Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 10/8 tsamba 4-6
  • Achichepere a Lerolino—Kodi Ali Mikhole Yosavuta ya Kulambira Satana?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Achichepere a Lerolino—Kodi Ali Mikhole Yosavuta ya Kulambira Satana?
  • Galamukani!—1994
  • Nkhani Yofanana
  • Kukwera ndi Kugwa kwa Kulambira Satana
    Galamukani!—1994
  • Kulambira Satana mu Nthaŵi Yathu
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Chidziŵitso pa Nyuzi
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Kodi Pali Vuto Ngati Nditachitako Chidwi Pang’ono Ndi Zamatsenga?
    Galamukani!—2002
Onani Zambiri
Galamukani!—1994
g94 10/8 tsamba 4-6

Achichepere a Lerolino—Kodi Ali Mikhole Yosavuta ya Kulambira Satana?

“KULAMBIRA Satana kukufalikira pakati pa achichepere,” inasimba motero nyuzipepala ya Chifinishi ya pa February 27, 1993. Malinga ndi zopezedwa ndi polisi ya ku Tampere, Finland, apandu ochita malonda a anamgoneka akuloŵetsa achichepere, ndipo makamaka atsikana, m’kulambira kwausatana. M’zochitika zambiri mikhole imeneyi ndi oloŵetsedwamo chatsopano ali ana a misinkhu kuyambira pa zaka 10 kufika 15. “Kulambira Satana kwapeza nthaka yachonde pakati pa achichepere a lerolino,” linasimba motero pepalalo.

“Kudza chatsopano kwa kulambira Satana sikuli chabe mkhalidwe wamomwemo (wa Afinishi),” linachenjeza motero pepalalo. “Mwachitsanzo, magazini a ku South Africa otchedwa Star ya ku Johannesburg posachedwapa anachenjeza kuti kulambira Satana kukukopa azungu achichepere olemera a m’dzikolo.” Kunena zoona, kulambira kwausatana kuli chothetsa nzeru cha padziko lonse kwa makolo limodzinso ndi ana.

Kwenikweni, kulambira Satana mwachinyengo kumalonjeza kuti mudzapeza zochuluka mwa kuchita zochepa chabe. “Lambira mdyerekezi; chita ntchito zake zonyansa, ndiyeno iyenso, adzakupatsa zimene ufuna. Ndipo ndicho chifukwa chake ana ena amaona kulambira Satana kukhala kokhumbirika kwambiri,” anafotokoza motero magazini a ’Teen.

“Ndimakhulupirira kukhala ndi moyo mwa kukhutiritsidwa nawo kotheratu,” anatero wachichepere yemwe akuvomereza kukhala chiŵalo cha gulu lausatana. “Ndimaona mphamvu ziŵiri m’chilengedwe: yabwino ndi yoipa. Zinthu zonse zimene anthu amanena kuti nzoipa nzimene zimakukhalitsa wachimwemwe. Machimo amachititsa kukhutiritsidwa kwa mtima, thupi ndi maganizo,” iye anatero.

Pamene mtekitivi wa ku Denver, Colorado, U.S.A., katswiri pa za magulu ausatana, anafunsidwa chifukwa chake iye analingalira kuti achichepere amaoneka kukhala pachiswe kwambiri kulinga ku kulambira Satana, iye anayankha kuti: “Sindidzaiŵala konse zimene wachichepere wina wolambira Satana anandiuza. Iye anati, ‘Kodi pali chiyani chokhalira ndi moyo? Tidzakhalira moyo lero ndi kuchita zimene tifuna. Palibe mtsogolo.’ ”

Dr. Khalil Ahmad, mtsogoleri wa mautumiki othandiza achinyamata pa Nova Scotia Hospital, mu Dartmouth, Canada, anapereka lingaliro lake ponena za chikoka cha kulambira Satana. “Achichepere amafuna zokondweretsa. Amalingaliro ofooka, kaŵirikaŵiri aja olephera, amakopeka ndi [kulambira Satana]. Iko kumawapatsa lingaliro lolakwa la kudzimva kukhala ndi mphamvu.”

Wapolisi wina wotchuka pa za kulambira Satana, mtekitivi wa ku San Francisco, akutchula vutolo kuti: “Dziko lathu ndilo malo amphwayi. Timaganiza kwambiri za ife eni osati za wina ndi mnzake. Tikukhala m’chitaganya cha malingaliro oipa ndi chachiwawa. Ana amaona zimenezo kukhala khalidwe labwino la moyo ndipo m’kupita kwa nthaŵi amaloŵa m’kulambira Satana.”

Kodi achichepere a lerolino ali oloŵetsedwa m’kulambira Satana pamlingo wotani? “Ana akudzipha okha ndi kupha anzawo. Tili ndi vuto,” anachenjeza motero Larry Jones, mkulu wa gulu la Cult Crime Impact Network amenenso ndi mkulu wa polisi ya ku Boise, Idaho, U.S.A. Wapolisi wina, wa ku boma la Illinois, yemwe amapenda mosamalitsa machitidwe a kulambira Satana m’ntchito yake monga mlangizi wapolisi wa sukulu za sekondale, ananena kuti 90 peresenti ya achichepere omwe amachita za kulambira mdyerekezi amadziloŵetsamo monga choseŵeretsa chosangulutsa, koma 10 peresenti “amakoledwa namamwerekera pamlingo wokulirakulira.”

Nyuzipepala ya sukulu ku Brooklyn, New York, yotchedwa School News Nationwide, ya January-February-March 1994, m’chigawo chake chakuti “Chipembedzo” inali ndi mutu wankhani wakuti “Chifukwa Chake Kulambira Satana Kumakopa Achichepere.” Iyo inasimba kuti: “Anyamata aŵiri atamenyana m’chipinda chodyera cha sukulu ya sekondale, wolakikayo analumpha m’mwamba ndi kuchita sawatcha yachilendo ndi dzanja, mwa kuumba nkhonya atatambasula chala chake chamkombaphala ndi chakaninse. Mphunzitsi wa luso la zojambula analephera kudziŵa chifukwa chake ana ambiri anajambula zithunzi za amuna ooneka mwauchiŵanda okhala ndi mitu ya mbuzi. Ndipo mabuku a zamalaulo anapitirizabe kumasoŵa m’laibulale ya sukulu.

“Kwenikweni, anawo ankaseŵera ndi mphamvu, matsenga, chinsinsi cha kulambira Satana. Kwa ambiri, zinali zoseŵeretsa ndi zosangalatsa. Kwa ena, zinali zowopsa​—⁠zowopsa ndi zakupha kwa Lloyd Gamble wa zaka 17​—⁠yemwe anataya moyo wake monga nsembe ya usatana.

“Pambuyo pa imfa ya Lloyd ndi kumangidwa kwa mng’ono wake wa zaka 15 chifukwa cha mbanda, achikulire a ku dera la Monroe anadziŵa kuzindikira zizindikiro zomwe poyamba zinali zachinsinsi kwambiri: ‘chizindikiro cha mdyerekezi’ cha dzanja, zithunzi za mutu wa mbuzi ndi mabuku omwe anapatsa achichepere zoyerekezera m’maganizo, madzoma ndi kuchisa.”

Malipoti akuoneka kukhala osatha onena za achinyamata aang’ono ndi okulirapo omwe amapha makolo awo ndi ziŵalo zina za mabanja awo chifukwa cha kulambira Satana. Ana aphedwa ndi ana ena m’machitidwe oterowo. Mofanana ndi achikulire ochita zausatana, ana adula ziŵalo za zinyama ndi kuzipha. Ziŵeto zapanyumba zaperekedwa nsembe pa guwa la madzoma ausatana. Malo sakulola kulemba ngakhale theka lokha la kupha kochitidwa ndi ana odziloŵetsa m’chipembedzo cha kulambira Mdyerekezi.

Kodi zitsanzo za ana zimenezi zangokhala kuseŵera chabe ndi kulambira Satana? Kodi awo ozama kwambiri m’kulambira Mdyerekezi ali oŵerengeka chabe ndi osapezekapezeka? Iyayi, ndilo yankho la awo omwe afufuza ochita za malaulo ameneŵa. David Toma, mtekitivi wachiŵiri wakale yemwe anadzakhala wokamba nkhani zosonkhezera, ananena kuti m’sukulu iliyonse kumene iye akamba nkhani, amafunsa funso limodzimodzi lakuti, “Kodi ndi angati pakati pa ana inu amene adziŵa munthu wina kapena kumva za munthu wodziloŵetsa m’machitachita a Usatana?” Iye anati pafupifupi “mbali imodzi yathunthu mwa zitatu ya ophunzirawo ananyamula manja awo.”

Malinga ndi kunena kwa Shane Westhoelter, prezidenti wa National Information Network, kuyambira pa 30 kufika pa 40 peresenti ya ophunzira a sukulu za sekondale amadziloŵetsa m’mitundu ina ya malaulo. Ndiponso, Westhoelter akugomeka kuti kufikira 70 peresenti ya maupandu onse ochitidwa ndi achichepere apansi pa usinkhu wa zaka 17 amasonkhezeredwa ndi kudziloŵetsa m’zamalaulo.

[Mawu Otsindika patsamba 5]

Kulambira Satana kwapeza nthaka yachonde pakati pa achichepere a lerolino

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena