Chididikizo cha Kupambana
MALONDA a pa TV amasonkhezera anthu a ku Nigera “Kukhala achipambano. Kukhala ofunika koposa” mwa kugwiritsira ntchito mtundu watsopano wa mankhwala otsukira mano. Pamene kuli kwakuti tonsefe timadziŵa kuti mankhwala otsukira mano sangayamule nkomwe mfungulo ku kukhala wofunika kwa munthu, osatsa malondawo akusonyeza kuti iwo amazindikira kuti anthu amafuna kuzindikiritsidwa ndi zinthu zomwe zimanyamula chizindikiro cha “chimpambano.”
Chikhumbo cha kupambana ndi kukhala ozindikiridwa ndi ena chiri chachibadwa. Mosasamala kanthu za chimenecho, ponse paŵiri amuna ndi akazi kaŵirikaŵiri amaika chigogomezero choterocho pa zokwaniritsa za anthu kotero kuti iwo amadzika iwo eni pansi pa chididikizo “kuti ayendere limodzi ndi mafashoni atsopano.” Kodi ichi chingakhale chowopsya? Kodi icho chingakuyambukireni?
Zididikizo Zimene Anthu Amayang’anizana Nazo
Chikhumbo chaumwini cha kukhala wolemera chingadzetse chididikizo. Anthu ambiri amafuna kukhala okhoza kupanga “matamandidwe a moyo [wawo],” kuti akhale ndi kunyada kwa mayanjano ndi kutchuka.—1 Yohane 2:16.
Banja lingaike chididikizo. M’nyumba zambira mwamuna mopitiriza ayenera kukalamira kuti awongolere malipiro ake ndi kaimidwe kake pa malo ake a ntchito ndi cholinga chofuna kukweza kaimidwe ka mayanjano ka banja lake. Kapena mkazi angakalamire kukhala mkazi wogwira ntchito wachipambano. Ana angakankhidwire kulinga ku kachitidwe kapamwamba ka maphunziro kosalingalirika pa sukulu. Iri liridi vuto lapadera m’mitundu yotukuka kumene kumene ambiri amakhulupirira kuti mfungulo ya kukhala bwinopo kwa munthu iri maphunziro apamwamba.
Chitanganya nachonso chingaike chididikizo pa munthu cha kuika chonulirapo kaamba ka maphunziro apamwamba, chuma, ndi malo otchuka ndi achisonkhezero. Chipambano, chimene kaŵirikaŵiri chimayesedwa mwa ndalama, chingatsogoze ku kutchuka, chitamando, ndi ulemu. Mkonzi wa nkhani wa Daily Times ya ku Nigeria ananena kuti: “Mosasamala kanthu kuti ndi yabwino ndi yosangalatsa chotani mmene mikhalidwe ya wina ingakhalire, [anthu] ambiri samamlemekeza ndi kumuzindikira iye, ngati iye alibe ndalama.”
Nchiyani Chomwe Chingatulukepo?
Chipambano cha kudziko choterocho chingabweretse chimwemwe china, koma lingalirani mtengo wokulira umene chimadzetsa. Wolemba nkhani m’danga la nyuzipepala Achike Okafo analemba kuti: “Mabanja okhazikika . . . tsiku ndi tsiku akusweka, mokulira chifukwa cha ndalama ndi zimene ndalama zingagule. . . . Ngakhale akazi amene adakakwanitsabe kugwirira pamodzi samalankhula nkomwe ponena za mathayo awo a ukholo . . . chifukwa chakuti iwo ali otanganitisidwa kwambiri m’kulondola zofunika zakuthupi za kukhala bwino.” Onjezerani ku ichi vuto la ana onyalanyazidwa omatembenukira ku anamgoneka ndi upandu kapena kuthaŵa panyumba, ndipo mtengo umakhala wokwera koposa.
Chididikizo cha chipambano chakankhira anthu ena onyada mu kusawona mtima ndi mkhalidwe woipa wa chisembwere. Akazi achichepre afikira pa kugulitsa ziyanjo za kugonana kaamba ka zotulukapo zabwino za mayeso ndi ntchito. Ngakhale pamene chipambano chafikiridwa mwaulemu, anthu otchuka angayang’anizana ndi kukwiya kapena kuipidwa ndi anthu opanda chipambano limodzinso ndi chinyengo cha “mabwenzi” omwe ali okokedwa ndi chuma ndi kutchuka. (Mlaliki 5:1) Kodi ichi ndithudi chiri chipambano?
Wolemba wanzeru wa Mlaliki m’Baibulo akuyankha kuti ayi. Pambuyo pa kufufuza chuma chake chokulira, mphamvu, ndi kutchuka, limodzinso ndi chisangalalo chimene izi zinabweretsa, iye anamaliza kuti izi zinali “zachabechabe ndi kungosautsa mtima.”—Mlaliki 2:3-11.
Kodi ichi chimatanthauza kuti cholondola chirichonse m’moyo chiri chopanda pake? Kapena kodi pali kulinganizika koyenerera kumene anthu angakhale nako pamene akumangirira ntchito yopindulitsa? Ndi chiyani chimene chokumana nacho chikusonyeza kuti mwachidziŵikire chidzatsimikizira kukhala chonulirapo chawo chopindulitsa kwenikweni?