Mafano a Chimpembedzo—Kodi Ndimotani Mmene Mumawawonera Iwo?
MU 1888 panali kusefukira kokulira mu Canton, China. Mvula yosalekeza inawononga mbewu. Mosowa chochita anthu a kumalowo anapemphera kwa mulungu wawo Lung-wong kupangitsa mvulayo kuleka, koma popanda phindu. Atakwiitsidwa ndi kusachitapo kanthu kwa mulungu wawo, iwo anaika m’ndende fano lake kwa masiku asanu! Zaka zingapo chisanachitike, mulungu mmodzimodziyo ananyalanyaza mapemphero awo a kuthetsa chilala. Iwo anamanga unyolo fano lake kunja kwa zitseko m’kutentha kowopsya.
Mu 1893 chilala chinakantha Sicily. Machitatchita a chipembedzo, makandulo oyatsidwa m’matchalitchi, ndi mapemphero kwa mafano zonsezo zinalephera kubweretsa mvula. Atataya kuleza mtima, anthu a kumalowo anavula mafano ena minjiro yawo, kutembenuzira nkhope za ena ku khoma, ndipo ngakhale kuponya ena m’malo osambira akavalo! Mu Licata, Angelo “Woyera” anavulidwa, kumangidwa unyolo, kunyozedwa, ndi kuwopsyezedwa ndi kupachikidwa. Mu Palermo, Italy, Joseph “Woyera” anaponyedwa m’munda kuti adikirire mvula.
Zochitika zimenezi, zolongosoledwa m’bukhu la The Golden Bough, ndi Sir James George Frazer, ziri ndi matanthauzo osokoneza. Izo zimasonyeza kuti ponse paŵiri awo odzinenera kukhala Akristu ndi awo osakhala Akristu amawoneka kukhala ndi kawonedwe kofanana ka mafano a chipembedzo. M’nkhani ziŵiri zonsezi, olambirawo anagwiritsira ntchito mafano awo monga njira ya kufikira “woyera” kapena ka mulungu. Ndipo mosangalatsa, onse aŵiri anayesera kusonkhezera “oyera” awo opanda thandizowo kapena milungu kuchita kanthu mwa kubweretsa pa iwo mikhalidwe yoipa imene alambiri awo anali kukumana nayo!
Lerolino, ngakhale ndi tero, ambiri omwe amagwiritsira ntchito mafano a chipembedzo angawone kachitidwe koteroko kukhala konkitsa, mwinamwake koseketsa. Iwo angatsutse kuti kwa iwo mafano ali chabe zinthu zolemekezedwa—osati zolambira. Iwo angafikire pa kudzinenera kuti mafano, mitanda, ndi zopkidwa utoto za chipembedzo ziri zothandiza zoyenera mkulambira Mulungu. Mwinamwake mumadzimva mwanjira yofananayo. Koma funso liri lakuti: Ndimotani mmene Mulungu amadzimverera ponena za ichi? Kodi icho chingakhale chakuti kulemekeza kwa fano ndithudi kumafikira ku kulambira ilo? Kodi chiri chotekera kuti machitachita oterowo m’chenicheni amapereka ngozi zobisika?