Kodi Ndisinthe Chipembedzo Changa?
WOYENDETSA ndege anali atangowuluka kumene kuchoka pa Bwalo la Ndege la Naha la ku Okinawa ndi okweramo 101 mkatimo. Mwadzidzidzi iye anawona ndege zosokoneza mphepo zitatu zikumaloza kulinga kwa iye m’mkhalidwe wokagundana. Akumachitapo kanthu mwamsanga, woyendetsa ndegeyo anatembenukira mwamsanga kumanzere, mwakutero kupewa kugundana kwa mlengalenga, kupulumutsa moyo wa iyemwini ndi miyoyo ya okweramo ake. Cholembedwa chimenecho cha kuphonya pang’ono, monga momwe chinasimbidwira m’nyuzipepala ya kumpoto kwa Japan, chimachitira chitsanzo bwino lomwe kuti kuti mupulumutse miyoyo kusintha kwa mwadzidzidzi m’kachitidwe kuli nthaŵi zina kofunika.
Ngakhale kuli tero, anthu ambiri amadzimva kuti kusintha chipembedzo cha wina iri nkhani yosiyanako. Mantha okulira amadzamo. Pali mantha a kuyamba njira yosazoloŵereka. Akazi a Tachi, omwe anaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, anadzilongosola iwo eni m’njirayi: “Anthu ochulukira omwe ndimadziŵa ali ndi zikaikiro ponena za chipembedzo ndi chigogomezero chake pa ndalama. Koma zonse zomwe tadziŵa ndi kuwona kuyambira ku ubwana kunka mtsogolo ali mapwando a chipembedzo ndi miyambo. Sitilingalira zambiri ponena za tanthauzo lauzimu la hoji [kachitidwe ka pa nthaŵi ka chiBuddha ka kukumbukira munthu womwalira]. Timalingalira mokulira za hoji monga nthaŵi yosangalatsa kukhala ndi achibale ndi anansi. Lingaliro la kusiya zonsezo, kapena choipabe, kutulutsidwa ndi banja linandiwopsya ine.” Kudzimva kumeneku ponena za chipembedzo mwinamwake kumagawanidwa ndi anthu m’dera lanu.
Pali mantha ena kachiŵirinso. M’malo ambiri, anthu amawopa mtundu wina wa kuwukiridwa kwa umulungu ngati asintha chipembedzo chawo. Mkazi mmodzi yemwe anayamba kuphunzira Baibulo mu Japan anawuzidwa ndi achibale ake kuti iye anali kukumanizana ndi mavuto aumoyo ndi a banja chifukwa chakuti “ananyalanyaza makolo ake akale” ndipo anaputa ukali wawo mwa kuphunzira “chipembedzo chachilendo.”
Mantha ena omwe amaletsa anthu kusintha chipembedzo chawo ali kuwopa kusakondweretsa mnzawo wa mu ukwati kapena makolo. M’maiko ambiri a Kum’mawa, kumene kukhulupirika kwa makolo ndi banja kumawonedwa kukhala kofunika mwapadera, mkazi watsopano mofala amayembekezedwa kuchirikiza kawonedwe ka chipembedzo ka banja mu limene wakwatiwa. Ngakhale ngati okwatiranawo sali achipembedzo kwenikweni, kusungilira unansi wabwino ndi banja ndi kusunga thayo la chipembedzo zikulingaliridwa kukhala zofunika koposa. Banja limodzi la okwatirana achichepere linaleka kuphunzira kwawo Baibulo pambuyo pa kuikidwa pansi pa chididikizo chokulira pa “msonkhano wa banja.” “Kwakukulukulu, tinali ndi mantha a munthu,” akulongosola tero mwamunayo, yemwe pambuyo pake anapitirizabe phunzirolo. “Tinadzimva kuti tinafunikira kumvera zikhumbo za makolo athu, ndipo sitinafune kuwavulaza iwo mwa kusintha chipembedzo chathu.”
Ichi chimabweretsa m’malingaliro chifukwa china chimene ambiri amawopera kusintha chipembedzo chawo: kuipidwa kwa dziko lonse kwa kuwonedwa monga wosiyana. M’banja lotchulidwa pamwambapo, chimodzi cha zifukwa zopatsidwa ndi makolo kaamba ka okwatirana achicheperewo kuleka phunziro lawo la Baibulo chinali chakuti sanafune ana awo kuwonedwa monga achilendo kapena odulidwa ku machitachita a m’mudzi.
Mantha amphamvu, chotero, akuphatikizidwa mu funso lakuti, Kodi ndisinthe chipembedzo changa? Monga chotulukapo, ambiri amatenga kawonedwe ka nthanthi: Sichiri kanthu kwenikweni chipembedzo chimene muli nacho, kodi chimatero? Kodi zipembedzo zonse siziri kokha njira zosiyana zotsogolera ku nsonga imodzi ya phiri? Pamene chidza ku chipembedzo, iwo, monga anyani atatu a m’mwambi, samawona choipa, samamva choipa, samalankhula choipa.
Koma ena asintha chipembedzo chawo. Nchifukwa ninji? Kwa ambiri a awa, chinali kokha nkhani ya kugwirizana ndi chipembedzo china chomwe chinalonjeza umoyo wa mwamsanga kapena mapindu a za ndalama, pamene pa nthaŵi imodzimodziyo akusungirira malingaliro awo a chipembedzo cha mwambo ndi zochitachita. Koma kwa ena, kwakhala kusintha kwenikweni ndipo kotheratu. Inu mungakhale mukudabwa, ngakhale kuli tero kuti, ‘Kodi pali zifukwa zokwanira kaamba ka ine za kusinthira chipembedzo changa? Nchifukwa ninji ena akhala ofunitsitsa kusintha? Kodi kusinthaku kungakhale ndi chiyambukiro chenicheni pa moyo wanga?’ Tikuitanani kusanthula nkhani yotsatirayi kaamba ka yankho.
[Chithunzi patsamba 3]
Kodi nchiyani chimene chimasonkhezera anthu kumamatira ku miyambo yawo yofala ya chipembedzo?