zankhondo za United States zinkafuna kwambiri kuphulitsako mabomba. Masana, ndege zankhondo zamtundu wa B-29 Superfortress zinali kuuluka mwadongosolo pa mzindawu pamtunda wa mamita 9,000 m’mwamba, zikumaponya matani mazana ambiri a mabomba pa mafakitale a m’deralo. Usiku magetsi anali kuonetsa ndege zankhondo cha m’munsi pamtunda wa mamita 1,300. Ndege zankhondo mobwerezabwereza zinali kuphulitsa mabomba amoto m’madera a nyumba zokhala anthu. Mzinda wa Nagoya wokha unaphulitsidwa maulendo 54, patangotsala miyezi isanu ndi inayi kuti nkhondo ithe, zinadzetsa mavuto ndi kupha anthu oposa 7,700.

Panthaŵi imeneyi, sitima zankhondo zinali zitayamba kuponya mabomba ku mizinda khumi ya kudoko, ndipo anthu anali kunena kuti ndege zankhondo za United States zidzatera pafupi ndi Tokyo. Amayi ndi anyamata anaphunzitsidwa kumenya nkhondo ndi mikondo yansungwi poteteza dziko. Tinali kulimbikitsana ndi mawu akuti “Ichioku Sougyokusai,” kutanthauza kuti “Ndi bwino anthu mamiliyoni 100 kufa kuposa kugonja.”

Pa August 7, 1945, mutu wa nyuzipepala unati: “Bomba Lamtundu Watsopano Laponyedwa ku Hiroshima.” Patapita masiku aŵiri, lina linaponyedwa ku Nagasaki. Amenewa anali mabomba a atomu, pambuyo pake tinauzidwa kuti anasakaza miyoyo ya anthu oposa 300,000. Kenako pa August 15, titamaliza ligubo loyesera nkhondo ndi mfuti zamatabwa, tinamva zimene mfumu inalankhula mmene inalengeza za kugonja kwa Japan. Tinakhulupirira kuti tidzapambana, koma tsopano m’nkhongono munangoti zii!

Ndikhala ndi Chiyembekezo Chatsopano

Pamene asilikali a Amerika anayamba kufika, pang’onopang’ono tinayamba kuvomereza kuti United States anapambana nkhondo. Demokalase inayamba m’Japan, komanso malamulo atsopano amene anapereka ufulu wa kulambira. Moyo unali wovuta, chakudya chinali chosoŵa, ndipo mu 1946 bambo anga anamwalira chifukwa cha njala.

Tsopano, Chingelezi chinayamba kuphunzitsidwa pasukulu imene ndinali kuphunzira, ndipo siteshoni ya wailesi ya NHK inayambitsa pologalamu yophunzitsa kulankhula Chingelezi. Kwa zaka zisanu ndinkamvetsera pologalamu yotchuka imeneyi tsiku lililonse, buku lake lili m’manja ntalitsegula. Zimenezi zinandipatsa maganizo ofuna kupita ku United States tsiku lina. Chifukwa cha kukhumudwa ndi chipembedzo cha Chishinto ndi Chibuda, ndinayamba kulingalira kuti mwina choonadi cha Mulungu chingapezeke m’zipembedzo za Kumadzulo.

Kuchiyambi kwa mwezi wa April, 1951, ndinakumana ndi Grace Gregory, mmishonale wa Watch Tower Society. Anaima kutsogolo kwa siteshoni ya sitima ya Nagoya ya pamtunda akumagaŵira Nsanja ya Olonda yachingelezi ndi kabuku kachijapani ka nkhani ya m’Baibulo. Ndinachita chidwi ndi kudzichepetsa kwake ntaona ntchito imene anali kuchita. Ndinatenga mabuku aŵiriwo ndipo ndinavomera pempho lake lakuti tiziphunzira Baibulo. Ndinalonjeza kupita kunyumba kwake pambuyo pa masiku angapo kukachita phunziro la Baibulolo.

Pamene ndinakhala pansi m’sitima ndi kuyamba kuŵerenga Nsanja ya Olonda, liwu loyamba m’nkhani yotsegulira loti “Yehova,” linandikopa chidwi. Ndinali ndisanalione dzina limenelo ndi kale lonse. Sindinayembekezere kulipeza m’dikishonale laling’ono la Chingelezi ndi Chijapani limene ndinali nalo, koma linalimo! “Yehova . . . , Mulungu wa Baibulo.” Tsopano ndinayamba kumdziŵa Mulungu wa Chikristu!

Paulendo woyamba kunyumba ya amishonale, ndinamva za nkhani ya Baibulo imene inali kudzakambidwa pambuyo pa milungu ingapo ndi Nathan H. Knorr, amene panthaŵiyo anali pulezidenti wa Watch Tower Bible and Tract Society. Iye ndi mlembi wake Milton Henschel anali kucheza m’Japan, ndipo anali kubwera ku Nagoya. Ngakhale kuti chidziŵitso changa cha Baibulo chinali chochepa, nkhaniyo inandisangalatsa zedi, kuphatikizapo kucheza ndi amishonale komanso ndi ena amene anapezekapo.

Pafupifupi miyezi iŵiri, ndinaphunzira kwa Grace choonadi choyambirira chonena za Yehova, Yesu Kristu, Dipo, Satana Mdyerekezi, Armagedo ndi dziko lapansi la Paradaiso. Uthenga wabwino wa Ufumu unalidi mtundu wa uthenga umene ndinali kufunafuna. Panthaŵi imene ndinayamba kuphunzira, ndinayambanso kufika pamisonkhano ya mpingo. Ndinasangalala ndi mayanjano a ubwenzi pamisonkhano imeneyi, pamene amishonale anakhala momasuka pamodzi ndi Ajapani ndiponso anakhala nafe pa tatami (mikeka).

Msonkhano wadera woyamba ku Japan unachitikira ku Nakanoshima Public Hall mu mzinda wa Osaka mu October 1951. Anthu pafupifupi 300 anafika pa msonkhanowo kuphatikizapo amishonale pafupifupi 50 ngakhale kuti munali Mboni zosakwana 300 m’Japan monse. Ndinalinso ndi mbali yochepa pa pologalamu. Zimene ndinaona ndi kumva kumeneko zinandichititsa chidwi kwambiri kotero kuti ndinatsimikiza mtima kutumikira Yehova kwa moyo wanga wonse. Mmaŵa mwake, ndinabatizidwa m’madzi ofunda m’bafa la anthu onse lomwe linali pafupi.

Chimwemwe cha Utumiki wa Upainiya

Ndinkafuna kukhala mpainiya, mmene atumiki anthaŵi zonse a Mboni za Yehova amatchulidwira, komanso ndinali ndi udindo wothandiza banja langa. Pamene ndinalimba mtima kuuza bwana wanga zimene ndinali kufuna, ndinazizwa kumva akuti: “Ndidzagwirizana nawe ngati zimenezo zikupatsa chimwemwe.” Ndinali kugwira ntchito masiku aŵiri pa mlungu ndipo ndinakhoza kuthandiza amayi ndi zofunika za panyumba. Ndinadzimva ngati mbalame yoti yatulutsidwa m’chikwere.

Pamene zinthu zinapitirira kuwongokera, ndinayamba upainiya pa August 1, 1954, mu gawo la kuseri kwa siteshoni ya sitima ya Nagoya, pafupi ndi pamene ndinakumana ndi Grace kwanthaŵi yoyamba. Patatha miyezi ingapo, ndinalandira ntchito yokatumikira ngati mpainiya wapadera ku Beppu, mzinda wa kumadzulo kwa chisumbu cha Kyushu. Ndipo Tsutomu Miura anaikidwa kukhala mnzanga wogwira nane ntchito.a Panthaŵiyi, panalibe mipingo ya Mboni za Yehova pa chisumbu chonse, koma tsopano ilipo mazanamazana, yogaŵidwa m’madera 22!

Kulaŵiratu Dziko Latsopano

Pamene mbale Knorr anadzachezanso ku Japan mu April 1956, anandipempha kuti ndiŵerenga mokweza ndime zingapo kuchokera m’magazini yachingelezi ya Nsanja ya Olonda. Sanandiuze chifukwa chake, koma pambuyo pa miyezi yochepa, ndinalandira kalata yondiitana kukakhala nawo pa maphunziro a sukulu ya Gileadi ya amishonale mu kalasi la nambala 29. Choncho mu November chaka chomwecho, ndinayamba ulendo wosangalatsa wopita ku United States umene unakwaniritsa cholinga changa chakalekale. Kukhala ndi kugwirira ntchito pamodzi ndi banja lalikulu la Beteli ku Brooklyn kunalimbitsa chikhulupiriro changa mu gulu la Yehova looneka.

Mu February 1957, Mbale Knorr ananditenga pamodzi ndi ophunzira enanso aŵiri pa galimoto kukatitula ku Sukulu ya Gileadi ku South Lansing, cha kumpoto kwa New York. Miyezi isanu imene ndinakhala ku Sukulu ya Gileadi, ndi kumalandira malangizo kuchokera m’Mawu a Yehova ndiponso kukhala m’malo okongola pamodzi ndi ophunzira anzanga, ndinalaŵiratu dziko lapansi la Paradaiso. Anthu khumi mwa ophunzira 103, kuphatikizapo ineyo, tinatumizidwa ku Japan.

Kuyamikira Ntchito Zanga

Pamene ndinabwerera ku Japan mu October 1957 munali Mboni pafupifupi 860. Ndinapatsidwa ntchito yoyendayenda monga woyang’anira dera, koma choyamba ndinaphunzira masiku angapo za ntchitoyi kwa Adrian Thompson ku Nagoya. Dera langa linayambira ku Shimizu, pafupi ndi Phiri la Fuji, mpaka ku Chisumbu cha Shikoku kuphatikizapo mizinda ikuluikulu ngati Kyoto, Osaka, Kobe ndi Hiroshima.

Mu 1961, ndinaikidwa kukhala woyang’anira chigawo. Izi zinaphatikizapo kuyenda kuchoka ku malo ozizira kwambiri akumpoto kwa chisumbu cha Hokkaido kumka ku chisumbu chotentha cha Okinawa ndiponso kupitirira mpaka kukafika ku zisumbu za Ishigaki pafupi ndi Taiwan, mtunda wa makilomita pafupifupi 3,000.

Ndiyeno mu 1963, ndinaitanidwa ku kosi ya miyezi khumi ku Sukulu ya Gileadi ku Beteli ya ku Brooklyn. Mkati mwa kosiyo, Mbale Knorr anagogomezera kufunika kwa kuŵerengera ntchito yathu. Ananena kuti, kuyeretsa zimbudzi inali ntchito yofunika mofanana ndi kugwira mu ofesi. Ngati zimbudzi sizikanakhala za udongo, banja lonse la Beteli ndi ntchito zawo zomwe zikanakhudzidwa, iye anatero. Pambuyo pake, mbali ina ya ntchito yanga pa Beteli inaphatikizapo kuyeretsa zimbudzi, ndipo ndinakumbukira uphungu umenewo.

Nditabwerera ku Japan, ndinapatsidwanso ntchito yoyendayenda. Patapita zaka ziŵiri, mu 1966, ndinakwatira Junko Iwasaki, mpainiya wapadera yemwe ankatumikira mu mzinda wa Matsue. Lloyd Barry, amene panthaŵiyo anali woyang’anira nthambi ya Japan, anakamba nkhani ya ukwati yogwira mtima. Kenako Junko anatsagana nane m’ntchito yoyendayenda.

Ntchito yathu inasintha mu 1968 pamene ndinaitanidwa kukagwira ntchito yotembenuza ku ofesi yanthambi ku Tokyo. Chifukwa cha kuchepa kwa zipinda zogonamo pa Beteli, ndinali kuyendera kuchokera ku Sumida Ward ku Tokyo, ndipo Junko anali kutumikira monga mpainiya wapadera pampingo wathu. Panthaŵi imeneyi, malo aakulu a nthambi ankafunika. Chotero mu 1970 malo anagulidwa ku Numazu, pafupi ndi Phiri la Fuji. Pamenepo, anamangapo fakitale yosanja kaŵiri ndi nyumba zogonamo. Kumanga kusanayambe, nyumba zingapo za pamalowo zinagwiritsidwa ntchito pa Sukulu Yautumiki Waufumu, yophunzitsa oyang’anira mipingo. Ndinali ndi mwayi wophunzitsa pasukuluyi, ndipo Junko ankakonza chakudya cha ophunzira. Kunali kokondweretsa kuona mazanamazana aamuna achikristu akuphunzitsidwa maphunziro apadera a utumiki.

Tsiku lina masana ndinalandira telegalamu yofulumira. Amayi anga anali atagonekedwa m’chipatala ndipo zinali za kayakaya kuti achira. Ndinakwera sitima yachangu kwambiri kupita ku Nagoya ndipo ndinathamangira kuchipatala. Anali atakomoka, koma ndinakhala pambali pa bedi lawo usiku wonse. Anamwalira m’mbandakucha. Pamene ndinali kubwerera ku Numazu, sindinathe kungokhala osalira pamene ndinakumbukira mavuto amene anakhala nawo m’moyo mwawo ndi chikondi chomwe anali nacho pa ine. Ngati chili chifuno cha Yehova, ndidzawaona pa chiukiriro.

Banja la Beteli linadzaza m’nyumba za ku Numazu. Choncho malo okwanira mahekitala asanu ndi aŵiri anagulidwa ku Ebina City, ndipo mu 1978 nthambi yatsopano inayamba kumangidwa. Tsopano pamalo amenewa pali fakitale, nyumba zokhalamo, kuphatikizapo Nyumba ya Msonkhano imene muli mipando yoposa 2,800. Zomangidwa zaposachedwapa zimene zatha kumayambiriro a chaka chino ndi nyumba ziŵiri za nsanjika 12 kudzanso galaja yasanjika 4. Banja la Beteli tsopano lili ndi anthu pafupifupi 530, koma chifukwa cha kuwonjezereka kwa nyumba zogonamo titha kukhala ndi anthu pafupifupi 900.

Zifukwa Zambiri Zokhalira ndi Chimwemwe

Kwakhala kokondweretsa kuona ulosi wa Baibulo ukukwaniritsidwa, inde, kuona ‘wochepa akusanduka mtundu wamphamvu.’ (Yesaya 60:22) Ndikukumbukira kalekale mu 1951, mkulu wanga akundifunsa kuti, “Kodi mu Japan muli Mboni zingati?”

“Pafupifupi 260,” ndinatero.

“Basi?” anafunsa monyoza.

Ndikukumbukira ndikulingalira kuti, ‘Nthaŵi idzasonyeza chiŵerengero cha anthu amene Yehova adzasonkhanitsire ku kulambira kwake m’dziko lino la Chishinto ndi Chibuda.’ Ndipo Yehova wapereka yankho! Lerolino, m’Japan mulibe magawo osafoledwa, ndipo chiŵerengero cha alambiri oona chawonjezeka kupitirira 222,000 m’mipingo 3,800!

Zaka 44 zamoyo wanga zapitazo mu utumiki wanthaŵi zonse​—32 ndili ndi mkazi wanga wokondedwa​—zakhala zosangalatsa kwambiri zedi. Zaka 25 pa zaka zimenezi, ndatumikira ku Dipatimenti Yotembenuza pa Beteli. Mu September 1979, ndinaikidwa m’komiti ya nthambi ya Mboni za Yehova muno m’Japan.

Wakhala mwayi ndiponso dalitso kutengako mbali yochepa pothandiza anthu oona mtima, okonda mtendere kukhala alambiri a Yehova. Ambiri achita mmene ine ndinachitira​—kusiya kupembedza mfumu ndi kuyamba kulambira Mulungu yekha woona, Yehova. Nchikhumbo changa chachikulu kuthandiza anthu ochuluka kuti adze kumbali yachipambano ya Yehova ndi kupeza moyo wosatha m’dziko latsopano la mtendere.​—Chibvumbulutso 22:17.

[Mawu a M’munsi]

a Atate ake anali Mboni ija yokhulupirika imene inapulumuka bomba la atomu limene linaponyedwa ku Hiroshima mu 1945 ali m’ndende ku Japan. Onani Galamukani! yachingelezi ya October 8, 1994, masamba 11-15.

[Chithunzi patsamba 29]

Maphunziro akusukulu makamaka anali a kulambira mfumu

[Mawu a Chithunzi]

The Mainichi Newspapers

[Chithunzi patsamba 29]

Ku New York ndi Mbale Franz

[Chithunzi patsamba 29]

Ndi mkazi wanga, Junko

[Chithunzi patsamba 31]

Kuntchito m’Dipatimenti Yotembenuza

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena