Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 10/8 tsamba 6-8
  • Zipangizo za Kulambira Satana Anamgoneka ndi Nyimbo za Heavy-Metal

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zipangizo za Kulambira Satana Anamgoneka ndi Nyimbo za Heavy-Metal
  • Galamukani!—1994
  • Nkhani Yofanana
  • Zosangulutsa Zosavulaza Kapena Paizoni ya Maganizo?
    Galamukani!—1993
  • Chenjerani ndi Nyimbo Zosayenera!
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Kodi Nyimbo Zingandivulazedi?
    Galamukani!—1993
  • Kodi Mumasankha Nyimbo Mwanzeru?
    Galamukani!—2011
Onani Zambiri
Galamukani!—1994
g94 10/8 tsamba 6-8

Zipangizo za Kulambira Satana Anamgoneka ndi Nyimbo za Heavy-Metal

CARL A. RASCHKE, mtsogoleri wa pa University of Denver Institute of Humanities, analemba kuti: “Sikodabwitsa kuti anamgoneka, [nyimbo za] heavy metal, nkhalwe, ndi chiwawa chauchinyama zonsezo zakhala zizindikiro zonyansa za khalidwe lowonongeka la anthu pamene tikufika ku zaka za khumi lachitatu za Nyengo ya Satana.” Iye anatinso: “Munganene kuti heavy metal ndi Usatana kodziveka zili monga momwe nyimbo za uthenga wabwino ziliri ndi Chikristu. Ali anthu oŵerengeka kwambiri amene amatembenukira ku Chikristu mwakungomvetsera nyimbo za uthenga wabwino pa wailesi. Koma heavy metal ili chisonkhezerezo champhamvu kwambiri. Imalungamitsa zinthu zonyansa zimene ana alimo kale.”

Chimenecho ndi chitsutso champhamvu cha zimene achichepere ambiri lerolino amaziona kukhala njira zabwino zothaŵira nkhaŵa za moyo​—⁠nyimbo za heavy metal ndi anamgoneka. Kodi mawu amenewa otsutsa zimenezi ali olungamitsika? Kodi kunganenedwe kuti anamgoneka ndi nyimbo za heavy metal ndi zizindikiro zothekera kukhala za kulambira Satana? Talingalirani ndemanga za awo omwe ayang’anizana maso ndi maso ndi chiwawa cha olambira ausatana ndi awo omwe awafufuza.

“Uthenga wosonkhezera wa nyimbo za heavy metal uli, mosadabwitsa kwenikweni, ‘wachipembedzo’​—⁠m’lingaliro lakuti umalengeza mphamvu yapamwamba yoyang’anira chilengedwe chonse. Komabe, mphamvu imeneyi sindiyo Mulungu,” analemba motero Raschke, m’buku lake lakuti Painted Black. “Uwo . . . umachititsidwa ndi Mdyerekezi mwiniyo.” Ndiponso, iye anati: “Mphamvu ndi chiwawa cha usatana ndi chinthu chimene achichepere opanda chiyembekezo, ndi a chikumbumtima chopotoka, angakopeke nacho mosavuta. . . . Achichepere ovutitsidwa ndi ochitiridwa nkhanza, amachititsidwa ndi zokumana nazo zoipazo, kukhulupirira kuti Mphamvu Yapamwambayo iyenera kukhala yoipa. Heavy metal imachirikiza ‘chiphunzitso chachipembedzo’ chimenechi ndi kuchivomereza m’nyimbozo.”

Malinga ndi kunena kwa Dr. Paul King wa pa University of Tennessee, yemwe anapereka umboni pamaso pamsonkhano wa United States Senate ponena za nyimbo za heavy metal, nyimbo zokondedwa ndi achichepere ambiri osokonezeka maganizo ndizo za “mitu yankhani yachilendo ya chiwawa, chidani, chipanduko, kugonana kwauchinyama, kuchitira nkhanza akazi, ndi kulemekeza Satana. Pamene khalidwe la wachinyamata liphatikizapo anamgoneka, nyimbo zimenezo zimakondeka koposerapo.” Nyimbo za heavy metal zimalemekeza ndi kutamanda mphamvu ya zoipa, anatero King. Mu nyimbo za heavy metal, “machitidwe oipa amathokozedwa mokulirakulira m’makonsati,” iye anatero.

Talingalirani zipatso za uthenga wosazindikirika kwenikweni wa nyimbo za heavy metal m’malipoti otsatiraŵa.

Chaka chatha mu New Jersey, U.S.A., anyamata aŵiri a zaka 15 anapha mwankhalwe galu wapanyumba wa mtundu wa Labrador wotchedwa Princess. “Inali nsembe kwa Satana,” iwo anatero. Iwo ananyamula galuyo ku unyolo wake, kumamponda chidyali kufikira atafa, anadula lilime lake ndi kuligwiritsira ntchito m’dzoma la usatana. Iwo anapachika thupi la galuyo lodulidwa ziŵalo pa mbedza yachitsulo yaikulu ndi kumkoloŵeka pabwalo la panyumba yoyandikana. Zizindikiro zausatana zinapezedwa pamutu wa galuyo, ndipo chizindikiro cha nyenyezi (yokhala ndi nsonga zisanu mkati mwa mzera wozikweteza​—⁠chizindikiro cha Usatana) chinalembedwa pansi mmunsi mwa thupi la galuyo. Pausiku wa kupha kumeneko, iwo ankamvetsera Deicide (imene imatanthauza kupha Mulungu), gulu loimba nyimbo za death metal, limene woimba wawo wotsogolera amadzitama za kuzunza ndi kupha zinyama.

Mu California, okondana aŵiri achichepere, omwe, malinga ndi kunena kwa mabwenzi awo, anamwerekera ndi kulambira Satana, anapha mwauchinyama amayi a mtsikanayo mwa kuwabaya ndi mwa kuwamenya ndi sipanela. M’dera limodzimodzilo, wachichepere wina anapemphera kwa Satana ndiyeno nkupha atate wake mwa kuwawombera mfuti. Apolisi ofufuza chiwawacho anakhutiritsidwa kuti nyimbo za heavy metal ndizo zinali chochititsa. “Kwenikweni, nyimbozo zimaphunzitsa kuti sufunikira kumvetsera makolo ako, ndi kuti uyenera kukhala ndi moyo mmene ufunira,” anatero mkulu wina wapolisi.

Mu England mikhole ya magulu ogwirira chigololo inauza apolisi kuti mmodzi wa ogwirira chigololowo anali ndi mphini za chizindikiro cha gulu la oimba nyimbo za heavy metal zimene mawu ake amanena za kugwirira chigololo ndi chiwawa.

Mu Arkansas, U.S.A., wachichepere wina wa kumudzi anayesa kupha makolo ake mwa kuwamenya ndi chibonga ndi kuwaduladula ndi chipula. Apolisi anapeza kuti m’wailesi yake munali kaseti yoikidwa kuti iyambe yokha kuimba nyimbo yotchedwa, “Altar of Sacrifice” ya gulu loimba heavy metal, mmene muli mawu ofuula akuti: “Mkulu wansembe akuyembekeza, chipula chili m’dzanja, kukhetsa mwazi woyera wa namwali. Kuphera Satana, imfa yadzoma, labadira lamulo lake lililonse. Loŵa m’dziko la Satana . . . Phunzira mawu opatulika a chitamando akuti, ‘Tamandani Satana.’ ”

Ponena za mawu a nyimbo zina zoimbidwa mokuwa ndi ziŵalo za magulu a heavy metal​—⁠mawu amene kaŵirikaŵiri amatsatiridwa ndi milomo ndi owachemerera ndi mzimu wa kutengeka maganizo pamakonsati, kapena pozimvetsera pa makaseti kwa maola ambiri​—⁠kodi mawu oterowo amakhala ndi chisonkhezero chotani kwa achichepere a maganizo anthete? Mwachitsanzo, talingalirani mawu aŵa: “Satana mbuye wathu m’zoipa zathu amatitsogolera pa sitepe loyambirira lililonse,” ndi “Tsanulira mwazi wako, lola kuti utayikire pa ine. Tenga dzanja langa ndipo taya moyo wako . . . Watsanulira mwazi. Ndalandira moyo wako.”

“Ngati tili ovomereza kale lingaliro lakuti zaumaliseche zingasonkhezere munthu wogona ana,” analemba motero Carl Raschke, “bwanji osavomereza lingaliro lakuti mawu amene amafuula kuti muphe, mdule chiŵalo, mlemaze, mzunze, mfafanize angathe kusonkhezera munthu waubongo wosaima bwino kuchitadi zinthu zimenezo?”

Lingaliro la ofufuza kulikonse nlakuti kugwiritsira ntchito molakwa anamgoneka ndi kulambira Satana zimayendera pamodzi. Wachiŵiri kwa mtekitivi wakale David Toma akudandaula kuti iye “sanaonepo wolambira Satana wosagwiritsira ntchito anamgoneka.” Kugwiritsira ntchito anamgoneka, anasimba motero magazini a ’Teen, kumacholoŵanitsa moyo wa achichepere “odziloŵetsa m’kulambira mdyerekezi, akumakuchititsa kukhala kovutirapo nthaŵi zonse kusiyanitsa chimene chili chenicheni ndi chimene chimangoonekera kukhala chenicheni kwa munthu womwerekera ndi anamgoneka ndi zakumwa zoledzeretsa.”

Nyimbo za “heavy metal nzogwirizana kwambri ndi kumwerekera ndi anamgoneka monga momwe malotale aliri ogwirizana kwambiri ndi otchova juga omwerekera,” anatero Raschke. “Wachichepere womwerekera ndi anamgoneka amakhala ndi khalidwe la mwano, nkhanza, umbala ndi chilakolako chonyansa chakugonana​—⁠zonsezo zochirikizidwa ndi mawu akulira ndi akubuula a magulu a metal.”

Mosakayikira, wachichepere amakhala mkhole wosavuta ku chisonkhezero cha Satana pamene maganizo abwino achotsedwa mu ubongo wake ndi kuloŵetsamo malingaliro a zoipa ndi chiwawa.

[Mawu Otsindika patsamba 8]

Munthu amakhala mkhole wosavuta ku chisonkhezero cha Satana pamene maganizo abwino achotsedwa mu ubongo ndi kuloŵetsamo oipa ndi achiwawa

[Chithunzi patsamba 7]

Kodi nchiyani chimene mukuloŵetsa m’maganizo anu?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena