Kulambira Satana mu Nthaŵi Yathu
PALIBE kukaikira kuti Satana amfuna kulambiridwa. Pamene anali kuyesa Yesu, iye anapereka kumpatsa iye mphatso yaikulu pa maziko amodzi okha: “Ngati udzagwa pansi ndi kundigwadira ine.” (Mateyu 4:9) Yesu, ndithudi, anakana, koma si aliyense amene watsatira chitsanzo chake. Kulambira Satana kuli kofala m’dziko lathu lamakono.
Mwachitsanzo, mu Canada The Calgary Herald inafalitsa mipambo ya nkhani pansi pa mutu wakuti “Ophunzira a Mdyerekezi.” Pepalalo linagwira mawu ripoti la wofufuza wapolisi, akumanena kuti: “Kupyolera m’kufunsa ndaphunzira kuti Usatana siuli wopatulika ku gulu lapadera m’chitaganya. Nzeru zosonkhanitsidwa ndi Calgary Police Service ndi Royal Canadian Mounted Police zikuvumbula kuti mu Calgary mokha muli chiŵerengero choyerekezera cha 5,000 ochita Usatana.”
Maripoti a manyuzipepala ena amasonyeza kuti matsenga a Satana, m’mitundu yosiyana, akuwonekera mu United States ndi Europe. Ngakhale apolisi amasonyeza chikondwerero mu Usatana. Nchifukwa ninji? Chifukwa m’nkhani zambiri iwo akupeza kugwirizana pakati pa upandu ndi matsenga a usatana. Posachedwapa, wapolisi wofufuza chinsinsi anagwidwa mawu akunena kuti: “Chomwe tikuchita nacho chiri chipembedzo ndi anthu omwe amakhulupirira mu icho monga mmene ena amakhulupirira mu Chikristu, Chiyuda kapena Chisilamu. Omwe mukuwona sali maupandu kaamba ka chifukwa cha upandu, koma maupandu kaamba ka chifukwa cha chipembedzo.”
Chitsanzo chimodzi chowonekera chinali kupha kochitidwa ndi fuko la Manson mu California kubwerera mu 1969. Mogwirizana ndi mbiri yakale profesa Jeffrey Russell, “Manson anadzinenera kukhala ponse paŵiri Kristu ndi Satana. . . . Wotsatira wa Manson’s Tex Watson analengeza, pamene anabwera kudzapha Sharon Tate, ‘Ndine mdyerekezi; Ndiri pano kuchita ntchito ya mdyerekezi.’” Koma Usatana suli nthaŵi zonse woipa monga ichi.
Ufiti, Kukhulupirira Mizimu, ndi Kupenduza
Ndithudi, kulambira Satana sikuli ndi malire ku kulambira kwachindunji kwa Satana ndi dzina. Mtumwi Paulo anachenjeza kuti: “Zimene amitundu apereka nsembe azipereka kwa ziwanda.” (1 Akorinto 10:20) Ndipo kulambira ziwanda kulidi kofanana ndi kulambira Satana, popeza Satana akutchedwa “mkulu wa ziwanda.” (Marko 3:22) Ndi machitachita otani a “amitundu” amene angazindikiritsidwe monga kulambira ziwanda, kapena kulambira Satana? Mawu a Mulungu kwa Israyeli amatipatsa ife zitsanzo zina: “Asapezeke mwa inu munthu . . . wosamalira mitambo, wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wa nyanga, kapena wotsirika kapena wobwebweta kapena wopenduza kapena wofunsira akufa. Popeza aliyense wakuchita izi Yehova anyansidwa naye.”—Deuteronomo 18:10-12.
Chotero, tikuchenjezedwa molimbana ndi nsembe za mwazi ndi nsembe za mizimu zochitidwa ndi ansembe a voodoo mu Brazil kapena ndi mahoungan ndi amambo a ku Haiti. Ndipo tikuchenjezedwa molimbana ndi machitachita ofananawo a Santeria, owonedwa ndi anthu othaŵa kwawo a ku Cuba mu United States. Tikuchenjezedwa, kachiŵirinso, molimbana ndi openduza omwe amadzinenera kukhala akulankhulana ndi miyoyo ya akufa kuwuzira mantha mwa amoyo.—Yerekezani ndi 1 Samueli 28:3-20.
Ufiti uli wofala m’mbali zosiyanasiyana za Africa. Mu South Africa, mwachitsanzo, adokotala a ufiti amapereka mphamvu yokulira, ndipo anthu amawatenga iwo mosamalitsa koposa. Nkhani zaposachedwapa zosimbidwa mu nyuzipepala zinali za khamu la anthu likumatentha anthu amoyo omwe anapatsidwa liwongo la kupangitsa chin’aning’ani kukantha anthu anzawo a m’mudzi! Asing’anga aufiti amenewo anapatsa liwongo minkhole yopanda liwongo ponena za zochitika “zosakhala za chilengedwe” zimenezi ndi kuwamangirira iwo ku mtengo kuti atenthedwe. Chikhulupiriro choterocho cha kupenduza kapena matsenga mofananamo chiri kulambira ziwanda.
Ngakhale kuli tero, ufiti suli wotsekerezedwa ku Africa. Mu 1985, Herbert D. Dettmer, akumatumikira chilango cha m’ndende pa malo owongolera mu Viriginia, U.S.A., anapatsidwa kuyenera ndi Bwalo Lamilandu la Bomalo kaamba ka Boma la Kum’mawa la Virginia kukhala ndi kuyenera ku zovala ndi zinthu kotero kuti angamachite chipembedzo chake m’ndende. Ndipo nchiyani chomwe chinali chipembedzo chake? Mogwirizana ndi cholembera cha bwalo lamilandulo, iye anali chiwalo cha “Tchalitchi cha Wicca (chodziŵika mofala monga ufiti).” Kenaka, Dettmer anali ndi kuyenera kwa lamulo kwa kugwiritsira ntchito m’kulambira kwake sulfure, m’chere wa m’nyanja, kapena m’chere wopanda iodine: makandulo; lubani; koloko yokhala ndi dongosolo la chidziŵitso; ndi mwinjiro woyera.
Inde, mogwirizana ndi zisonyezerozo, ufiti uli wofala Kumadzulo. Nyuzipepala ya chiBritish Manchester Guardian Weekly inasimba kuti: “Zaka zisanu zapitazo, panalingaliridwa kukhala chifupifupi mfiti 60,000 mu Britain: lerolino [1985] chiŵerengerocho chikuyerekezedwa ndi mfiti zina kukhala chinakwera kufika ku 80,000. Prediction, magazini ya mwezi ndi mwezi kaamba ka openda nyenyezi ndi matsenga, iri ndi kufalitsidwa kwa 32,000.”
Usatana ndi Nyimbo
Profesa Russell, m’bukhu lake Mephistopheles—The Devil in the Modern World, akukokera chisamaliro chathu kunjira ina mu imene zifuno za Satana zikupititsidwa patsogolo. Iye akulemba kuti: “Kuwonekera kwa Usatana kunatha mofulumira atapita ma 1970, koma mbali za mikhalidwe ya Usatana zinapitiriza mpaka mu ma 1980 m’nyimbo ‘zachitsulo zamphamvu’ za rock limodzi ndi kutchulidwa kwake kwa pa kanthaŵi kwa dzina la Mdyerekezi ndi ulemu wolingalirika kaamba ka mapindu Ausatana a nkhalwe, anamgoneka, kuipa, kupsyinjika, kudzimwerekeretsa, chiwawa, phokoso ndi chisokonezo, ndi kupanda chimwemwe.”—Kanyenye ngwathu.
Mwinamwake oimba nyimbo omwe anaphatikizamo mbali za Usatana mu nyimbo zawo sanali osamalitsa. Iwo angakhale anangoyesera kuwopsyeza kapena kukhala achilendo. Mosasamala kanthu za chimenecho, anthu ena osindikizika anayambukiridwa mwamphamvu. Profesa Russell akudziŵitsa kuti “kufalitsa nkhani kokhazikika kosamalitsa pang’ono kwa choipa kwakhala ndi zotulukapo zoipa pa maganizo opusa ndi ofooka. Chotulakapo chimodzi chakhala kuwirikiza kwa maupandu akale, kuphatikizapo kuwopsyeza ana ndi kuduladula kwa zinyama.”
Nkhani ya posachedwapa inadzidzimutsa anthu a ku New York. Mogwirizana ndi ripoti la nyuzipepalayo, mnyamata wa zaka 14 zakubadwa, “atadzazidwa m’maganizo ndi Usatana,” analasa amayi ake kufikira imfa ndipo kenaka anadzipha. Phungu wa banja wa ku Canada, ananena kuti monga mmene anasimbidwira mu magazini ya Maclean’s, chiŵerengero chomakula cha a zaka zapakati pa 13 ndi 19 ovutitsidwa ananena ponena za machitachita “a usatana, kaŵirikaŵiri m’kuphatikiza ndi anamgoneka ndi mitundu yotsendereza yowonjezereka ya nyimbo zachitsulo zamphamvu za rock.”
Osati Kokha Chizoloŵezi Chopita
Chizoloŵezi chopita chomwe chikukantha United States pa nthaŵi ino chikutchedwa kupitira. Anthu kaŵirikaŵiri amalipira mazana a madola kuti atengemo mbali mu magawo mu amene “wopititsa,” kunena kuti wobwebweta, amadzinenera kudziika iyemwini (opititsa kaŵirikaŵiri amakhala akazi) m’kugwirizana ndi mzimu wa munthu wakufa kale. Mu nkhani ya kupititsa kumodzi, nyuzipepala inasimba kuti, magawowo “mwakanthaŵi amawonetsedwanso ndi wailesi ya kanema yogwiritsira nthcito mphamvu ya chilengedwe yolunzanitsidwa kwa zikwi za anthu pa nthaŵi imodzi m’mizinda isanu ndi umodzi.” Chikhoterero chimenechi chiri chiwonetsero cha kusamvera uphungu wa Baibulo wa kupewa obwebweta ndi openduza. Chotero, uli mtundu wa kulambira umene ungazindikiritsidwe monga kulambira chiwanda. Ndipo mofanana ndi kukhulupirira mizimu konse, kuli kozikidwa pa bodza la usatana lakuti moyo wa munthu uli wosafa.—Mlaliki 9:5; Ezekieli 18:4, 20.
Chisonkhezero cha Mdyerekezi m’Dziko Lodzala ndi Udani
Mkhalidwe wowopsya wa mtundu wa anthu m’zana lino la 20 umatipangitsa ife kudabwa kuti kaya ngati chisonkhezero cha Satana sichimafikira ngakhale patali. Profesa Russell akukhudza ichi pamene akunena kuti: “Pa nthaŵi ino, ndi unyinji wa zida za nyukliya ukumayerekezeredwa pa nthaŵi makumi asanu ndi aŵiri unyinji wofunikira kupha chamoyo chirichonse choyenda pa dziko lonse lapansi, ife mouma khosi tikukonzekera kaamba ka nkhondo yomwe sidzapindulitsa munthu aliyense, mtundu, kapena malingaliro koma idzaŵeruza zikwi za mamiliyoni ku imfa yowopsya. Kodi ndi mphamvu yanji yomwe imatisonkhezera ife kupita m’njira yomwe tsiku ndi tsiku iri yowopsyerapo? Kodi ndi ku ubwino wandani kumene kuli kuwononga kwa nyukliya kwa pulanetiyi? Kokha mphamvu imeneyo imene kuyambira pa chiyambi yakhala ndi nkhalwe ndi nkhwidzi yopanda malire yafuna kuwononga chilengedwe.”
Ndani kapena nchiyani chimene chiri mphamvu imeneyo? Profesayo akupereka yankho lake m’mawu awa: “Mdyerekezi walongosoledwa kukhala mzimu umene umafuna kutsutsa ndi kuwononga chilengedwe cha Mulungu ku ukulu wa mphamvu yake. Kodi mphamvu yomwe ikutisonkhezera ife kuwunjika zida za nyukliya singakhale mphamvu imodzimodziyo yomwe nthaŵi zonse yakalamira kukana kukhalako kwa iyo yeni? Mu vuto lokulira koposa iri la pulaneti yathu, sitingachotse kuthekera kumeneko.” Akristu ndithudi samachotsa kuthekera kumeneko! Yesu iyemwini anasonyeza chisonkhezero chachikulu cha Satana pa dziko iri pamene Iye anamutcha iye “mkulu wa dziko iri lapansi.” (Yohane 12:31) Likumalongosola mkhalidwe wamaganizo wa Satana lerolino, bukhu la Chivumbulutso limanena kuti iye ali nawo “udani waukulu, podziŵa kuti kamutsalira kanthaŵi.” (Chivumbulutso 12:12) Likumalozera ku chimene Satana akuyesera kukwaniritsa m’nthaŵi yathu, bukhu limodzimodzilo limanena kuti iye akugwiritsira ntchito kubukitsa kwa uchiwanda kusonkhanitsa atsogoleri a dziko iri “kuwasonkhanitsira ku nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.” (Chivumbulutso 16:14) Ayi, sitingachotse chisonkhezero cha Satana Mdyerekezi pamene tiyesera kumvetsetsa chifukwa cha njira yodzisakaza mwamisala ya mtundu wa anthu.
Mtumwi Paulo anatcha Satana “Mkulu wa ulamuliro wa mlengalenga, wa mzimu wakuchita tsopano mwa ana akusamvera,” ndi “mulungu wa nthaŵi ino.” (Aefeso 2:2; 2 Akorinto 4:4) Nchosadabwitsa kwenikweni kuti ambiri amafunsa ngati nkhalwe yonse ya mbadwo uno wa sayansi “wowunikiridwa”—nkhondo ziŵiri za dziko, kupha kwa dala kwa mafuko mu Europe ndi Kampuchea, njala yosonkhezeredwa ndi ndale zadziko mu Africa, kugawanikana kozama kwa chipembedzo ndi ufuko kwa dziko lonse, udani, kuphana, kuzunza kwadongosolo, kupatutsidwa kwa upandu kwa mtundu wa anthu mwa anamgoneka, kungotchula zochepa zokha—sikungakhale kukutsatira pulani yaikulu ya mphamvu ya magwero amphamvu oposa, oipa omwe akhoterera ku kupatutsa mtundu wa anthu kuchoka kwa Mulungu ndipo mwinamwake kutsogolera ku kudzipha kwa chiwunda chonse.
Ndani, chotero, amene ali Satana? Kodi nchiyani kwenikweni chimene akufuna? Nchiyani chimene ife monga aliyense payekha tingachite ponena za icho? Tikukuitanani kulingalira kukambitsirana kwa mafunso amenewa m’nkhani ziŵiri zotsatirazi.
[Chithunzi patsamba 7]
Akumapewa nyimbo za usatana, anthu a Mulungu amafuna zosangulutsa zomangirira