Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g91 5/8 tsamba 4-6
  • Malotale Kodi Nchifukwa Ninji Ali Otchuka?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Malotale Kodi Nchifukwa Ninji Ali Otchuka?
  • Galamukani!—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Chatsopano Nchiyani Ponena za Malotale?
  • Chosangalatsa kwa Ochilikiza
  • Maloto a Chuma
  • Malotale—Kodi Ndani Amapambana? Kodi Ndani Amalephera?
    Galamukani!—1991
  • Mliri wa Lotale—Njuga ya Padziko Lonse
    Galamukani!—1991
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Chidziŵitso pa Nyuzi
    Nsanja ya Olonda​—1990
Onani Zambiri
Galamukani!—1991
g91 5/8 tsamba 4-6

Malotale Kodi Nchifukwa Ninji Ali Otchuka?

KODI nchifukwa ninji anthu amaseŵera lotale? “Ngwosangulutsa, nkuseŵera,” anatero wolankhulira wamkazi wa bungwe la lotale. Mwinamwake nditero, koma chisonkhezero chachikulu ndithudi ndicho ndalama za mphotho. Pafupifupi aliyense angakonde kukhala ndi ndalama zowonjezereka. Ndipo malotale amalonjeza ndalama zambiri. M’dziko lamakono losatsimikizirika la mitengo yokwera nthaŵi zonse, kugwa kwa mphamvu ya ndalama, ndi ntchito zosatsimikizirika, anthu mamiliyoni ambiri amakhulupirira kuti kupambana lotale ndiko njira imodzi yokha yolingalirika yakuti akhalire olemera koposa.

Kuwonjezera ku chisonkhezero chimenechi, malotale ngosavuta ndipo ngokhweka kuŵaseŵera. Pali mbali zambiri zosiyanasiyana, monga ngati Lotto, manambala, ndi maseŵera pamene mumakalaula pepala kuti muvumbule manambala obisika, koma zonsezi ziri ndi mbali ziŵiri. Yoyamba njakuti oseŵerawo amapambana pamene manambala amene ali pa tikiti yawo afanana ndi aja osankhidwa ndi olinganizawo. Chachiŵiri, mosiyana ndi mitundu ina ya kutchova njuga, palibe luso lapadera kapena chidziŵitso chimene chiri chofunikira kuti mupambane. Kupambana kapena kulephera kumangodalira pa mwaŵi.

Anthu amaseŵeranso malotale chifukwa chakuti kugula tikiti nkokhweka. Anthu ambiri a ku Amereka angawagule pagolosale yakwawoko. Kwina kulikonse, ngati malo ochitira lotale sali pafupi, oseŵerawo akhoza kubetcha mwakulemba makalata, kutumiza telefoni, telex, kapena fax.

Kodi Chatsopano Nchiyani Ponena za Malotale?

Kodi malotale ngatsopano? Kutalitali. Pamapwando m’Roma wamakedzana, olamulira Nero ndi Augustus anapereka akapolo ndi katundu monga mphotho. Imodzi ya mphotho zandalama zoyambirira zolembedwa mwinamwake inaperekedwa monga lotale mu 1530 mu Florence, Italiya. M’zaka mazana omwe anatsatirapo, malotale anapita patsogolo m’Yuropu. Malotale anakhala achipambano ku Amereka yakalenso, akumabweretsa ndalama zomwe zinathandiza kulipirira Jamestown, gulu la asirikali lotchedwa Continental Army, ndiponso kumanga nyumba zamayunivesite otchuka, monga ngati Harvard, Dartmouth, Yale, ndi Columbia.

Komabe, m’zaka za zana la 19, bizinesiyo inaloŵa m’vuto. Otsutsa anasuliza kutchova njuga ndipo anapereka zinenezo zakuti kuchita maere kunali kokondera. Malotale anadzazidwa ndi kupereka chiphuphu, kudyola, ndi kudziloŵetsa m’zaupandu. Ochilikiza amseri anapeza mapindu aakulu. Monga chotulukapo, malotale analetsedwa mu United States, Falansa, ndi Briteni.

Kodi zathera pompo? Ndithudi ayi. Malotale anapitirizabe kunka patsogolo kwinakwake—mwachitsanzo, Italiya ndi Australia. Carlos III wa ku Spanya anayambitsa lotale mu 1763; mpangidwe wake wamakono unakhazikitsidwa mwalamulo mu 1812. Dziko limodzi pambuyo pa linzake linayamba kutsatira chikhoterero cha lotale. Mu 1933, Falansa anachotsa chiletso chake nakhazikitsa Loterie nationale. Ndiponso m’ma 1930, Ireland anakhazikitsa Irish Hospitals Sweepstake yake yotchuka. Takarakuji ya ku Japan inayambako mu 1945. Briteni inavomereza kubetcha m’maseŵera a mpira ndi kugulitsa manambala a mwaŵi, kwenikwenidi malotale. Ndipo mu 1964 United States inabwerera m’bizinesiyo.

Kenaka m’ma 1970, zochitika ziŵiri zinasintha kachitidwe ka lotale. Choyamba chinali kuyambitsidwa kwa makompyuta olunzanitsidwa kumalo ogulitsira zinthu. Tsopano kunali kotheka kuyambitsa maseŵera omveka patali, amawu okweza, mmene oseŵera akanadzisankhira manambala awo. Sipanafunikirenso kudikirira kwa milungu kapena miyezi kuti awone ngati anapambana; oseŵerawo akakhoza kudziŵa m’masiku ochepa, maola, kapena ngakhale mphindi.

Chochitika chachiŵiri chinali kuyambitsidwa kwa Lotto, maseŵera omwe mwaŵi wakupambana ngochepa zedi. M’maseŵera a Lotto, ngati jackpot sinapambanidwe, iyo imapitirizidwa m’maseŵera otsatirapo. Monga chotulukapo chake, ndalama za mphotho zingafikire madola mamiliyoni ambiri. M’maseŵera a Lotto, zinthu zogulitsidwa zinachuluka, ndipo bizinesiyo inakhala yaikuludi.

Chosangalatsa kwa Ochilikiza

Kodi nchifukwa ninji maboma amachilikiza kutchova njuga? Chifukwa chakuti ndinjira yopepuka yopezera ndalama popanda kukweza misonkho. Pamene kuli kwakuti makina otchovera njuga ndi maseŵera a roulette amabweza ndalama zamphotho zochuluka kufika ku 95 peresenti ya zimene amatenga, malotale amalipira yochepera pa 50 peresenti. Mwachitsanzo, mu United States mu 1988, pafupifupi masensi 48 a dola imodzi iriyonse ya lotale anabwezeredwa monga mphotho ndipo masensi 15 ananka kwa ochilikiza, ogulitsa, ndi oyang’anira. Masensi 37 otsalawo anagwiritsiridwa ntchito kulipirira zowongolera zaunyinji, maphunziro, malo a zaumoyo, ndi kuthandiza okalamba. M’dziko lonselo, chiŵerengerocho chinafika pa madola zikwi 7.2 miliyoni.

Koma maboma samalinganiza malotale kuti adzipanga ndalama zokha. Ngati iwo sangaloŵe m’bizinesiyo, angamataye ndalama. Nzika zawo zingakaseŵere kwinakwake. Chotero pamene dziko kapena boma limodzi liyamba lotale, dziko kapena boma loyandikana nalo limakhala pansi pa chididikizo chakuchita chinthu chofananacho. Chiyambukiro chofalikira chimenechi nchowonekera mu United States. Mu 1964 kunali lotale ya Boma imodzi yokha; mu 1989 analimo 30.

Maloto a Chuma

Ndithudi, pali anthu ambiri amene akuyesayesa kusunga ndalama zimene amapeza. Chotero kodi ochilikiza amawakhutiritsa motani anthu kuti awonongere ndalama zawo pa malotale? Mwakulengeza! Kuitana akatswiri odziŵa kukakamiza!

Kodi kulengeza kumagogomezera kuti mbali ina (kaya ichepe bwanji) ya ndalama zopezedwazo idzathandiza kulipirira maphunziro kapena kupereka chisamaliro kwa okalamba? Kutalitali! Zimenezo sizimatchulidwa kaŵirikaŵiri. M’malomwake, kulengezako kumagogomezera mmene kudzakhalira kosangalatsa kupambana madola mamiliyoni ambiri. Nazi zitsanzo zoŵerengeka:

◻ “Njira Yamoyo Yosangalatsa ya Anthu Olemera ndi Otchuka Ingakhale Yanu Tsopano Lino . . . Mutaseŵera LOTTO 6/49 Yotchuka ya Madola Mamiliyoni Ambiri ya ku Canada.”

◻ “LOTALE YA FLORIDA . . . Lemerani ndi Lotale Yaikulu Koposa ya ku Amereka.”

◻ “Ndalama Zopangidwa m’Jeremani—SANKHANI CHUMA nimukhale Mpondamatiki usiku umodzi wokha.”

Kodi nkunenerera kopambanitsa? Inde ndithudi! Zoyesayesa zakuchepetsako kulengezako zimatha kaŵirikaŵiri pamene matikiti sakugulitsidwa. Kwenikweni, ochilikiza amatembenukira ku maseŵera ena amphamvu ndi malonda kotero kuti akope oseŵera atsopano ndikupangitsa akale kukhalabe okondweretsedwa. Nthaŵi zonse ochilikiza amapereka chinachake chimene chimawoneka kukhala chatsopano. Wotsogoza lotale wa ku Oregon wotchedwa James Davey ananena kuti: “Tiri ndi mitu ina yotchovera njuga, timachita maseŵera a Olympic. Pa Krisimasi timachita maseŵera otchedwa Holiday Cash. Ndi Nyenyezi Zamwaŵi timagwiritsira ntchito zizindikiro zanyenyezi za anthu. Timapeza kuti titachitira pamodzi maseŵera aŵiri kapena atatu, anayi kapena asanu, timagulitsa matikiti ambiri.”

Koma chokopa chachikulu koposa ndicho jackpot yaikulu. M’maseŵera a Lotto, pamene ndalama zamphotho zawonjezeredwa, monga momwe zinachitikira pamene zinafika pa $115 miliyoni mu Pennsylvania mu 1989, zimakhala nkhani ya tsiku ndi tsiku. Anthu amathamangira kukagula matiki m’njira imene mkonzi wina aitcha kukhala “kududukira kwa wotchova njuga.” Mkati mwa kutengeka maganizoko, ngakhale awo amene mwanthaŵi zonse samaseŵera lotale amatenga ndalama zawo.

[Bokosi patsamba 6]

Mliri wa Kutchova Njuga ndi Chipembedzo

“Tchalitchi cha Katolika chandiphunzitsa kutchova njuga. Bingo ndi maraffle sizosiyana konse ndi malotale. Ngati Tchalitchi cha Katolika chingatsogolere ndikuleka kutchova njuga konse, ndingapendenso lingaliro loleka kuseŵera lotale. Ngati ndine waumbombo, nchifukwa chakuti uwo uli pafupifupi dzoma lachipembedzo m’Tchalitchi.”—Woŵerenga analembera magazini a U.S. Catholic.

“Mogwirizana ndi kufufuza kwa nyumba za agulupa Achikatolika kochitidwa ndi Notre Dame University, pamapeto pa Misa ya pa Sande, chochitika china chachiŵiri pamene pamapezeka anthu ambiri m’matchalitchi a Katolika ndi pamaseŵera a mlungu ndi mlungu a bingo.” Komabe, ansembe ambiri amanena kuti anthu ambiri amene amapezekapo pamaseŵera a bingo samapita ku tchalitchi.—The Sunday Star-Ledger, New Jersey, U.S.A.

“Pancras Woyera Mtima Anabweretsa Mwaŵi ku Madrid” umenewo ndiwo unali mutu wa kope lamitundu yonse Lachispanya la mlungu ndi mlungu la ABC. Nkhaniyo inapitiriza kuti: “‘Anali Pancras Woyera Mtima’ anafuula mobwerezabwereza olembedwa ntchito aŵiri pasitolo ya lotale . . . kumene anagulitsa mpambo umodzi wokha wa 21515, ndipo mphotho ya ‘gordo’ [yaikulu] inali ndi mtengo wa 250 miliyoni [pesetas, kapena lerolino, $2,500,000, U.S.], yomwe inagaŵiridwa m’Madrid. [Olembedwa ntchitowo] anavomereza kuti anapemphera kwa woyera mtima, yemwe chifano chake chimayang’anira malo awo pomwe anaikapo chitsamba cha parsley, kuti akhale ndi mwaŵi wakugulitsa ‘gordo’ ya Krisimasi.”

“Poyesayesa kupeza njira zofotokozera mwaŵi wawo, opambana akale anakhulupirira kuti Mulungu ndi choikidwiratu anawasankha iwo kuti apambane ndalama. . . . ‘Tikufuna kukhulupirira kuti mwaŵi ndi tsoka nzogwirizana ndi chinachake, osati ngozi,’ anatero Dr. Jack A. Kapchan, profesa wa maphunziro a maganizo pa Yunivesite ya Miami. ‘Ndipo kodi pali chiyani chinanso choigwirizanitsako kuposa Mulungu?’”—The New York Times.

Kodi Baibulo limanenanji ponena za mwaŵi? Yehova anauza Israyeli wosakhulupirika kuti: “Koma inu amene mwasiya Yehova, amene mwaiŵala phiri langa lopatulika, ndi kukonzera mlungu wamwaŵi gome, ndi kudzazira mlungu wa [Choikidwiratu, NW] zikho za vinyo wosanganiza.”—Yesaya 65:11.

Kodi ndi opambana angati amene amalingalirapo kuti mwaŵi wawo wosankhika ngozikidwa pa tsoka la mamiliyoni ambiri olephera? Kodi kutchova njuga kumasonyeza ‘chikondi cha pa mnansi’ m’njira ina iliyonse? Kodi nkwanzeru kapena Kwamalemba kulingalira kuti Mfumu Ambuye wa chilengedwe chonse angadziloŵetse m’machitachita adyera a kutchova njuga oterowo?—Mateyu 22:39.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena