Mtsogolo Mowala mwa Dziko Lapansi Pansi pa Ufumu wa Mulungu
BAIBULO limanena kuti “chikhulupiriro ndicho chikhazikitso cha zinthu zoyembekezeredwa.” (Ahebri 11:1) Monga mmene tawonera m’nkhani yapitayo, zoposa zaka 500 asanabadwe Kristu, Mulungu anapangitsa kulembedwa mu bukhu la Danieli kuwoneratu kwa ulosi kwa kukwera ndi kugwa kwa mphamvu za dziko kuchokera m’tsiku la Danieli kufikira ku nthaŵi yathu. Kulongosoka kwa maulosi amenewa kumatitsimikizira ife, kutipatsa ife chifukwa champhamvu kaamba ka chikhulupiriro, kuti otsalira a maulosi a Danieli adzakwaniritsidwanso, ndipo kuti posachedwapa Ufumu wa Mulungu pansi pa Kristu Yesu udzaloŵa m’malo maboma a anthu.
Ndi kusintha kotani kumene iko kudzakhala kaamba ka mtundu wa anthu! Kuyang’ana kutsogolo ku nthaŵi imeneyo, Mulungu iyemwini akunena kuti: “Tawonani! Ndikupanga zinthu zonse zatsopano.” (Chivumbulutso 21:5) Kulingalira kwa ena a maulosi ouziridwawo omwe amaika chithunzi kaamba ka ife cha nthaŵi ya chimwemwe imeneyo kudzatithandiza ife kuwona kuti ndi “mwatsopano” chotani mmene zinthu zidzakhalira, kuti zidzakhala zosiyana kotheratu chotani kuchokera ku zimene timawona lerolino pansi pa utsogoleri wa anthu. Ndithudi, chimene Baibulo limanena ponena za mtsogolo mwa dziko lathu lapansi ndi moyo wathu pa iro sichiri chinachake chosasangalatsa. Lingalirani:
Upandu ndi chiwawa zidzatha. “Pakuti ochita zoipa adzadulidwa, . . . ndipo woipa adzatha psiti.” Awo okhala ndi moyo “adzakhala yense patsinde pa mpesa wake ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwawopsya; pakuti pakamwa pa Yehova wa makamu padanena.”—Masalmo 37:9, 10; Mika 4:4.
Kugawanikana kwa ufuko ndi utundu, ndi nkhondo zomwe zimadzutsa, zidzatheratu. “Mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.”—Yesaya 2:4.
Kupereŵera kwa nyumba, kusowa kokhala, ndi kusowa ntchito zidzakhala zinthu zakale. Yesaya ananeneratu kuti: “Ndipo iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzaoka minda yampesa, ndi kudya zipatso zake. . . . Adzasangalala nthaŵi zambiri ndi ntchito za manja awo.”—Yesaya 65:21, 22.
Njala yowopsya, yonga ngati iyo imene posachedwapa yakantha mbali zambiri za Africa, idzaloŵedwa m’malo ndi chakudya chochuluka kaamba ka onse. “M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri.” “Dziko lapansi lapereka zipatso zake, Mulungu, Mulungu wathu, adzatidalitsa.”—Masalmo 72:16; 67:6, 7.
M’kuwonjezerapo, padzakhala umoyo wabwino ndi moyo ndi umene tidzasangalala ndi madalitso amenewa. Ngakhale m’nthaŵi ya utumiki wa pa dziko lapansi wa Yesu, mowonadi chinanenedwa kuti “anthu akhungu alandira kuwona kwawo, opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, ogontha akumva.” Ngakhale kuli tero, lonjezo lokulira lidzagwira ntchito: “Iye [Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo, ndipo sipadzakhalanso imfa, ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.”—Luka 7:22; Chivumbulutso 21:4.
Kudzakhala kusintha kokulira chotani nanga! Ndi mpumulo wotani nanga umene zonsezi zidzabweretsa kwa mtundu wa anthu opsyinjika! Tikukulimbikitsani inu kudzigonjetsera inu eni ngakhale tsopano ku Ufumu wa Mulungu, kotero kuti inu nanunso mungatute mapindu amene adzabwera kuchokera ku kusintha kwa mwadzidzidzi kumeneku m’kulamulira kwa dziko.
[Chithunzi patsamba 7]
Anthu okhala ndi moyo tsopano angayang’ane kutsogolo ku madalitso osangalatsa—kutha kwa nkhondo, upandu, umphaŵi, matenda, ndipo ngakhale imfa. Kodi mungasangalale ndi mtsogolo moteromo?