Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 10/8 tsamba 3
  • Kukwera ndi Kugwa kwa Kulambira Satana

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kukwera ndi Kugwa kwa Kulambira Satana
  • Galamukani!—1994
  • Nkhani Yofanana
  • Achichepere a Lerolino—Kodi Ali Mikhole Yosavuta ya Kulambira Satana?
    Galamukani!—1994
  • Kulambira Satana mu Nthaŵi Yathu
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Satana—Kodi Iye Ali Weniweni?
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Satana
    Galamukani!—2013
Onani Zambiri
Galamukani!—1994
g94 10/8 tsamba 3

Kukwera ndi Kugwa kwa Kulambira Satana

Kulambira mulungu wawo, Satana, kuli mkati m’zipinda zapansi pamene madzoma ausatana akuchitidwa ndi ansembe ovala minjiro yakuda, akumafuula mapemphero kaamba ka mikhole yomangiriridwa pa guwa la nsembe, makandulo ali phetipheti akumachititsa zithunzithunzi zowopsa pazipupa. Pogwirizanitsidwa pamodzi ndi chidziŵitso chawo chobisika cha zinsinsi limodzi ndi zamizimu, otengamo mbali achichepere okhala pa ulendo umenewu woloŵa mu malaulo amakondwera ndi chisangalalo chimene chimadzaza malowo. Iwo amayandikira pafupi ndi guwa la nsembelo ndi malingaliro a mphamvu akudziona kukhala ndi kupatulika kwambiri kokhala ndi iwo okha.

Kodi ndi chikondwerero wamba chopanda ngozi? Kapena kodi ndi uchiŵanda umene wafalikira m’chitaganya cha lerolino?

ZOCHULUKA zalembedwa m’manyuzipepala, magazini, ndi mabuku ponena za machitachita ochititsa kakasi a timagulu tausatana. Zochitika za ntchito zofala za magulu achiwawa a Usatana zafalitsidwa pa wailesi ya kanema ya boma ndi pa wailesi. Zakhala vuto lalikulu kwa apolisi ponse paŵiri m’mizinda yaing’ono ndi yaikulu ku America, Canada, ndi Ulaya.

Kulambira Satana kuli ndi chikoka champhamvu kwa achichepere a lerolino. Woyambitsa chipembedzo cha Church of Satan akufotokoza chifukwa chake, monga momwe anasimbidwira m’magazini a ’Teen a June 1993 kuti: “M’malo mwa kulamulira ziŵalo za chipembedzo kupondereza zilakolako zawo zachibadwa, timaphunzitsa kuti ayenera kuzitsatira. Zimenezi zimaphatikizapo chilakolako chonyansa cha thupi, chikhumbo cha kulipsira, kukondetsa zinthu zakuthupi.”

Satana ayenera kukhala wokondwera chotani nanga ndi chiphunzitso chouziridwa mwauchiŵanda chimenechi, popeza kuti chimawombana ndi malamulo a mkhalidwe Achikristu ouziridwa ndi Mulungu!

Kulambira Satana kukukwera. Kuli chiwopsezo chomakula, koma kugwa kwake kwayandikira. Mulungu wake ali pansi pa chiweruzo cha imfa. Zilinso motero ponena za dziko la Satana ndi olichirikiza, popeza kuti “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19; Aroma 6:16) Kwa alambiri a Satana ndi kwa ena onse amene modziŵa kapena mosadziŵa amatumikira zifuno za Satana, uthenga wa Yehova uli wakuti: “Mulungu wa mtendere adzaphwanya Satana pansi pa mapazi anu tsopano lino.”—Aroma 16:20.

Kodi pamenepo “Mulungu wa mtendere” adzabweretsa mtsogolo motani kwa anthu omwe akhala akuvutika? Nkhani zitatu zotsatira zidzasonyeza kukwera ndi kugwa kwa kulambira Satana ndi mikhalidwe padziko lapansi imene idzakuloŵa m’malo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena