Chidziŵitso pa Nyuzi
Nyumba Yogawanika
Yesu ananena kuti “nyumba ikagawanika pa iyo yokha,” iyo singathe kuima. (Marko 3:25) Umu ndi mmene United Church of Canada, tchalitchi cha Chiprotestanti chachikulu koposa mu mutunduwo, chikudzipeza icho cheni pa nkhani ya kugonana kofanana ziwalo ndi kuikidwa kwa amuna ndi akazi ogonana ofanana ziwalo.
Chigamulo chotengedwa ndi Msonkhano Wachisawawa wa 32 wa United Church of Canada chimavomereza ochita kugonana kwa ofanana ziwalo kugwira ntchito monga atsogoleri a chipembedzo. Mogwirizana ndi nyuzipepala ya ku Canada, The Globe and Mail, chigamulocho chimanena kuti mosasamala kanthu za zikhoterero zawo za kugonana, aiyense “yemwe amadzinenera kukhala nid chikhulupiriro mwa Yesu Kristu ndi chimvero kwa Iye ali wolandiridwa kulowa kapena kukhala ziwalo zokhazikika za Tchalitchi,” ndipo “ziwalo zonse za Tchalitchi ziri zoyenerera kulingaliridwa kaamba ka utumiki wolamulidwa.” Ripoti la masamba 125 la United Church linanena kuti: “Pali unyinji wa zikhoterero za kugonana: kugonana kwa ofanana ziwalo, kugonana kwa okhala ndi ziwalo zogonanira zonse ziŵiri, kugonana kwa osiyana ziwalo. Izi zifunikira kuwonedwa monga zachibadwa ndipo monga mphatso yochokera kwa Mulungu.”
Ikumachitira ndemanga pa chosankha cha tchalitchicho kulandira ogonana ofanana ziwalo monga atsogoleri a chipembedzo, Globe ikulongosola kuti “nkhani yaikulu inali kupulumuka kwa tchalitchicho.” Chiyambire 1972, maripoti avumbula kuti, tchalitchicho chakhala chikumataya ziwalo mokhazikika ndipo chiri m’mavuto a za chuma. Chifukwa chake? Mtsogoleri wa chipembedzo Johan Tweedie akusonyeza “kutuluka kopita patsogolo kuchoka m’tchalitchicho pamene anthu akuchiwona icho chikutengeka kuchoka ku maziko ake a Chikristu.” “Chotero,” ikusimba tero The Post ya ku Canada, “kuvomereza kwawo kwa zinthu zoterozo zonga kugonana kwa ofanana ziwalo, kugonana kunja kwa chomangira cha ukwati, kuchotsa mimba kolamulidwa ndi kuthetsa maukwati kuli zosangalatsa kwa mbadwo wachichepere.”
Ngakhale kuli tero, kodi chimvero kwa Kristu chimalola kaamba ka kupotoza maprinsipulo a Baibulo? Mosiyanako, Mawu a Mulungu ali achimvekere: “Musadziputsitse inu eni; anthu omwe ali a makhalidwe achisembwere . . . olakalaka ogonana ofanana ziwalo . . . palibe aliwonse a awa adzalowa Ufumu wa Mulungu.”—1 Akorinto 6:9, 10, Today’s English Version.
Kugwiritsira Ntchito Nthyole
“Musagwiritsire Nthyole, koma Dziŵani Zotulukapo Zake” unali mutu wa nkhani yowonekera mu The Natal Mercury, nyuzipepala ya ku South Africa, ikumachitira chisoni chikhoterero chamakono cha kusapereka chilango cha kuthupi pa ana kunyumba ndi mu sukulu. Ndani yemwe ali ndi thayo kaamba ka kusinthidwa kwa mkhalidwe kulinga ku kumenya? Profesa Smythe, katswiri wodiŵa za matenda a ana pa Yuniversite ya Natal, South Africa, akuika liwongolo kotheratu pa akatswiri odziŵa za malingaliro a ana. “Kaŵirikaŵiri pamene ndifufuza pa mizu ya nkhani ya malingaliro,” akulongosola tero smythe, “wina amapeza kusintha m’mikhalidwe kuyambira ndi nthanthi ya malingaliro. Choyamba yotsutsa mwachiwawa ku mtundu wina uliwonse wa chilango cha kuthupi, kenaka kuzizwitsidwa ndi zotulukapo za kupanda chilango kotulukapo kuchokera ku nthanthi ya yopanda zokwiyitsa ndi yopanda zotsekereza.”
Smythe akubukitsa kulinganizika. “Kunkitsa kwa kulekerera kuli koipa mofanana ndi kunkitsa kwa kulanga,” iye akudziŵitsa tero, “koma chenicheni chakuti kuwongolera kuli kopepuka kwa mwana wolangidwa mopambanitsa kuposa mwana wosalangidwa ziyanjo zimakhoterera ku mbali ya kulanga pamene mukaikira.” Profesayo akugogomezera kuti cholinga choperekera chilanga cha kuthupi chiyenera kukhala kudera nkhaŵa kwa chikondi kaamba ka ubwino wa pa nthaŵi ino ndi wa mtsogolo wa mwanayo.
Uphungu woterowo suli watsopano koma kubwerera ku chitsogozo chosalakwika cha Baibulo: “Wolekerera mwanake osammenya amuda, koma womkonda amyambize kumlanga.”—Miyambo 13:24; onaninso Miyambo 23:13, 14.
Kutchova Njuga Si Kuchimwa?
Malo a ansembe a Roma Katolika posachedwapa anakhala malo a chipembedzo oyamba mu Wisconsin, U.S.A., kufunsira kaamba ka chilolezo cha kugulitsa matiketi a lottery, ikusimba tero The Sheboygan Press. Pamene kuli kwakuti zogulitsidwazo zalongosoledwa kukhala kuyesayesa kwa “kuwonjezera” zosonkhanitsidwa za mlungu ndi mlungu, Press yadziŵitsa kuti chifukwa chachikulu kumbuyo kwa kulingaliridwa kwa kugulitsa matiketi a lottery “chiri kuwonjezera opezekapo kwa maseŵera ake a bingo.” Tchalitchicho chasimbidwa kale kukhala chikupangitsa maseŵera a bingo ndi phindu lomwe “limachokera pa $800 kufika ku $1,000” usiku uliwonse.
Pamene anafunsidwa ngati kutchova njuga kuli ndithudi kuchimwa, wansembe wa pa malo a nsembewo Robert Fleishman anayankha kuti: “Sindidziŵa.” Pamene anatsimikizira kuti kpititsa patsogolo kwa tchalitchiko kwa bingo kapena kugulitsa kwa matiketi a lottery “kuli mwinamwake kosagwirizana mochepera ndi chiitano chathu chauzimu,” iye anawonjezera kuti “ngati iwo sabwera kuno, adzapita kwinakwake” kukawononga ndalama zawo.
Kodi mtsogoleri wachipembedzo yemwe amadzinenera kukhala mtsatiri wa Kristu ayenera kupititsa patsogolo kutchova njuga? Kutalitali! Kutchova njuga mu mtundu uliwonse kumasangalatsa umodzi wa mikhalidwe yoipa koposa mwa anthu—umbombo. Anthu omwe amapititsa patsogolo iko amalimbikitsa anthu kukhulupirira kuti chiri cholondola kupeza phindu kuchokera ku kutaikiridwa kwa ena. Komabe, Mawu owuziriddwa a Mulungu amanena mwachindunji kuti anthu a umbombo sadzalowa Ufumu wa Mulungu.—1 Akorinto 6:9, 10; Aefeso 4:19; 5:3.