Chidziŵitso pa Nyuzi
Chisonkhezero Chausatana
Pambuyo pa kufufuza chisonkhezero cha kulambira Satana m’nyimbo za roko ndi mu roko yachisonkhezero champhamvu, Tom Harpur mkonzi wa nyuzipepala ya Toronto akulemba mu The Sunday Star kuti: “Ndiyenera kupereka chenjezo lamphamvu koposa lothekera ponena za zimene zikuchitika. . . . Sindinawonepo konse chinthu chochititsa manyazi motero. Nyimbozo nzoyambukiridwa ndi kupenga, kugwidwa ziŵanda, ziŵanda, mwazi, kutukwana, chiwawa cha mtundu uliwonse, kuphatikizapo kugwirira chigololo, kudzichekacheka, mbanda, ndi kudzipha. Imfa ndi chiwonongeko, maulosi a kuwononga, kukanidwa kwa zabwino zonse ndipo kuvomerezedwa kwa zonyansa zonse ndi zoipa—imeneyi ndiyo mitu yake.”
Koyendera limodzi ndi kuchuluka kwa nyimbo zausatana ndiko kuwonjezereka kwa mipatuko yausatana mu United States ndi Canada. Pochitira ripoti msonkhano waposachedwapa wa apolisi mu Ontario, The Globe and Mail, nyuzipepala ya ku Canada, ikunena kuti mipatuko yausatana “imadziloŵetsa m’nsembe za nyama, machitachita onyansa a kunsitu ndi dzoma la kuchitira nkhanza ana.” Tifitifi James Bradley wa ku Washington, D.C., anagwirizanitsa zochitika mazana ambiri za kuchitiridwa nkhanza kwa ana ndi madzoma aupandu a kulambira Satana. Monga momwe anagwidwira mawu mu The Globe and Mail, tifitifi Bradley akuwonjezera kuti mkati mwa zaka zisanu zapitazo, maripoti a madzoma akuchitiridwa nkhanza kwa ana ochokera kwa “ana mazana ambiri, kwa ogwira ntchito zokhudza makhalidwe a anthu ndi aphunzitsi mazana ambiri.”
Polankhula za “masiku otsiriza” a dongosolo lamakonoli loipa la zinthu, mtumwi Yohane analemba kuti: “Mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu, podziŵa kuti kamtsalira kanthaŵi.” (2 Timoteo 3:1; Chibvumbulutso 12:12) Chisonkhezero cha Satana, “mkulu wa ulamuliro wa m’lengalenga,” chikukhathamira ngakhale nyimbo zotchuka za dziko lino. (Aefeso 2:2) Ndicho chifukwa chake mtumwi Paulo analangiza Akristu anzake “kuchirimika pokana machenjerero a Mdyerekezi.”—Aefeso 6:11.
“Osalamulirika”
Pamene mkazi wina wa zaka 28 zakubadwa anali kuthamanga kulimbitsa thupi anamenyedwa ndi kugwiriridwa chigololo mu paki yotchedwa Central Park ya Mzinda wa New York, anthu mamiliyoni ambiri anadabwa ndi kuchita mantha. Chifukwa? Kuwukira kwauchinyama ndi kwa nkhanza kunachitidwa ndi gulu la achichepere amene “chikhutiro chawo chonyansa cha kupeza chipambano ndi zotulukapo zake ndi kusadera nkhaŵa kwawo za kuvutika kochititsidwa ziridi zochititsa mantha,” ikusimba motero New York Post. Ena a achichepere ochita upandu wauchinyama umenewo anasimbidwa kukhala aang’ono a zaka 14 zakubadwa. Powopsyedwa ndi kuwukirako, wolemba Post wina anavomereza kuti dziko lakhala “chitaganya chosalamulirika, chodzikondweretsa, chomwerekera ndi anam’goneka, chokhathamira m’zakugonana, cha mabanja osweka, chopenga mwachiwawa” ndiko kuti “chosalamulirika ndiyeno funso nlakuti: chifukwa ninji?”
M’chenicheni, mbadwo wachiwawa chosayerekezeka umenewu ndiwodi umene unanenedweratu ndi mtumwi Paulo pa 2 Timoteo 3:1-5. Pamenepo iye analongosola kuti “masiku otsiriza” akakhala ndi anthu amene ali “adyera, aumbombo, odzitukumula, onyang’wa.” Ndiponso, “iwo adzakhala achipongwe, osamvera makolo awo, osayamika, ndi osapembedza; iwo adzakhala osakoma mtima, opanda chifundo, oneneza, achiwawa, ndi aukali; iwo adzada abwino; adzakhala onyenga, osakhoza kudziletsa, ndi odzitukumula; adzakonda zokondweretsa m’malo mokonda Mulungu.” (Today’s English Version) Kodi dziko lachiwawa limeneli lidzapitirizabe liri “losalamulirika” kunthaŵi yosadziŵika? Ayi! Yesu anati: “Koma poyamba kuchitika izi weramukani, tukulani mitu yanu, chifukwa chiwomboledwe chanu chayandikira.”—Luka 21:28.